Beginning
Mawu a Elihu
32 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. 2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. 3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. 4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. 5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:
“Ine ndine wamngʼono,
inuyo ndinu akuluakulu,
nʼchifukwa chake ndimaopa,
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru,
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 Ndadikira nthawi yonseyi,
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12 ineyo ndinakumvetseranidi.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;
mawu awathera.
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,
pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;
nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,
ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,
kapena kuyankhula zoshashalika,
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”
33 “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga;
mutcherere khutu zonse zimene ndinene.
2 Tsopano ndiyamba kuyankhula;
mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.
3 Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama;
pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.
4 Mzimu wa Mulungu wandiwumba,
mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
5 Mundiyankhe ngati mungathe;
konzekani tsopano kuti munditsutse.
6 Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu;
nanenso ndinachokera ku dothi.
7 Musachite mantha ndipo musandiope ayi,
Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.
8 “Koma inu mwayankhula ine ndikumva,
ndamva mawu anuwo onena kuti,
9 ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo;
ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.
10 Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo;
Iye akundiyesa ngati mdani wake.
11 Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo,
akulonda mayendedwe anga onse.’
12 “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi,
pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
13 Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye
kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?
14 Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana,
ngakhale munthu sazindikira zimenezi.
15 Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku,
pamene anthu ali mʼtulo tofa nato
pamene akungosinza chabe pa bedi,
16 amawanongʼoneza mʼmakutu
ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,
17 kumuchotsa munthu ku zoyipa,
ndi kuthetseratu kunyada kwake,
18 kumulanditsa munthu ku manda,
kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.
19 “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake,
nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,
20 kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya,
ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.
21 Thupi lake limawonda
ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.
22 Munthuyo amayandikira ku manda,
moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.
23 “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi,
mmodzi mwa ambirimbiri oterewa,
adzafotokoza zimene zili zoyenera,
24 kudzamukomera mtima ndi kunena kuti,
‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda;
ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’
25 pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana;
ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.
26 Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.
Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe
ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.
27 Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti,
‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama,
koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.
28 Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda,
ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’
29 “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu
kawirikawiri,
30 kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda,
kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.
31 “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere;
khalani chete kuti ndiyankhule.
32 Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni;
yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.
33 Koma ngati sichoncho, mundimvere;
khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”
34 Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,
2 “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru;
tcherani khutu inu anthu ophunzira.
3 Pakuti khutu limayesa mawu
monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.
4 Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera;
tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.
5 “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa,
koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.
6 Ngakhale ndine wolungama mtima,
akundiyesa wabodza;
ngakhale ndine wosachimwa,
mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’
7 Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani,
amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?
8 Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa;
amayanjana ndi anthu oyipa mtima.
9 Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu
poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’
10 “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu.
Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe,
Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.
11 Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake;
Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.
12 Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa,
kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.
13 Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani?
Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?
14 Mulungu akanakhala ndi maganizo
oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,
15 zamoyo zonse zikanawonongekeratu
ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.
16 “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi;
mvetserani zimene ndikunena.
17 Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira?
Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?
18 Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’
ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’
19 Iye sakondera akalonga
ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka,
pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?
20 Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku;
anthu amachita mantha ndipo amamwalira;
munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.
21 “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu;
amaona mayendedwe ake onse.
22 Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani
kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.
23 Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu,
kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.
24 Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu
ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.
25 Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo
amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.
26 Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo,
pamalo pamene aliyense akuwaona;
27 Chifukwa anasiya kumutsata
ndipo sasamaliranso njira zake zonse.
28 Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake,
kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.
29 Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa?
Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe?
Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,
30 kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza,
kuti asatchere anthu misampha.
31 “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti,
‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,
32 ndiphunzitseni zimene sindikuziona
ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’
33 Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira,
pamene inu mukukana kulapa?
Chisankho nʼchanu, osati changa;
tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.
34 “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana,
anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,
35 ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru;
mawu ake ndi opanda fundo.’
36 Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto
chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!
37 Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira;
amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu,
ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.