Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 7-9

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako. Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto, iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto. Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.”

Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira. Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao.

Ndodo ya Aaroni Isanduka Njoka

Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.”

10 Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. 11 Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. 12 Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. 13 Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.

Mliri wa Magazi

14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite. 15 Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako. 16 Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. 17 Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: 18 Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ”

19 Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”

20 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. 21 Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.

22 Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu. 23 Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire. 24 Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo.

Mliri wa Achule

25 Panapita masiku asanu ndi awiri Yehova atamenya madzi a mu mtsinje wa Nailo.

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Ukamuwuze Farao kuti, Lolani anthu anga kuti apite, akandipembedze. Ndipo ngati simulola kuti apite Ine ndidzalanga dziko lonse la Igupto polidzaza ndi achule. Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo. Achulewo adzakulumphira iwe ndi anthu ako ndiponso nduna zako.”

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ”

Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto. Koma amatsenga anachita zinthu zomwezo mʼmatsenga awo. Iwonso anatulutsa achule mʼdziko lonse la Igupto.

Kenaka, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Pemphera kwa Yehova kuti achulewa achoke kwa ine ndi anthu anga, ndipo ine ndidzalola kuti anthu anu apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”

Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.”

10 Farao anati, “Mawa.”

Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu. 11 Achule adzachoka mʼnyumba yanu, mʼnyumba za nduna zanu pamodzi ndi za anthu anu. Koma adzatsala mu mtsinje wa Nailo basi.”

12 Mose ndi Aaroni anachoka, ndipo Mose anapemphera kwa Yehova kuti achotse achule amene anatumiza kwa Farao. 13 Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha. Achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anafa 14 Aigupto anawunjika achulewo milumilu ndipo dziko linanunkha. 15 Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.

Mliri wa Nsabwe

16 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.” 17 Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe. 18 Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo.

19 Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.

Mliri wa Ntchentche Zoluma

20 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze. 21 Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’ ”

22 “Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino. 23 Ndidzasiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chizindikiro chozizwitsa ichi chidzachitika mawa.”

24 Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto.

25 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu mʼdziko lomwe lino.”

26 Koma Mose anati, “Sitingathe kutero pakuti nsembe zathu kwa Yehova Mulungu ndi zowayipira Aigupto. Ngati tipereke nsembe zowayipira Aigupto mʼmaso mwawo, adzatiponya miyala kuti tife. 27 Ife tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu kupita ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu monga anatilamulira.”

28 Farao anati, “Ine ndikulolani kuti mupite ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma musapite kutali kwambiri. Tsopano ndipempherereni.”

29 Mose anayankha kuti, “Ine ndikangochoka pano, ndikapemphera kwa Yehova ndipo mawa lomweli ntchentche zoluma zidzachoka kwa Farao, nduna zake pamodzi ndi anthu ake. Koma Farao, onetsetsani kuti musachitenso zachinyengo ndi kuwakaniza anthu kuti asakapereke nsembe kwa Yehova.”

30 Choncho Mose anasiyana ndi Farao nakapemphera kwa Yehova. 31 Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala. 32 Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke.

Mliri pa Ziweto

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao ndipo ukamuwuze kuti Yehova, Mulungu wa Ahebri akuti alole anthu anga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri. Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.”

Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.” Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite.

Mliri wa Zotupa

Kenaka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Tapani phulusa la pa moto lodzaza dzanja ndipo Mose aliwaze mmwamba pamaso pa Farao. Phulusalo lidzasanduka fumbi pa dziko lonse la Igupto. Tsono fumbilo lidzasanduka zithupsa zomaphulika nʼkukhala zilonda pa munthu aliyense ndi pa nyama zomwe mʼdziko lonse la Igupto.”

10 Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto. 11 Amatsenga sanathe kumuyandikira Mose chifukwa nawonso anali ndi zithupsa monga mmene analili Aigupto ena onse. 12 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.

Mliri wa Mvula ya Matalala

13 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze. 14 Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi. 15 Pakuti ndikanakhala nditatukula kale dzanja langa ndikupheratu iwe pamodzi ndi anthu ako onse pa dziko lapansi. 16 Koma ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga kwa iwe ndiponso kuti dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi. 17 Komabe iwe ukudzitukumula pa anthu anga osawalola kuti atuluke. 18 Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero. 19 Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.”

20 Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba. 21 Koma iwo amene ananyozera mawu a Yehova anasiya akapolo ndi ziweto zawo panja.

22 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti matalala agwe pa dziko lonse la Igupto, pa munthu aliyense, pa ziweto ndi pa zonse zomera mʼminda ya Igupto.” 23 Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. 24 Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha. 25 Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse. 26 Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli.

27 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 Upemphere kwa Mulungu chifukwa mabingu ndi matalala atikwana. Ine ndidzakulolani kuti mupite. Simuyenera kukhalabe kuno.”

29 Mose anayankha, “Ndikangotuluka mu mzinda muno, ine ndidzakweza manja anga kwa Yehova ndi kupemphera. Mabingu ndi matalalawa adzaleka ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova ndiye akulamulira dziko lapansi. 30 Koma ine ndikudziwa kuti inu ndi nduna zanu simukuopabe Yehova Mulungu.”

31 Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa. 32 Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa.

33 Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo. 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zaleka, anachimwanso. Iye ndi nduna zake anawumitsanso mitima yawo. 35 Choncho Farao sanalole kuti Aisraeli apite monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.