Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 40-42

40 Yehova anati kwa Yobu:

“Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse?
    Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”

Pamenepo Yobu anayankha Yehova:

“Ine sindili kanthu konse,
    kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.
Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho,
    ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”

Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,

“Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna;
    ndikufunsa mafunso
    ndipo iwe undiyankhe.

“Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama?
    Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu,
    ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?
10 Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola,
    ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.
11 Tsanula ukali wako wosefukirawo,
    uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,
12 Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,
    uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.
13 Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi;
    ukulunge nkhope zawo mʼmanda.
14 Ukatero Ine ndidzakuvomereza
    kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.

15 “Taganiza za mvuwu,
    imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe,
    ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.
16 Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri,
    thupi lake ndi lanyonga kwambiri!
17 Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza;
    mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
18 Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa,
    nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
19 Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu,
    komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.
20 Imapeza chakudya chake ku mtunda
    ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.
21 Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta,
    imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.
22 Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta;
    imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.
23 Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha,
    iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.
24 Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza
    kapena kuyikola mu msampha?

41 “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba
    kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake,
    kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo?
    Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
Kodi idzachita nawe mgwirizano
    kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
Kodi udzasewera nayo ngati mbalame,
    kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
Kodi anthu adzayitsatsa malonda?
    Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga,
    kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo,
    ndipo iweyo sudzabwereranso.
Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza;
    kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
10 Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa.
    Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
11 Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere?
    Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.

12 “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho,
    za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
13 Ndani angasende chikopa chake?
    Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
14 Ndani angatsekule kukamwa kwake,
    pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
15 Kumsana kwake kuli mizere ya mamba
    onga zishango zolumikizanalumikizana;
16 Mambawo ndi olukanalukana
    kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
17 Ndi olumikizanalumikizana;
    ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
18 Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali;
    maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
19 Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo
    mumathetheka mbaliwali zamoto.
20 Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi
    ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
21 Mpweya wake umayatsa makala,
    ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
22 Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake;
    aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
23 Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo
    ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
24 Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala,
    ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
25 Ngʼonayo ikangovuwuka,
    ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
26 Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu,
    ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
27 Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe
    ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
28 Muvi sungathe kuyithawitsa,
    miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
29 Zibonga zimakhala ngati ziputu;
    imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
30 Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo
    imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
31 Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali,
    imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
32 Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee,
    kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
33 Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho,
    nʼcholengedwa chopanda mantha.
34 Chimanyoza nyama zina zonse;
    icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”

Yobu

42 Pamenepo Yobu anayankha Yehova kuti,

“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse;
    chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.
Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru?
    Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse,
    zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe.

“Inu munandiwuza kuti, ‘Mvetsetsa tsopano ndipo ndidzayankhula;
    ndidzakufunsa
    ndipo iwe udzandiyankhe.’
Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga,
    koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.
Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi,
    ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”

Mulungu Adalitsa Yobu

Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu. Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.” Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama anachita zimene Yehova anawawuza ndipo Yehova anamvera pemphero la Yobu.

10 Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale. 11 Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.

12 Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. 13 Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu. 14 Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki. 15 Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.

16 Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi. 17 Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.