Bible in 90 Days
15 Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata. 16 Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu. 17 Ndipo ndinadzudzula anthu olemekezeka a dziko la Yuda. Ndinawafunsa kuti, “Nʼchoyipa chanji mukuchitachi, kumayipitsa tsiku la Sabata chotere? 18 Makolo anu anachita zomwezi ndipo Mulungu wathu anadzetsa mavuto pa ife ndi pa mzinda uwu. Kodi inu mukufuna kuwutsanso mkwiyo wa Mulungu pa Israeli pamene mukudetsa tsiku la Sabata?”
19 Nʼchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuyamba kuda, tsiku la Sabata lisanayambe, azitseka zipata zonse za Yerusalemu ndipo asazitsekule mpaka sabata litatha. Ndinayika ena mwa antchito anga oyangʼanira pa zipata kuti katundu aliyense asalowe mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata. 20 Choncho kamodzi kapena kawiri anthu amalonda ndi anthu ogulitsa katundu osiyanasiyana ankagona usiku wonse kunja kwa Yerusalemu. 21 Koma ndinawachenjeza ndi kuwafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Ngati muchitanso zimenezi, ine ndidzakugwirani.” Kuyambira nthawi imeneyo, sanabwerenso pa tsiku la Sabata. 22 Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera.
Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
23 Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu. 24 Theka la ana awo linkayankhula chiyankhulo cha Asidodi kapena chiyankhulo chimodzi cha anthu ena, ndipo sankathanso kuyankhula chiyankhulo cha Ayuda. 25 Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi. 26 Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo. 27 Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?”
28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada mwana Eliyasibu mkulu wa ansembe nʼkuti nthawi imeneyi ali mpongozi wa Sanibalati wa ku Horoni. Choncho ndinamuthamangitsa pamaso panga.
29 Inu Mulungu wanga, mukumbukire mmene iwo anayipitsira unsembe, pangano la unsembe komanso la Alevi.
30 Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake. 31 Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake.
Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.
Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa
1 Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. 2 Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, 3 ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.
4 Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. 5 Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. 6 Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. 7 Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. 8 Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake.
9 Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero.
10 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11 kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12 Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima.
13 Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14 Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo.
15 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?”
16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18 Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.”
19 “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20 Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.”
21 Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. 22 Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera.
Mfumu Ikwatira Estere
2 Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. 2 Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola. 3 Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola. 4 Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo.
5 Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa. 6 Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda. 7 Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.
8 Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja. 9 Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.
10 Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero. 11 Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji.
12 Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa. 13 Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu. 14 Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.
15 Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye. 16 Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.
17 Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. 18 Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu.
Mordekai Awulula Chiwembu
19 Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu. 20 Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera.
21 Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. 22 Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai. 23 Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.
Chiwembu cha Hamani Chopha a Yuda
3 Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse. 2 Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.
3 Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?” 4 Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda.
5 Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri. 6 Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira.
7 Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.
8 Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere. 9 Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.”
10 Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. 11 Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.”
12 Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake. 13 Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo. 14 Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo.
15 Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka.
Mordekai a Pempha Estere kuti Athandize
4 Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima. 2 Ndipo anapita ndi kuyima pa chipata cha mfumu, chifukwa panalibe wina aliyense amaloledwa kulowa pa chipata cha mfumu atavala chiguduli. 3 Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
4 Anamwali otumikira mfumukazi Estere ndi adindo ake ofulidwa atabwera ndi kumuwuza za Mordekai, anavutika kwambiri. Estere anamutumizira zovala kuti avale ndi kuti avule chiguduli chake koma Mordekai sanalole zimenezo. 5 Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi.
6 Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu. 7 Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda. 8 Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake.
9 Hataki anabwerera ndi kumufotokozera Estere zimene Mordekai ananena. 10 Ndipo Estere anamutuma Hataki kuti akanene kwa Mordekai kuti, 11 “Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”
12 Tsono Mordekai anawuzidwa mawu a Estere. 13 Kenaka Mordekai anawawuza kuti akamuyankhe Estere motere: “Usaganize kuti iwe wekha mwa Ayuda onse udzapulumuka chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu. 14 Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?”
