Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Chronological

Read the Bible in the chronological order in which its stories and events occurred.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yohane 14-17

Yesu Atonthoza Ophunzira Ake

14 “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.”

Yesu Njira ya kwa Atate

Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”

Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.”

Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ 10 Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. 11 Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. 12 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13 Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. 14 Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Lonjezo la Mzimu Woyera

15 “Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16 Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17 Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18 Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. 19 Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20 Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. 21 Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”

22 Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”

23 Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24 Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

25 “Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27 Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29 Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. 30 Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, 31 koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine.

“Nyamukani; tizipita.”

Mpesa ndi Nthambi

15 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.

“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.

“Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’

Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu

18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’

Ntchito ya Mzimu Woyera

26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”

16 “Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe. Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”

Ntchito ya Mzimu Woyera

“Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. 10 Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. 11 Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.

12 “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. 13 Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. 14 Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. 15 Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”

Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe

16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”

17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”

19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22 Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23 Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

25 “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. 26 Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. 27 Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. 28 Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”

29 Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. 30 Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”

31 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” 32 Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.

33 “Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

Yesu Adzipempherera Yekha

17 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:

“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.

Yesu Apempherera Ophunzira Ake

“Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.

13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.

Yesu Apempherera Okhulupirira Onse

20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21 Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22 Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23 Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.

24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.

25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26 Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.