Beginning
Pemphero la Davide.
17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
2 Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
maso anu aone chimene ndi cholungama.
3 Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
4 Kunena za ntchito za anthu,
monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
posatsata njira zachiwawa.
5 Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
mapazi anga sanaterereke.
6 Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
7 Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
8 Mundisunge ine ngati mwanadiso;
mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
9 kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.
10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
ngati mkango waukulu wokhala mobisala.
13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.
Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
18 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
2 Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;
Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.
Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
3 Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
4 Zingwe za imfa zinandizinga;
mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
5 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
misampha ya imfa inalimbana nane.
6 Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.
Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;
kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
7 Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,
ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;
ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
8 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;
moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,
makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
9 Iye anangʼamba thambo natsika pansi;
pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
10 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;
nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
11 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,
chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.
12 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala,
makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.
13 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,
mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
14 Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,
ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
15 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera;
maziko a dziko lapansi anakhala poyera,
Yehova atabangula mwaukali,
pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.
16 Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;
anandivuwula mʼmadzi ozama.
17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.
18 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,
koma Yehova anali thandizo langa.
19 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;
anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
20 Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
21 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
22 Malamulo ake onse ali pamaso panga;
sindinasiye malangizo ake.
23 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
24 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.
25 Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;
kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
26 kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
27 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
28 Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;
Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
29 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;
ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
30 Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
kwa onse amene amathawira kwa Iye.
31 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
32 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu
ndi kulungamitsa njira yanga.
33 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;
Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
34 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
35 Inu mumandipatsa chishango chachipambano,
ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;
mumawerama pansi kundikuza.
36 Munakulitsa njira yoyendamo ine,
kuti mapazi anga asaguluke.
37 Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira;
sindinabwerere mpaka atawonongedwa.
38 Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka;
anagwera pa mapazi anga.
39 Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo,
munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.
40 Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa,
ndipo ine ndinawononga adani angawo.
41 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.
Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
42 Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.
Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;
mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
akangomva za ine amandigonjera.
45 Iwo onse anataya mtima;
anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!
Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
48 amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;
ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;
amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
3 Iye akumbukire nsembe zako zonse
ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
Sela
4 Akupatse chokhumba cha mtima wako
ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
Tiyankheni pamene tikuyitanani!
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.