15 Pamenepo Estere anatumiza yankho ili kwa Mordekai: 16 “Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.”
17 Choncho Mordekai anapita ndi kuchita monga Estere anamupemphera.
Pempho la Estere kwa Mfumu
5 Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. 2 Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.
3 Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”
4 Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.”
5 Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.”
Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. 6 Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.”
7 Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: 8 Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.”
Mkwiyo wa Hamani Ukulabe pa Mordekai
9 Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, 10 komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake.
Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. 11 Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. 12 Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. 13 Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.”
14 Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.
Mordekai Apatsidwa Ulemu
6 Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. 2 Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.
3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”
Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.”
4 Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera.
5 Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”
“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira.
6 Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”
Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” 7 Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: 8 Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. 9 Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”
10 Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.”
11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!”
12 Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13 Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.
Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14 Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.
Hamani Aphedwa
7 Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. 2 Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”
3 Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. 4 Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”
5 Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”
6 Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”
Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. 7 Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.
8 Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.
Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?”
Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. 9 Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”
Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10 Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.
Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda
8 Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. 2 Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani.
3 Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. 4 Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake.
5 Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. 6 Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?”
7 Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. 8 Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.”
9 Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10 Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu.
11 Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12 Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13 Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.
14 Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa.
15 Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16 Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17 Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.
Chigonjetso cha Ayuda
9 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. 2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. 3 Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. 4 Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.
5 Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. 6 Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. 7 Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.
11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”
14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.
16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.
Kukondwerera Purimu
18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.
19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.
23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.
Ukulu wa Mordekai
10 Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. 2 Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? 3 Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.
Mawu Oyamba
1 Mʼdziko la Uzi munali munthu wina, dzina lake Yobu. Munthu ameneyu anali wosalakwa ndi wolungama mtima, ankaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. 2 Anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu, 3 ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa.
4 Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthanasinthana mʼnyumba zawo, ndipo ankayitana alongo awo atatu aja kudzadya ndi kumwa nawo. 5 Masiku aphwandowo atatha, Yobu ankawayitana kuti adzawayeretse. Mmamawa iye ankapereka nsembe yopsereza kuperekera mwana aliyense, poganiza kuti, “Mwina ana anga achimwa ndi kutukwana Mulungu mʼmitima yawo.” Umu ndi mmene Yobu ankachitira nthawi zonse.
Yobu Ayesedwa Koyamba
6 Ana a Mulungu atabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anafika nawo limodzi. 7 Yehova anati kwa Satanayo, “Kodi iwe ukuchokera kuti?”
Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”
8 Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa.”
9 Satana anayankha kuti, “Kodi Yobu amaopa Mulungu popanda chifukwa?” 10 “Kodi Inu simumamuteteza iyeyo, nyumba yake ndi zonse zimene ali nazo? Mwadalitsa ntchito ya manja ake, kotero kuti nkhosa ndi ngʼombe zake zili ponseponse mʼdzikomo. 11 Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kukantha zonse ali nazo ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.”
12 Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, tsono zonse zimene ali nazo ndaziyika mʼmanja mwako, koma iye yekhayo usamukhudze.”
Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova.
13 Tsiku lina pamene ana aamuna ndi ana aakazi a Yobu ankachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba mwa mkulu wawo, 14 wamthenga anabwera kwa Yobu ndipo anati, “Ngʼombe zanu zotipula ndipo abulu anu amadya chapafupi pomwepo, 15 tsono panabwera Aseba kudzatithira nkhondo ndi kutenga zonse. Apha antchito ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
16 Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Kunagwa mphenzi ndipo yapsereza nkhosa ndi antchito anu onse, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
17 Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Akasidi anadzigawa mʼmagulu atatu ankhondo ndipo anafika pa ngamira zanu ndi kuzitenga. Apha antchito anu onse ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
18 Iyeyo akuyankhulabe, panafikanso wamthenga wina nati, “Ana anu aamuna ndi aakazi amachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba ya mkulu wawo, 19 mwadzidzidzi chinayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nʼkudzawomba nyumba mbali zonse zinayi. Nyumbayo yawagwera ndipo afa, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!”
