Beginning
Mawu a Yobu
21 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Mvetserani bwino mawu anga;
ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.
3 Ndiloleni ndiyankhule
ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.
4 “Kodi ine ndikudandaulira munthu?
Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
5 Ndipenyeni ndipo mudabwe;
mugwire dzanja pakamwa.
6 Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri;
thupi langa limanjenjemera.
7 Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo,
amakalamba ndi kusanduka amphamvu?
8 Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo,
zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.
9 Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha;
mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.
10 Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa;
ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.
11 Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa;
makanda awo amavinavina pabwalo.
12 Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze;
amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.
13 Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero
ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.
14 Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’
Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.
15 Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire?
Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?
16 Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo,
koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.
17 “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa?
Nʼkangati kamene tsoka limawagwera?
Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?
18 Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo,
ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?
19 Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’
Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.
20 Mulole kuti adzionere yekha chilango chake,
kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.
21 Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo,
pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?
22 “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru,
poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
23 Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse,
ali pa mtendere ndi pa mpumulo,
24 thupi lake lili lonenepa,
mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.
25 Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima,
wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.
26 Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda
ndipo onse amatuluka mphutsi.
27 “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,
ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.
28 Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti,
matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’
29 Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo?
Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?
30 Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka,
kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?
31 Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo?
Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?
32 Iye amanyamulidwa kupita ku manda
ndipo anthu amachezera pa manda ake.
33 Dothi la ku chigwa limamukomera;
anthu onse amatsatira mtembo wake,
ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.
34 “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo
palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”
Mawu a Elifazi
22 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu?
Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama?
Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
4 “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula,
kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
5 Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu?
Kodi machimo ako si opanda malire?
6 Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa;
umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
7 Sunawapatse madzi anthu otopa,
ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
8 ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake,
munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
9 Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu,
ndipo unapondereza ana amasiye.
10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira,
nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu,
nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?
Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani?
Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona
pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale
imene anthu oyipa ankayendamo?
16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane,
maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni!
Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,
choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera;
anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka
ndipo moto wawononga chuma chawo!’
21 “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere;
ukatero udzaona zabwino.
22 Landira malangizo a pakamwa pake
ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa;
ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
24 ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi,
golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
25 Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako,
siliva wako wamtengowapatali.
26 Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse
ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
27 Udzamupempha ndipo adzakumvera,
ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
28 Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi,
kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
29 Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’
Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
30 Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa,
ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”
Yobu
23 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri;
Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.
3 Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu;
ndikanangopita kumene amakhalako!
4 Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake
ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.
5 Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha,
ndi kulingalira bwino zimene akananena!
6 Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu?
Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.
7 Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake,
ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.
8 “Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko,
ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.
9 Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko
akapita kummwera, sindimuona.
10 Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera;
Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.
11 Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake;
ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.
12 Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake;
ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.
13 “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye?
Iye amachita chilichonse chimene wafuna.
14 Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire,
ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.
15 Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake;
ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.
16 Mulungu walefula mtima wanga;
Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.
17 Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima,
ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.