Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Oweruza 3-5

Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani (Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose.

Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo.

Otanieli

Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. 10 Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. 11 Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira.

Ehudi

12 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. 13 Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. 14 Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18.

15 Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. 16 Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. 17 Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. 18 Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. 19 Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.”

Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.

20 Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, 21 Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. 22 Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. 23 Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho.

24 Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. 25 Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa.

26 Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. 27 Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko.

28 Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. 29 Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. 30 Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80.

Samugara

31 Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli.

Debora

Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri.

Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ”

Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.”

Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. 10 Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi.

11 Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi.

12 Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, 13 anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni.

14 Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. 15 Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. 16 Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala.

17 Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja.

18 Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda.

19 Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso.

20 Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ”

21 Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo.

22 Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake.

23 “Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. 24 Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu.

Nyimbo ya Debora

“Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:

“Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli;
    ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu,
    tamandani Yehova:

“Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu!
    Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova,
    Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.

“Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri,
    pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu,
dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka
    nigwetsa madzi.
Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,
    Mulungu wa Israeli.

“Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati,
    pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa;
    alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi
    mpaka pamene iwe Debora unafika;
    unafika ngati mayi ku Israeli.
Pamene anasankha milungu ina,
    nkhondo inabwera ku zipata za mzinda,
ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke
    pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli,
    uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu.
    Tamandani Yehova!

10 “Inu okwera pa abulu oyera,
    okhala pa zishalo,
    ndi inu oyenda pa msewu,
yankhulani. 11 Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta;
    kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana;
    akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli.

“Choncho anthu a Yehova
    anasonkhana ku zipata za mzinda.
12 Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera;
    tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.
Iwe Baraki! nyamuka
    Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’

13 “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo;
    anthu a Yehova anapita
kukamenyera Yehova nkhondo
    kulimbana ndi adani amphamvu.
14 Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu;
    akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako.
Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri,
    ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
15 Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora;
    inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki,
    ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira.
Koma pakati pa mafuko a Rubeni
    panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
16 Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera
    zitoliro zoyitanira nkhosa?
Pakati pa anthu a fuko la Rubeni
    panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
17 Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani.
    Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi?
Aseri anali pa gombe la Nyanja;
    anangokhala mʼmadooko mwawo.
18 Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa.
    Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.

19 “Mafumu anabwera, anachita nkhondo;
    mafumu Akanaani anachita nkhondo
ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,
    koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
20 Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo,
    zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,
    chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola.
    Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
22 Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu,
    akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
23 Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’
    ‘Tembererani nzika zake mwaukali,
chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova,
    kulimbana ndi adani ake amphamvu.’

24 “Akhale wodala kupambana akazi onse,
    Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni;
    inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
25 Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka;
    anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
26 Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake,
    anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja.
Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake,
    ndi kumubowola mu litsipa mwake.
27 Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa,
    anagwa; iye anagona pamenepo.
Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa;
    pamene anagwera, pamenepo anaferapo.

28 “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera;
    nafuwula mokweza kuti,
‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika?
    Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
29 Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha,
    ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
30 ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane;
    akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri.
    Sisera akumupatsa zofunkha:
    zovala zonyikidwa mu utoto,
    zoti ndizivala mʼkhosi
zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’

31 “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke,
    koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa
    pamene lituluka ndi mphamvu zake.”

Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.