20 Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, 21 nati,
“Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga,
namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche.
Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga;
litamandike dzina la Yehova.”
22 Mu zonsezi, Yobu sanachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”
Yobu Ayesedwa Kachiwiri
2 Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova. 2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, “Kodi iwe ukuchokera kuti?”
Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.”
3 Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. Ndipo iye akanalibe wangwiro, ngakhale iwe unandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.”
4 Satana anayankha kuti, “Iye ayesedwe mʼthupi mwake. Munthu angathe kupereka zonse ali nazo malingana iyeyo ali ndi moyo. 5 Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kuwononga thupi lake, ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.”
6 Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako; koma moyo wake usawuchotse.”
7 Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova napita kukazunza Yobu ndi zilonda zaululu pa thupi lake lonse. 8 Pamenepo Yobu anatenga phale ndi kumadzikanda nalo atakhala pa dzala la phulusa.
9 Mkazi wake anati kwa iye, “Kodi ukuwumirirabe kukhala wangwiro? Tukwana Mulungu kuti ufe!”
10 Yobu anayankha kuti, “Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?”
Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula.
Abwenzi Atatu a Yobu
11 Abwenzi atatu a Yobu, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama, atamva za tsoka lonse limene linamugwera iye, ananyamuka ku nyumba zawo nakumana malo amodzi mopangana kuti apite ndi kukamupepesa Yobu ndi kumutonthoza. 12 Atamuona Yobuyo, iwo ali chapatalipo, sanathe kumuzindikira. Choncho anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba mikanjo yawo ndi kuwaza fumbi pa mitu yawo. 13 Tsono anakhala naye pamodzi pansi kwa masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku omwe. Palibe ndi mmodzi yemwe anayankhula naye, chifukwa anazindikira kuti Yobu amavutika kwambiri.
Mawu a Yobu
3 Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. 2 Ndipo Yobu anati:
3 “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe
ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
4 Tsiku limenelo lisanduke mdima;
Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso;
kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
5 Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli;
mtambo uphimbe tsikuli;
mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
6 Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani;
usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka,
kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
7 Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino;
kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
8 Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo,
iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
9 Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima;
tsikulo liyembekezere kucha pachabe
ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
10 Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga
ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.
11 “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa
ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
12 Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo
ndi mawere woti andiyamwitsepo?
13 Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere;
ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
14 pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi,
amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
15 pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide,
amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
16 Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale,
ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
17 Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto,
ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
18 A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere;
sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
19 Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko,
ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.
20 “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto,
ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
21 kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera,
amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
22 amene amakondwa ndi kusangalala
akamalowa mʼmanda?
23 Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu
amene njira yake yabisika,
amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
24 Mʼmalo moti ndidye, ndimalira,
ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
25 Chimene ndinkachiopa chandigwera;
chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
26 Ndilibe mtendere kapena bata,
ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
Mawu a Elifazi
4 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe?
Koma ndani angakhale chete wosayankhula?
3 Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri,
momwe walimbitsira anthu ofowoka.
4 Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa;
unachirikiza anthu wotha mphamvu.
5 Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima,
zakukhudza ndipo uli ndi mantha.
6 Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako?
Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako?
7 “Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse?
Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa?
8 Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa,
ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo.
9 Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu;
amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake.
10 Mikango imabangula ndi kulira,
komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa.
11 Mkango umafa chifukwa chosowa nyama,
ndipo ana amkango amamwazikana.
12 “Mawu anabwera kwa ine mwamseri,
makutu anga anamva kunongʼona kwake.
