Beginning
Koresi Athandiza Ayuda Kubwerera Kwawo
1 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.
2 Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti,
“ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu. 4 Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5 Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu. 6 Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. 7 Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake. 8 Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
9 Chiwerengerochi chinali motere:
Mabeseni agolide | 30 |
mabeseni asiliva | 1,000 |
a zopereka | 29 |
10 timiphika tagolide | 230 |
timiphika tasiliva | 410 |
ziwiya zina | 1,000. |
11 Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.
Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
2 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2 Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
3 Zidzukulu za Parosi | 2,172 |
4 zidzukulu za Sefatiya | 372 |
5 zidzukulu za Ara | 775 |
6 zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) | 2,812 |
7 zidzukulu za Elamu | 1,254 |
8 zidzukulu za Zatu | 945 |
9 zidzukulu za Zakai | 760 |
10 zidzukulu za Bani | 642 |
11 zidzukulu za Bebai | 623 |
12 zidzukulu za Azigadi | 1,222 |
13 zidzukulu za Adonikamu | 666 |
14 zidzukulu za Bigivai | 2,056 |
15 zidzukulu za Adini | 454 |
16 zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) | 98 |
17 zidzukulu za Bezayi | 323 |
18 zidzukulu za Yora | 112 |
19 zidzukulu za Hasumu | 223 |
20 zidzukulu za Gibari | 95. |
21 Anthu a ku Betelehemu | 123 |
22 Anthu aamuna a ku Netofa | 56 |
23 Anthu aamuna a ku Anatoti | 128 |
24 Anthu aamuna a ku Azimaveti | 42 |
25 Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti | 743 |
26 Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba | 621 |
27 Anthu aamuna a ku Mikimasi | 122 |
28 Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai | 223 |
29 Anthu aamuna a ku Nebo | 52 |
30 Anthu aamuna a ku Magaibisi | 156 |
31 Anthu aamuna a ku Elamu wina | 1,254 |
32 Anthu aamuna a ku Harimu | 320 |
33 Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono | 725 |
34 Anthu aamuna a ku Yeriko | 345 |
35 Anthu aamuna a ku Sena | 3,630. |
36 Ansembe anali awa:
Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) | 973 |
37 Zidzukulu za Imeri | 1,052 |
38 Zidzukulu za Pasuri | 1,247 |
39 Zidzukulu za Harimu | 1,017. |
40 Alevi anali awa:
Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) | 74. |
41 Anthu oyimba nyimbo anali awa:
Zidzukulu za Asafu | 128. |
42 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai | 139. |
43 Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za |
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti, |
44 zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni, |
45 zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu, |
46 zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani, |
47 zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya, |
48 zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu, |
49 zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai, |
50 zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu, |
51 zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri, |
52 zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa, |
53 zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema, |
54 zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa. |
55 Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:
Zidzukulu za | |
Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda, | |
56 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli, | |
57 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu, | |
zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami. | |
58 Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali | 392. |
59 Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
60 Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali | 652. |
61 Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
Zidzukulu za |
Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.) |
62 Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63 Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65 kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66 Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67 ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68 Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69 Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70 Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
Kumangidwanso kwa Guwa la Nsembe
3 Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi. 2 Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja. 3 Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo. 4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa. 5 Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova. 6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
Kumangidwanso kwa Nyumba ya Mulungu
7 Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
8 Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova. 9 Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
10 Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli. 11 Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi:
“Yehova ndi wabwino;
chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.”
Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa. 12 Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala. 13 Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.