Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 17-19

Makwangwala Adyetsa Eliya

17 Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”

Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani. Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”

Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko. Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo.

Mayi Wamasiye wa ku Zarefati

Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo. Yehova anayankhula naye kuti, “Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” 10 Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” 11 Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”

12 Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”

13 Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. 14 Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”

15 Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. 16 Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.

17 Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. 18 Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”

19 Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. 20 Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” 21 Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”

22 Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. 23 Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”

24 Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”

Eliya ndi Obadiya

18 Patapita masiku ambiri, mʼchaka chachitatu cha chilala, Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Pita ukadzionetse kwa Ahabu ndipo ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.” Choncho Eliya anapita kukadzionetsa kwa Ahabu.

Tsono nthawi imeneyi njala inakula kwambiri mu Samariya, ndipo Ahabu anayitana Obadiya amene ankayangʼanira nyumba yake yaufumu. (Obadiya ankaopa Yehova kwambiri. Pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 ndi kuwabisa mʼmapanga awiri, phanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi). Ahabu anawuza Obadiya kuti, “Pita mʼdziko kulikonse kumene kuli zitsime za madzi ndi ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu oti nʼkumadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale ndi moyo, kuti tisaphe chiweto chilichonse.” Choncho anagawana dziko loti apiteko, Ahabu anapita mbali ina, Obadiya nʼkupita ina.

Obadiya akuyenda mʼnjira anakumana ndi Eliya. Ndipo taonani, Obadiya anamuzindikira Eliyayo, naweramira pansi ndipo anati, “Kodi ndinu, mbuye wanga Eliya?”

Eliya anayankha kuti, “Inde. Pita kawuze mbuye wako kuti, ‘Eliya wabwera.’ ”

Obadiya anafunsa kuti, “Kodi ndalakwa chiyani kuti inu mupereke mtumiki wanu kwa Ahabu kuti akaphedwe? 10 Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuye wanga sanatumeko anthu okakufunafunani. Ndipo pamene mtundu wa anthu kapena ufumu unena kuti kuno kulibe, Ahabu ankawalumbiritsa kuti atsimikizedi kuti inuyo kulibe kumeneko. 11 Koma tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ 12 Ine sindikudziwa kumene Mzimu wa Yehova udzakupititsani ine ndikachoka. Ngati ndipita kukamuwuza Ahabu ndipo iye wosadzakupezani, adzandipha. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndi kupembedza Yehova kuyambira ubwana wanga. 13 Mbuye wanga, kodi simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ine ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼmapanga awiri, mʼphanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi akumwa. 14 Ndiye inu tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ Iyeyo adzandipha ndithu!”

15 Eliya anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamutumikira, ine lero ndidzaonekera ndithu pamaso pa Ahabu.”

Eliya pa Phiri la Karimeli

16 Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu, namuwuza, ndipo Ahabu anapita kukakumana ndi Eliya. 17 Pamene Ahabu anaona Eliya, anati kwa iye, “Kodi ndiwedi, munthu wovutitsa Israeli uja?”

18 Eliya anayankha kuti, “Ine sindinavutitse Israeli, koma ndinuyo ndi banja lanu. Mwasiya malamulo a Yehova ndipo mwatsatira Abaala. 19 Tsopano sonkhanitsani anthu a mʼdziko lonse la Israeli kuti akumane nane pa Phiri la Karimeli. Ndipo mubwere nawo aneneri a Baala 450 ndi aneneri a fano la Asera 400, amene amadya pa tebulo la Yezebeli.”

20 Choncho Ahabu anatumiza mawu mʼdziko lonse la Israeli, ndipo anasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimeli. 21 Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.”

Koma anthu aja sanayankhe.

22 Pamenepo Eliya ananena kwa iwo kuti, “Ine ndilipo ndekha mneneri wa Yehova, koma Baala ali ndi aneneri 450. 23 Tibweretsereni ngʼombe zazimuna ziwiri. Iwo asankhepo okha ngʼombe imodzi, ndipo ayidule nthulinthuli ndi kuziyika pa nkhuni nthulizo, koma osakolezapo moto. Ndipo ine ndidzadula nthulinthuli ngʼombe inayo ndi kuyika pa nkhuni koma sindikolezapo moto. 24 Kenaka inu muyitane dzina la mulungu wanu, ndipo ine ndidzayitana dzina la Yehova. Mulungu amene ati ayankhe potumiza moto, iyeyo ndiye Mulungu.”

Pamenepo anthu onse anati, “Izi mwanena zamveka bwino.”

25 Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.” 26 Choncho iwo anatenga ngʼombe yayimunayo imene anawapatsa, nayikonza.