13 Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku,
nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato,
14 ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera
ndipo mafupa anga onse anaweyeseka.
15 Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga,
ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo.
16 Chinthucho chinayimirira
koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani.
Chinthu chinayima patsogolo panga,
kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti,
17 ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu?
Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake?
18 Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe,
ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa,
19 nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi,
amene maziko awo ndi fumbi,
amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche!
20 Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa;
mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya.
21 Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu,
kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’
5 “Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe?
Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?
2 Mkwiyo umapha chitsiru,
ndipo njiru imawononga wopusa.
3 Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu,
koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.
4 Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe;
amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.
5 Anthu anjala amamudyera zokolola zake,
amamutengera ndi za pa minga pomwe,
ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
6 Pakuti masautso satuluka mʼfumbi,
ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.
7 Komatu munthu amabadwira kuti azunzike
monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.
8 “Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu;
ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.
9 Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,
zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.
10 Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi,
ndipo amathirira minda ya anthu.
11 Iye amakweza anthu wamba,
ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.
12 Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera,
kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.
13 Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,
ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
14 Mdima umawagwera nthawi yamasana;
nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.
15 Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo;
amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.
16 Choncho osauka ali ndi chiyembekezo,
ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.
17 “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula;
nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.
18 Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo;
Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.
19 Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi,
mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.
20 Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa,
ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.
21 Adzakuteteza kwa anthu osinjirira,
ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.
22 Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala,
ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.
23 Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako,
ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.
24 Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa;
udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.
25 Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri,
ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.
26 Udzafika ku manda utakalamba,
monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.
27 “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona,
choncho uzimvere ndi kuzitsata.”
Mawu a Yobu
6 Tsono Yobu anayankha kuti,
2 “Achikhala mavuto anga anayezedwa,
ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo!
3 Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja;
nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula.
4 Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya,
thupi langa likumva ululu wa miviyo;
zoopsa za Mulungu zandizinga.
5 Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu,
nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya?
6 Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere,
nanga choyera cha dzira chimakoma?
7 Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe;
zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi.
8 “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha,
chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera,
9 achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye,
kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu!
10 Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi,
ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu
podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo.
11 “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo?
Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe?
12 Kodi ine ndili ndi mphamvu?
Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo?
13 Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha,
nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine?
14 “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,
ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
15 Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga,
ngati mitsinje imene imathamanga.
16 Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja,
imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
17 koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe,
ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
18 Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi;
iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
19 Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi,
anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
20 Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi;
koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
21 Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza,
mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
22 Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake,
ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
23 ndilanditseni mʼdzanja la mdani,
ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
24 “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete;
ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
25 Ndithu, mawu owona ndi opweteka!
Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
26 Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena,
ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
27 Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye
ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
28 “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana.
Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
29 Fewani mtima, musachite zosalungama;
ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
30 Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga?
Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?
7 “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi?
Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?
2 Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo,
kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,
3 choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe,
ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.
4 Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’
Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.
5 Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera,
khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.
6 “Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu,
ndipo amatha wopanda chiyembekezo.
7 Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya;
sindidzaonanso masiku achisangalalo.
8 Amene akundiona tsopano akundiona;
mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.
9 Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,
momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.
10 Iye sadzabweranso ku nyumba kwake
ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.
11 “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete;
ndidzayankhula mopsinjika mtima,
ndidzadandaula mowawidwa mtima.
12 Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja
kuti inu mundiyikire alonda?
13 Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga
ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,
14 ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto
ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,
15 kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa,
kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.
16 Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse.
Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.
17 “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,
kuti muzisamala zochita zake,
18 kuti muzimusanthula mmawa uliwonse
ndi kumamuyesa nthawi yonse?
19 Kodi simudzaleka kumandizonda
kuti ndipezeko mpata wopumula?
20 Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu,
Inu wopenyetsetsa anthu?
Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu?
Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?
21 Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga
ndi kundichotsera machimo anga?
Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda;
mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.