Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 25

Salimo la Davide.

25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
    Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
    kapena kuti adani anga andipambane.
Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
    sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
    ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
    phunzitseni mayendedwe anu;
tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
    pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
    ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
    pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
    ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
    pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
    choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
    ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
    kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,
    khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?
    Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,
    ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;
    amawulula pangano lake kwa iwowo.
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,
    pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.

16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,
    pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;
    masuleni ku zowawa zanga.
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga
    ndipo mufafanize machimo anga onse.
19 Onani mmene adani anga achulukira
    ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
    musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndimathawira kwa Inu.
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
    chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

22 Wombolani Israeli Inu Mulungu,
    ku mavuto ake onse!

Masalimo 29

Salimo la Davide.

29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
    pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
    Mulungu waulemerero abangula,
    Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
    liwu la Yehova ndi laulemerero.
Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
    Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
    Siriyoni ngati mwana wa njati:
Liwu la Yehova limakantha
    ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
    Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
    ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
    Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
    Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Masalimo 33

33 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,
    nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
Mutamandeni Yehova ndi pangwe;
    muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
Muyimbireni nyimbo yatsopano;
    imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;
    Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;
    dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.

Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,
    zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;
    amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
Dziko lonse lapansi liope Yehova;
    anthu onse amulemekeze Iye.
Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;
    Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;
    Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
    zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
    ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
    onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
    amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
    palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
    ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
    ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
    Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
    pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
    chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Masalimo 36

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

36 Uthenga uli mu mtima mwanga
    wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:
Mu mtima mwake
    mulibe kuopa Mulungu.
Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri,
    sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.
Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo;
    iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.
Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa;
    iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo
    ndipo sakana cholakwa chilichonse.

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
    kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
    chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
    Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
    amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
    Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
    mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
    chilungamo chanu kwa olungama mtima.
11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,
    kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
12 Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa,
    aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!

Masalimo 39

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

39 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga
    ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;
ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero
    nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
Koma pamene ndinali chete
    osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino
    mavuto anga anachulukirabe.
Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,
    ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;
    kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

“Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga
    ndi chiwerengero cha masiku anga;
    mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.
Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,
    kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;
    moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.
            Sela
Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:
    Iye amangovutika koma popanda phindu;
    amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?
    Chiyembekezo changa chili mwa Inu.
Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;
    musandisandutse chonyozeka kwa opusa.
Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga
    pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.
10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;
    ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.
11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;
    mumawononga chuma chawo monga njenjete;
    munthu aliyense ali ngati mpweya.
            Sela

12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,
    mverani kulira kwanga kopempha thandizo;
    musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,
popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;
    monga anachitira makolo anga onse.
13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala
    ndisanafe ndi kuyiwalika.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.