Beginning
Yosiya Achita Chikondwerero cha Paska
35 Yosiya anachita chikondwerero cha Paska wa Yehova mu Yerusalemu, ndipo mwana wankhosa wa Paska anaphedwa pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba. 2 Iye anasankha ansembe pa maudindo awo ndipo anawalimbikitsa pa ntchito ya mʼnyumba ya Yehova. 3 Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli. 4 Mukhale mʼmagulu anu molingana ndi mabanja anu, molingana ndi momwe analembera Davide mfumu ya Israeli ndiponso mwana wake Solomoni.
5 “Muziyima ku malo opatulika pamodzi ndi gulu la Alevi oyimira gulu lililonse lalingʼono la mabanja a abale anu amene ndi anthu wamba. 6 Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.”
7 Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu.
8 Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300. 9 Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi.
10 Mwambo unakonzedwa ndipo ansembe anayima pamalo pawo pamodzi ndi Alevi mʼmagulu awo monga mfumu inalamulira. 11 Ana ankhosa a Paska anaphedwa ndipo ansembe anawaza magazi amene anaperekedwa kwa iwo pamene Alevi anali kusenda nyamazo. 12 Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe. 13 Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse. 14 Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni.
15 Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse.
16 Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya. 17 Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri. 18 Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu. 19 Chikondwerero cha Paska ichi chinachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.
Imfa ya Yosiya
20 Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye. 21 Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.”
22 Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido.
23 Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.” 24 Choncho anamuchotsa iye mʼgaleta lake, ndipo anamuyika mʼgaleta lina limene anali nalo ndipo anabwera naye ku Yerusalemu kumene anamwalirira. Iye anayikidwa mʼmanda a makolo ake. Ndipo Ayuda ndi Yerusalemu yense anamulira.
25 Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro.
26 Zochitika zina za ulamuliro wa Yosiya ndi ntchito za kudzipereka kwake, monga zinalembedwa mʼMalamulo a Yehova, 27 zochitika zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.
36 Tsono anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namuyika kukhala mfumu mu Yerusalemu mʼmalo mwa abambo ake.
Yehowahazi Mfumu ya Yuda
2 Yowahazi anali wa zaka 23 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu. 3 Mfumu ya Igupto inamuchotsa pa udindo wa ufumu mu Yerusalemu ndipo inakhometsa msonkho dziko la Yuda wa makilogalamu 3,400 asiliva ndi agolide. 4 Mfumu ya Igupto inakhazika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehowahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasintha dzina la Eliyakimu kukhala Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yowahazi mʼbale wake wa Eliyakimu ndi kupita naye ku Igupto.
Yehoyakimu Mfumu ya Yuda
5 Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. 6 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anachita naye nkhondo ndipo anamumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kumutenga kupita naye ku Babuloni. 7 Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.
8 Zochitika zina za pa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zonyansa zimene anachita ndi zonse zinapezeka kuti zinali zomutsutsa zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehoyakini Mfumu ya Yuda
9 Yehoyakini anali ndi zaka 21 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu ndi masiku khumi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 10 Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.
Zedekiya Mfumu ya Yuda
11 Zedekiya anali ndi zaka 21 pamene ankakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. 12 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake ndipo sanadzichepetse yekha pamaso pa mneneri Yeremiya amene ankayankhula mawu a Yehova. 13 Iye anawukiranso mfumu Nebukadinezara amene anamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Iyeyo anali wosamva ndipo anawumitsa mtima wake. Sanatembenukire kwa Yehova Mulungu wa Israeli. 14 Kuwonjezera apo, atsogoleri onse a ansembe ndi anthu ena anapitirapitira kukhala osakhulupirika, kutsatira machitidwe onse onyansa a mitundu ina ndi kudetsa Nyumba ya Yehova Mulungu wawo, imene anayipatula mu Yerusalemu.
Kugwetsedwa kwa Yerusalemu
15 Yehova, Mulungu wa makolo awo, ankatumiza mawu kwa iwo kudzera kwa amithenga ake kawirikawiri, chifukwa ankawamvera chisoni anthu ake ndi malo ake okhalapo. 16 Koma iwo ananyoza amithenga a Mulungu, anapeputsa mawu awo ndipo ankaseka aneneri ake mpaka anawutsa mkwiyo wa Yehova pa anthu ake ndipo panalibenso mankhwala owachiritsa. 17 Yehova anabweretsa mfumu ya anthu a ku Babuloni, imene inapha anyamata awo ndi lupanga ku malo opatulika, ndipo sanasiye kaya mnyamata kapena mtsikana, wamkulu kapena wokalamba. Mulungu anapereka onsewo kwa Nebukadinezara. 18 Iye ananyamula kupita nazo ku Babuloni zipangizo zonse za mʼNyumba ya Yehova Mulungu wawo, zazikulu ndi zazingʼono zomwe, ndi chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso chuma cha mfumu ndi akuluakulu ake. 19 Iwo anayatsa moto Nyumba ya Mulungu, ndipo anagwetsa makoma a Yerusalemu. Anatentha moto nyumba zonse zaufumu ndipo anawononga chilichonse chimene chinali chofunika.
20 Iye anagwira ukapolo anthu otsala amene anapulumuka ku lupanga ndi kupita nawo ku Babuloni, ndipo anakhala antchito ake ndi ana ake mpaka pamene ufumu wa Peresiya unakhazikitsidwa. 21 Dziko linakondwera ndi masabata ake. Pa nthawi yonse ya chipasuko chake nthaka inapuma, mpaka zaka 70 zinakwana pokwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya.
22 Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:
23 Chimene mfumu Koresi ya Peresiya ikunena ndi ichi:
“Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa ine mafumu onse a dziko lapansi ndipo wandisankha kuti ndimumangire Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ku Yuda. Aliyense wa anthu ake pakati panu, Yehova Mulungu wake akhale naye, ndipo apite.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.