Chronological
Alonda a pa Zipata
26 Magulu a alonda a pa zipata:
Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.
2 Meselemiya anali ndi ana awa:
woyamba Zekariya,
wachiwiri Yediaeli,
wachitatu Zebadiya,
wachinayi Yatinieli,
3 wachisanu Elamu,
wachisanu ndi chimodzi Yehohanani,
ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.
4 Obedi-Edomu analinso ndi ana awa:
woyamba Semaya,
wachiwiri Yehozabadi,
wachitatu Yowa,
wachinayi Sakara,
wachisanu Netaneli,
5 wachisanu ndi chimodzi Amieli,
wachisanu ndi chiwiri Isakara
ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi.
(Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).
6 Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu. 7 Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu. 8 Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.
9 Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.
10 Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri), 11 wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.
12 Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo. 13 Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.
14 Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye. 15 Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake. 16 Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa.
Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake: 17 Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu. 18 Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.
19 Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.
Asungichuma ndi Akuluakulu Ena
20 Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu.
21 Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli, 22 ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova.
23 Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli:
24 Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma. 25 Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake. 26 Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. 27 Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova. 28 Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.
29 Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli.
30 Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani. 31 Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi. 32 Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.
Magulu a Anthu Ankhondo
27 Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
2 Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. 3 Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.
4 Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
5 Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000. 6 Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.
7 Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
8 Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
9 Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
10 Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
11 Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000
12 Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
13 Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
14 Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
15 Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
Akuluakulu a Mafuko a Israeli
16 Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa:
Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri;
mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;
17 mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli,
mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;
18 mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide;
mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;
19 mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya;
mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;
20 mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya;
mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;
21 mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya;
mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;
22 mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu.
Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.
23 Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga. 24 Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.
Anthu Oyangʼanira Chuma cha Mfumu
25 Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu.
Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.
26 Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.
27 Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa.
Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.
28 Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela.
Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.
29 Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni.
Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.
30 Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira.
Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.
31 Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi.
Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.
32 Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.
33 Ahitofele anali phungu wa mfumu.
Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu. 34 Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara.
Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
Ndondomeko ya Kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu
28 Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.
2 Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.” 3 Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”
4 “Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse. 5 Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.” 6 Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. 7 Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”
8 “Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”
9 “Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya. 10 Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”
11 Kotero Davide anapatsa Solomoni mwana wake mapulani a khonde la Nyumba ya Mulungu, nyumba zake, mosungiramo katundu, zipinda zake zamʼmwamba, zipinda zamʼkati ndi malo a nsembe zopepesera machimo. 12 Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova. 13 Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira. 14 Iye anakonzeratu za kulemera kwa golide wopangira zida zonse zagolide zogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndiponso kulemera kwa siliva wopangira zida zonse zasiliva zogwirira ntchito zosiyanasiyana: 15 kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse; 16 kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoyikapo buledi wopatulika; kulemera kwa siliva wopangira matebulo asiliva; 17 muyeso wa golide woyengeka bwino wopangira mafoloko, mbale ndi zotungira; muyeso wa golide wa beseni lililonse la siliva; 18 ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova.
19 Davide anati, “Zonsezi ndalemba kuchokera kwa Yehova, ndipo Iye wachita kuti ndimvetsetse zonse za mapulaniwa.”
20 Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha. 21 Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.”
Zopereka Zomangira Nyumba ya Mulungu
29 Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu. 2 Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. 3 Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu: 4 Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba, 5 zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?”
6 Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. 7 Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. 8 Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. 9 Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri.
Pemphero la Davide
10 Davide anatamanda Yehova pamaso pa gulu lonse, ponena kuti,
“Mutamandidwe Inu Yehova
Mulungu wa kholo lathu Israeli
kuchokera muyaya mpaka muyaya.
11 Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,
ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.
Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.
Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;
Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.
12 Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu;
Inu ndinu wolamulira zinthu zonse.
Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu,
kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.
13 Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozani
ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
14 “Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. 15 Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. 16 Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. 17 Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu. 18 Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu. 19 Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.”
20 Kenaka mfumu Davide inati kwa gulu lonse, “Tamandani Yehova Mulungu wanu.” Kotero onse anatamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anawerama pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Yehova ndi mfumu.
Solomoni Avomerezedwa Monga Mfumu
21 Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse. 22 Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri.
Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe. 23 Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera. 24 Akuluakulu onse a ankhondo ndi anthu amphamvu, pamodzinso ndi ana onse aamuna a mfumu Davide, analonjeza kumvera mfumu Solomoni.
25 Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli.
Imfa ya Davide
26 Davide mwana wa Yese anali mfumu ya Aisraeli onse. 27 Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu. 28 Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
29 Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi, 30 pamodzi ndi tsatanetsatane wa mbiri ya ulamuliro wake ndi mphamvu zake, ndi zonse zomwe zinamuzungulira iye ndi Israeli ndiponso mafumu a mayiko ena onse.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
mlonda akanangolondera pachabe.
2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa
ndi kusagona msanga madzulo,
kuvutikira chakudya choti mudye,
pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3 Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4 Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
mwa munthu wankhondo.
5 Wodala munthu
amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.