Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Estere 1-5

Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa

Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.

Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake.

Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero.

10 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi 11 kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. 12 Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima.

13 Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. 14 Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo.

15 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?”

16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. 17 Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ 18 Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.”

19 “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. 20 Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.”

21 Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. 22 Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera.

Mfumu Ikwatira Estere

Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola. Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola. Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo.

Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa. Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda. Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.

Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja. Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.

10 Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero. 11 Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji.

12 Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa. 13 Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu. 14 Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.

15 Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye. 16 Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.

17 Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. 18 Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu.

Mordekai Awulula Chiwembu

19 Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu. 20 Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera.

21 Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. 22 Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai. 23 Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.

Chiwembu cha Hamani Chopha a Yuda

Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse. Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.

Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?” Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda.

Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri. Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira.

Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.

Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere. Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.”

10 Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. 11 Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.”

12 Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake. 13 Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo. 14 Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo.

15 Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka.

Mordekai a Pempha Estere kuti Athandize

Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima. Ndipo anapita ndi kuyima pa chipata cha mfumu, chifukwa panalibe wina aliyense amaloledwa kulowa pa chipata cha mfumu atavala chiguduli. Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.

Anamwali otumikira mfumukazi Estere ndi adindo ake ofulidwa atabwera ndi kumuwuza za Mordekai, anavutika kwambiri. Estere anamutumizira zovala kuti avale ndi kuti avule chiguduli chake koma Mordekai sanalole zimenezo. Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi.

Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu. Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda. Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake.

Hataki anabwerera ndi kumufotokozera Estere zimene Mordekai ananena. 10 Ndipo Estere anamutuma Hataki kuti akanene kwa Mordekai kuti, 11 “Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”

12 Tsono Mordekai anawuzidwa mawu a Estere. 13 Kenaka Mordekai anawawuza kuti akamuyankhe Estere motere: “Usaganize kuti iwe wekha mwa Ayuda onse udzapulumuka chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu. 14 Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?”

15 Pamenepo Estere anatumiza yankho ili kwa Mordekai: 16 “Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.”

17 Choncho Mordekai anapita ndi kuchita monga Estere anamupemphera.

Pempho la Estere kwa Mfumu

Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.

Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”

Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.”

Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.”

Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.”

Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.”

Mkwiyo wa Hamani Ukulabe pa Mordekai

Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, 10 komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake.

Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. 11 Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. 12 Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. 13 Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.”

14 Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.