Beginning
Mawu a Zofari
11 Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,
2 “Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa?
Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?
3 Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku?
Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?
4 Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika
ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’
5 Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula
kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe
6 ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake,
pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri.
Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.
7 “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu?
Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?
8 Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani?
Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani?
9 Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi
ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.
10 “Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende
nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?
11 Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo;
akaona choyipa, kodi sachizindikira?
12 Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru
monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.
13 “Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye
ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,
14 ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako
ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,
15 udzatukula mutu wako wosachita manyazi;
udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.
16 Udzayiwala ndithu zowawa zako,
zidzakhala ngati madzi amene apita kale.
17 Moyo wako udzawala kupambana usana,
ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.
18 Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo;
ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.
19 Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza
ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.
20 Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza,
ndipo adzasowa njira yothawirapo;
chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”
Mawu a Yobu
12 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Ndithudi inuyo ndinu anthu
ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
3 Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu;
ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?
4 “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga,
ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha.
Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
5 Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka.
Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
6 Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere,
ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino,
amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.
7 “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa,
kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
8 kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,
kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
9 Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa
kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
10 Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse,
ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
11 Kodi khutu sindiye limene limamva mawu
monga mmene lilime limalawira chakudya?
12 Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba?
Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?
13 “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu;
uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
14 Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso.
Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
15 Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma;
akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana;
munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
17 Iye amalanda aphungu nzeru zawo
ndipo amapusitsa oweruza.
18 Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo
ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
19 Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo
ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
20 Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika
ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
21 Iye amanyoza anthu otchuka
ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
22 Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima
ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
23 Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso;
amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
24 Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi;
amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
25 Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira;
Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.
13 “Ndaziona ndi maso anga zonsezi,
ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.
2 Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa;
ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
3 Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse
ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.
4 Koma inu mukundipaka mabodza;
nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!
5 Achikhala munangokhala chete nonsenu!
Apo mukanachita zanzeru.
6 Tsopano imvani kudzikanira kwanga;
imvani kudandaula kwa pakamwa panga.
7 Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu?
Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?
8 Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera?
Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?
9 Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa?
Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?
10 Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani
ngati muchita zokondera mseri.
11 Kodi ulemerero wake sungakuopseni?
Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?
12 Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo;
mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.
13 “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule;
tsono zimene zindichitikire zichitike.
14 Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe
ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
15 Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira;
ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
16 Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa
pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
17 Mvetserani mosamala mawu anga;
makutu anu amve zimene ndikunena.
18 Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga,
ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
19 Kodi alipo wina amene angatsutsane nane?
ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.
20 “Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi,
ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:
21 Muchotse dzanja lanu pa ine,
ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.
22 Tsono muyitane ndipo ndidzayankha,
kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.
23 Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati?
Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.
24 Chifukwa chiyani mukundifulatira
ndi kundiyesa ine mdani wanu?
25 Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo?
Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?
26 Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo
ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.
27 Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo.
Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse
poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.
28 “Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa,
ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.