Beginning
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.
46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
3 ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
5 Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
Mulungu adzawuthandiza mmawa.
6 Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.
7 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
8 Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
9 Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”
11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
anayika anthu pansi pa mapazi athu.
4 Iye anatisankhira cholowa chathu,
chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
Sela
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
imbirani Iye salimo la matamando.
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
Iye wakwezedwa kwakukulu.
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.
48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
2 Lokongola mu utali mwake,
chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
mzinda wa Mfumu yayikulu.
3 Mulungu ali mu malinga ake;
Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
4 Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
5 iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
anathawa ndi mantha aakulu.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
7 Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
8 Monga momwe tinamvera,
kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
mu mzinda wa Mulungu wathu.
Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
9 Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
midzi ya Yuda ndi yosangalala
chifukwa cha maweruzo anu.
12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
penyetsetsani malinga ake,
kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
49 Imvani izi anthu a mitundu yonse;
mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
2 anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,
olemera pamodzinso ndi osauka:
3 Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;
mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
4 Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,
ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.
5 Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,
pamene achinyengo oyipa andizungulira.
6 Iwo amene adalira kulemera kwawo
ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
7 Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake
kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
8 Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,
palibe malipiro amene angakwanire,
9 kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya
ndi kusapita ku manda.
10 Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;
opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka
ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11 Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,
malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,
ngakhale anatchula malo mayina awo.
12 Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,
adzafa ngati nyama.
13 Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,
ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula.
Sela
14 Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,
ndipo imfa idzawadya.
Olungama adzawalamulira mmawa;
matupi awo adzavunda mʼmanda,
kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
15 Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;
ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.
16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,
pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17 Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,
ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18 Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,
ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19 iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,
amene sadzaonanso kuwala.
20 Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru
adzafa ngati nyama yakuthengo.
Salimo la Asafu.
50 Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
2 Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
Mulungu akuwala.
3 Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
moto ukunyeketsa patsogolo pake,
ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
4 Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
5 Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
6 Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
7 Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
ndine Mulungu, Mulungu wako.
8 Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
9 Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako
kapena mbuzi za mʼkhola lako,
10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga
ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
11 Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri
ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
12 Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,
pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
13 Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna
kapena kumwa magazi a mbuzi?
14 “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,
kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
15 Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;
Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,
“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga
kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
17 Iwe umadana ndi malangizo anga
ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
18 Ukaona wakuba umamutsatira,
umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa
ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
20 Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako
ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
21 Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;
umaganiza kuti ndine wofanana nawe
koma ndidzakudzudzula
ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
chipulumutso cha Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.