Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 36-39

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

36 Uthenga uli mu mtima mwanga
    wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:
Mu mtima mwake
    mulibe kuopa Mulungu.
Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri,
    sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.
Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo;
    iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.
Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa;
    iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo
    ndipo sakana cholakwa chilichonse.

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
    kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
    chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
    Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
    amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
    Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
    mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
    chilungamo chanu kwa olungama mtima.
11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,
    kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
12 Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa,
    aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!

Salimo la Davide.

37 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa
    kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,
    ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.

Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
    khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
Udzikondweretse wekha mwa Yehova
    ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Pereka njira yako kwa Yehova;
    dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,
    chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
    usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
    pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,
    usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,
    koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;
    ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko
    ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.

12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama
    ndipo amawakukutira mano;
13 koma Ambuye amaseka oyipa
    pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

14 Oyipa amasolola lupanga
    ndi kupinda uta
kugwetsa osauka ndi osowa,
    kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,
    ndipo mauta awo anathyoka.

16 Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo
    ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;
17 pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,
    koma Yehova amasunga olungama.

18 Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova,
    ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.
19 Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota;
    mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri.

20 Koma oyipa adzawonongeka;
    adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo,
    iwo adzazimirira ngati utsi.

21 Oyipa amabwereka ndipo sabweza
    koma olungama amapereka mowolowamanja.
22 Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko,
    koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa.

23 Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu,
    amakhazikitsa mayendedwe ake;
24 ngakhale atapunthwa sadzagwa,
    pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.

25 Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba
    koma sindinaonepo olungama akusiyidwa
    kapena ana awo akupempha chakudya.
26 Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu;
    ana awo adzadalitsika.

27 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
    pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya.
28 Pakuti Yehova amakonda wolungama
    ndipo sadzasiya okhulupirika ake.

Iwo adzatetezedwa kwamuyaya,
    koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa;
29 olungama adzalandira dziko
    ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.

30 Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru,
    ndipo lilime lake limayankhula zolungama.
31 Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake;
    mapazi ake saterereka.

32 Oyipa amabisala kudikira olungama;
    kufunafuna miyoyo yawoyo;
33 koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo
    kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu.

34 Khulupirira Yehova,
    ndipo sunga njira yake;
Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako;
    udzaona anthu oyipa akuwonongeka.

35 Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo
    akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake.
36 Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso;
    ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso.

37 Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama;
    udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.
38 Koma anthu ochimwa adzawonongeka;
    iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe.

39 Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;
    Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.
40 Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa;
    Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa,
    pakuti amathawira kwa Iye.

Salimo la Davide. Kupempha.

38 Yehova musandidzudzule mutapsa mtima
    kapena kundilanga muli ndi ukali.
Pakuti mivi yanu yandilasa,
    ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa;
    mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
Kulakwa kwanga kwandipsinja
    ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.

Mabala anga akuwola ndipo akununkha
    chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri;
    tsiku lonse ndimangolira.
Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika,
    mulibe thanzi mʼthupi langa.
Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu;
    ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.

Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,
    kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
10 Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha;
    ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga;
    anansi anga akhala kutali nane.
12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo,
    oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga;
    tsiku lonse amakonza zachinyengo.

13 Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve,
    monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
14 Ndakhala ngati munthu amene samva,
    amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
15 Ndikudikira Inu Yehova;
    mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere
    kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”

17 Pakuti ndili pafupi kugwa,
    ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
18 Ndikuvomereza mphulupulu zanga;
    ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
19 Ambiri ndi adani anga amphamvu;
    amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino
    amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

21 Inu Yehova, musanditaye;
    musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
22 Bwerani msanga kudzandithandiza,
    Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

39 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga
    ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;
ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero
    nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
Koma pamene ndinali chete
    osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino
    mavuto anga anachulukirabe.
Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,
    ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;
    kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

“Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga
    ndi chiwerengero cha masiku anga;
    mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.
Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,
    kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;
    moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.
            Sela
Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:
    Iye amangovutika koma popanda phindu;
    amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?
    Chiyembekezo changa chili mwa Inu.
Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;
    musandisandutse chonyozeka kwa opusa.
Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga
    pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.
10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;
    ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.
11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;
    mumawononga chuma chawo monga njenjete;
    munthu aliyense ali ngati mpweya.
            Sela

12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,
    mverani kulira kwanga kopempha thandizo;
    musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,
popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;
    monga anachitira makolo anga onse.
13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala
    ndisanafe ndi kuyiwalika.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.