Kenaka anayitana dzina la Baala kuyambira mmawa mpaka masana. Iwo anafuwula kuti, “Inu Baala, tiyankheni ife.” Koma panalibe yankho; palibe amene anayankha. Ndipo anavinavina mozungulira guwa lansembe limene anapanga.

27 Nthawi yamasana Eliya anayamba kuwanyogodola ndipo anati, “Fuwulani kwambiri. Ndithudi, iye ndi mulungu! Mwinatu akulingalira kwambiri, kapena watanganidwa, kapena ali paulendo. Mwina wagona ndipo nʼkofunika kuti adzutsidwe.” 28 Choncho iwo anafuwula kwambiri ndi kudzichekacheka ndi malupanga ndi mikondo, potsata miyambo yawo, mpaka kutuluka magazi. 29 Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.

30 Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka. 31 Eliya anatenga miyala 12, mwala uliwonse kuyimira fuko lililonse la Yakobo, amene Yehova anamuwuza kuti, “Dzina lako lidzakhala Israeli.” 32 Ndi miyala imeneyo anamanga guwa mʼdzina la Yehova, ndipo anakumba ngalande yayikulu yolowa malita 15 a madzi kuzungulira guwalo. 33 Anayika nkhuni zija mʼmalo mwake nadula nthulinthuli ngʼombe yayimuna ija ndi kuyika nthulizo pa nkhunipo. Pamenepo Eliya anati, “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi ndipo muwathire pa nyama ya nsembeyo ndi nkhunizo.”

34 Eliya anati, “Thiraninso kachiwiri.” Anthu aja anathiranso madziwo kachiwiri.

Iye analamula kuti, “Thiraninso kachitatu.” Ndipo iwo anathiranso kachitatu. 35 Madziwo anayenderera pansi kuzungulira guwa lansembe, nadzaza ngalande yonse.

36 Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. 37 Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.”

38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.

39 Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”

40 Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.

41 Ndipo Eliya anati kwa Ahabu, “Pitani, kadyeni ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.” 42 Choncho Ahabu anapita kukadya ndi kumwa, koma Eliya anakwera pamwamba pa Phiri la Karimeli, ndipo anawerama mpaka pansi, nayika mutu wake pakati pa mawondo ake.

43 Eliya anawuza mtumiki wake kuti, “Pita kayangʼane ku nyanja.” Ndipo iye anapita nakayangʼana.

Mtumikiyo anati, “Kulibe kanthu.”

Kasanu nʼkawiri Eliya anati, “Pitanso.”

44 Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, “Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja.”

Pamenepo Eliya anati, “Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ ”

45 Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli. 46 Dzanja la Yehova linali pa Eliya ndipo atamangira lamba chovala chake, anathamanga ndi kumupitirira Ahabu mpaka kukhala woyamba kukafika ku Yezireeli.

Eliya Athawira ku Phiri la Horebu

19 Tsono Ahabu anawuza Yezebeli zonse zimene anachita Eliya ndi momwe anaphera aneneri onse ndi lupanga. Choncho Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya kuti akamuwuze kuti, “Milungu indilange, ndipo indilange koopsa, ngati mawa nthawi ngati yomwe ino sindidzakupha iwe monga unaphera aneneriwo.”

Eliya ataona zimenezi, ananyamuka nathawa kupulumutsa moyo wake. Atafika ku Beeriseba ku Yuda, anasiya mtumiki wake kumeneko, ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.” Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.

Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye.” Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.

Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali.” Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu. Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.

Ambuye Aonekera Eliya

Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”

10 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”

11 Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.”

Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. 13 Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.

Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”

14 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”

15 Yehova anati kwa Eliyayo, “Bwerera njira imene unadzera, ndipo upite ku Chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya ku Aramu. 16 Ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi kuti akhale mfumu ya Israeli, ndiponso ukadzoze Elisa mwana wa Safati wa ku Abeli-Mehola kuti akhale mneneri wolowa mʼmalo mwako. 17 Yehu adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaeli, ndipo Elisa adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu. 18 Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”

Kuyitanidwa kwa Elisa

19 Kotero Eliya anachoka kumeneko, nakapeza Elisa mwana wa Safati. Iye ankatipula ndi mapulawo khumi ndi awiri okokedwa ndi ngʼombe ziwiriziwiri zapamagoli, ndipo iye mwini ankayendetsa goli la khumi ndi chiwiri. Eliya anapita kumene anali namuveka chofunda chake. 20 Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, “Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani.”

Eliya anayankha kuti, “Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?”

21 Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.