Beginning
BUKU LOYAMBA
Masalimo 1–41
1 Wodala munthu
amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
4 Sizitero ndi anthu oyipa!
Iwo ali ngati mungu
umene umawuluzidwa ndi mphepo.
5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.
6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.
2 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
Akonzekeranji zopanda pake anthu?
2 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
ndi wodzozedwa wakeyo.
3 Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
ndipo titaye zingwe zawo.”
4 Wokhala mmwamba akuseka;
Ambuye akuwanyoza iwowo.
5 Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
6 “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
pa Ziyoni, phiri langa loyera.”
7 Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:
Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
lero Ine ndakhala Atate ako.
8 Tandipempha,
ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
9 Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”
10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;
chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova mwa mantha
ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.
Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.
3 Inu Yehova, achulukadi adani anga!
Achulukadi amene andiwukira!
2 Ambiri akunena za ine kuti,
“Mulungu sadzamupulumutsa.”
Sela
3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,
Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.
4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula
ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.
Sela
5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo;
ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.
6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene
abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.
7 Dzukani, Inu Yehova!
Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.
Akantheni adani anga onse pa msagwada;
gululani mano a anthu oyipa.
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.
Madalitso akhale pa anthu anu.
Sela
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.
4 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,
Inu Mulungu wa chilungamo changa.
Pumulitseni ku zowawa zanga;
chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.
2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?
Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?
Sela.
3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;
Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.
4 Kwiyani koma musachimwe;
pamene muli pa mabedi anu,
santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.
Sela
5 Perekani nsembe zolungama
ndipo dalirani Yehova.
6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”
Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
mumandisamalira bwino.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide.
5 Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova,
ganizirani za kusisima kwanga
2 Mverani kulira kwanga kofuna thandizo,
Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,
pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
3 Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;
Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu
ndi kudikira mwachiyembekezo.
4 Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa;
choyipa sichikhala pamaso panu.
5 Onyada sangathe kuyima pamaso panu;
Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
6 Mumawononga iwo amene amanena mabodza;
anthu akupha ndi achinyengo,
Yehova amanyansidwa nawo.
7 Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu,
ndidzalowa mʼNyumba yanu;
mwa ulemu ndidzaweramira pansi
kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
8 Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu
chifukwa cha adani anga ndipo
wongolani njira yanu pamaso panga.
9 Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike;
mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko.
Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;
ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
10 Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu!
Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo.
Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri,
pakuti awukira Inu.
11 Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere;
lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe.
Aphimbeni ndi chitetezo chanu,
iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
12 Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama;
mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
kapena kundilanga mu ukali wanu.
2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;
Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.
Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;
Amakutamandani ndani ali ku manda?
6 Ine ndatopa ndi kubuwula;
usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;
ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;
akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,
pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;
Yehova walandira pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;
adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini.
7 Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu;
pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
2 mwina angandikadzule ngati mkango,
ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.
3 Inu Yehova Mulungu wanga,
ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
4 ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere,
kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
5 pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira,
lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi
ndipo mundigoneke pa fumbi.
Sela
6 Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu;
nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga.
Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
7 Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani.
Alamulireni muli kumwambako;
8 Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo.
Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa,
monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
9 Inu Mulungu wolungama,
amene mumasanthula maganizo ndi mitima,
thetsani chiwawa cha anthu oyipa
ndipo wolungama akhale motetezedwa.
10 Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba,
amene amapulumutsa olungama mtima.
11 Mulungu amaweruza molungama,
Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
12 Ngati munthu satembenuka,
Mulungu adzanola lupanga lake,
Iye adzawerama ndi kukoka uta.
13 Mulungu wakonza zida zake zoopsa;
Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.
14 Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse.
Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
15 Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa
amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
16 Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini;
chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.
17 Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;
ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.
8 Inu Yehova Ambuye athu,
dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
mʼmayiko onse akumwamba.
2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
zimene mwaziyika pa malo ake,
4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
ndi nyama zakuthengo,
8 mbalame zamlengalenga
ndi nsomba zamʼnyanja
zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
9 Inu Yehova, Ambuye athu,
dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.