Beginning
Salimo la Davide. Malangizo.
32 Ngodala munthu
amene zolakwa zake zakhululukidwa;
amene machimo ake aphimbidwa.
2 Ngodala munthu
amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
3 Pamene ndinali chete,
mafupa anga anakalamba
chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
4 Pakuti usana ndi usiku
dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
monga nthawi yotentha yachilimwe.
Sela
5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
mlandu wa machimo anga.”
Sela
6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
sadzamupeza.
7 Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela
8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
koma chikondi chosatha cha Yehova
chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
33 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,
nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
2 Mutamandeni Yehova ndi pangwe;
muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
3 Muyimbireni nyimbo yatsopano;
imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
4 Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;
Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
5 Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;
dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
6 Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,
zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
7 Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;
amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
8 Dziko lonse lapansi liope Yehova;
anthu onse amulemekeze Iye.
9 Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;
Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;
Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.
Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka.
34 Ndidzayamika Yehova nthawi zonse;
matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
2 Moyo wanga udzanyadira Yehova;
anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine;
tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.
4 Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha;
anandilanditsa ku mantha anga onse.
5 Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira;
nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.
6 Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva;
Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
7 Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye
ndi kuwalanditsa.
8 Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;
wodala munthu amene amathawira kwa Iye.
9 Wopani Yehova inu oyera mtima ake,
pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.
10 Mikango itha kulefuka ndi kumva njala
koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.
11 Bwerani ana anga, mundimvere;
ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.
12 Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake
ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,
13 asunge lilime lake ku zoyipa
ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
14 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;
funafuna mtendere ndi kuwulondola.
15 Maso a Yehova ali pa olungama
ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;
16 nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa,
kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.
17 Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;
Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
18 Yehova ali pafupi kwa osweka mtima
ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
19 Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri,
Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,
20 Iye amateteza mafupa ake onse,
palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.
21 Choyipa chidzapha anthu oyipa;
adani a olungama adzapezeka olakwa.
22 Yehova amawombola atumiki ake;
aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.
Salimo la Davide.
35 Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;
mumenyane nawo amene akumenyana nane.
2 Tengani chishango ndi lihawo;
dzukani ndipo bwerani mundithandize.
3 Tengani mkondo ndi nthungo,
kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.
Uzani moyo wanga kuti,
“Ine ndine chipulumutso chako.”
4 Iwo amene akufunafuna moyo wanga
anyozedwe ndi kuchita manyazi;
iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke
abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
5 Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo
pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
6 Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera
pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
7 Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa
ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
8 chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa
ukonde umene iwo abisa uwakole,
agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
9 Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova
ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera,
“Ndani angafanane nanu Yehova?
Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,
osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14 ndinayendayenda ndi kulira maliro,
kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
19 Musalole adani anga onyenga
akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
koma amaganizira zonamizira
iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
ndi za matamando anu tsiku lonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.