Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yobu 38-39

Yehova Ayankhula

38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:

“Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
    poyankhula mawu opanda nzeru?
Onetsa chamuna;
    ndikufunsa
    ndipo undiyankhe.

“Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
    Ndiwuze ngati ukudziwa.
Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
    Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
Kodi maziko ake anawakumba potani,
    kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
    ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?

“Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
    pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
    ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
    ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
    apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’

12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,
    kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi
    ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;
    zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,
    ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.

16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja
    kapena pa magwero ake ozama?
17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?
    Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?
    Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.

19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?
    Nanga mdima umakhala kuti?
20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?
    Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!
    Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!

22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana
    kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
23 zimene ndazisungira nthawi ya mavuto
    ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani
    kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,
    nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,
    chipululu chopandamo munthu,
27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa
    ndi kumeretsamo udzu?
28 Kodi mvula ili ndi abambo ake?
    Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani?
    Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,
    pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?

31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?
    Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake
    kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?
    Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?

34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
    kuti igwetse mvula ya chigumula?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
    Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
    ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
    Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38 pamene fumbi limasanduka matope,
    ndipo matopewo amawumbika?

39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
    ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
    kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
    pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
    ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?

39 “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera?
    Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere?
    Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo;
    pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo;
    kenaka amachoka ndipo sabwereranso.

“Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera?
    Ndani amamasula zingwe zake?
Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake,
    nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda;
    ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu
    ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.

“Kodi njati ingavomere kukutumikira?
    Kodi ingagone mu gome lako usiku?
10 Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima?
    Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
11 Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake?
    Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
12 Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako
    ndi kumuyika ku malo opunthira?

13 “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira,
    koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.
14 Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi
    ndipo amafundidwa ndi nthaka,
15 nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa,
    ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.
16 Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake;
    Imayiwala zoti inavutika powabala.
17 Chifukwa Mulungu anayimana nzeru,
    simvetsa kanthu kalikonse.
18 Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga,
    imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.

19 “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo
    kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?
20 Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira,
    ukali wake nʼkumachititsa mantha?
21 Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake,
    ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
22 Iye sachita mantha, saopa chilichonse;
    sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.
23 Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake
    pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.
24 Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha;
    satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.
25 Lipenga likalira amati, ‘Twee!’
    Amamva fungo la nkhondo ali patali,
    kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.

26 “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako,
    ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?
27 Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka
    ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?
28 Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku;
    chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.
29 Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye;
    maso ake amachionera patali chinthucho.
30 Ana ake amayamwa magazi,
    ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.