Beginning
Ahazi Mfumu ya Yuda
28 Ahazi anali ndi zaka makumi awiri pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Iye sanachite zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide kholo lake. 2 Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo anawumbanso mafano a chipembedzo cha Abaala. 3 Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. 4 Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzerapo mafano, pamwamba pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu.
5 Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko.
Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri. 6 Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo. 7 Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu. 8 Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya.
9 Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba. 10 Ndipo tsopano mukufuna kuti amuna ndi akazi a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale akapolo anu. 11 Tsono mvereni! Abwezeni abale anu amene mwawagwira ukapolo, pakuti mkwiyo wa Yehova uli pa inu.”
12 Tsono atsogoleri ena a ku Efereimu, Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilayi anatsutsana nawo amene ankachokera ku nkhondo kuja. 13 Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.”
14 Kotero asilikali aja anawasiya akapolowo pamodzi ndi katundu amene analanda ku nkhondo pamaso pa akuluakulu ndi gulu lonse la anthu. 15 Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya.
16 Pa nthawi imeneyo mfumu Ahazi inatumiza mawu kwa mfumu ya ku Asiriya kupempha chithandizo. 17 Ankhondo a ku Edomu anabweranso ndi kuthira nkhondo Yuda ndi kugwira akapolo. 18 Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 19 Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova. 20 Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera kwa iye, ndipo anabweretsa mavuto mʼmalo momuthandiza. 21 Ahazi anatenga zinthu zochokera mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yaufumu ndi kwa atsogoleri ndipo anazipereka kwa mfumu ya ku Asiriya, koma zimenezo sizinamuthandize.
22 Pa nthawi yake yamavutoyi mfumu Ahazi inapitirira kukhalabe yosakhulupirika pamaso pa Yehova. 23 Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.
24 Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu. 25 Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake.
26 Zochitika zina pa ulamuliro wake ndi machitidwe ake onse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 27 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Mfumu Hezekiya Ayeretsa Nyumba ya Mulungu
29 Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya. 2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.
3 Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza. 4 Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa 5 ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika. 6 Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira. 7 Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli. 8 Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino. 9 Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo. 10 Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere. 11 Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”
12 Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito:
Kuchokera ku banja la Kohati,
Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya;
kuchokera ku banja la Merari,
Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli;
kuchokera ku banja la Geresoni,
Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;
13 kuchokera kwa zidzukulu za Elizafani,
Simiri ndi Yeiyeli;
kuchokera kwa zidzukulu za Asafu,
Zekariya ndi Mataniya;
14 kuchokera kwa zidzukulu za Hemani,
Yehieli ndi Simei;
kuchokera kwa zidzukulu za Yedutuni,
Semaya ndi Uzieli.
15 Atasonkhanitsa abale awo ndi kudziyeretsa, iwo anapita kukayeretsa Nyumba ya Yehova, monga inalamulira mfumu, potsatira mawu a Yehova. 16 Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni. 17 Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.
18 Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse. 19 Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”
20 Mmamawa tsiku linalo, mfumu Hezekiya inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu a mu mzindawo ndipo inapita ku Nyumba ya Yehova. 21 Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova. 22 Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe. 23 Mbuzi zoperekedwa chifukwa cha tchimo zija zinabweretsedwa pamaso pa mfumu ndi anthu onse, ndipo anasanjika manja awo pa izo. 24 Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.
25 Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri. 26 Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.
27 Hezekiya analamulira kuti apereke nsembe zopsereza pa guwa. Pamene amayamba kupereka nsembezo, kuyimbira Yehova kunayambikanso, pamodzi ndi malipenga ndi zipangizo zoyimbira za Davide mfumu ya Israeli. 28 Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.
29 Zopereka zitatha, mfumu ndi wina aliyense amene anali naye anagwada pansi ndi kulambira. 30 Mfumu Hezekiya ndi akuluakulu ake analamulira Alevi kuti atamande Yehova potsata mawu a Davide ndi mlosi Asafu. Kotero anayimba nyimbo zamatamando mokondwera ndipo anaweramitsa mitu yawo ndi kulambira.
31 Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.
32 Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova. 33 Ziweto zimene zinapatulidwa kukhala nsembe zinalipo ngʼombe zazimuna 600, nkhosa ndi mbuzi 3,000. 34 Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe. 35 Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza.
Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso. 36 Hezekiya ndi anthu onse anakondwera pa zimene Mulungu anachitira anthu ake, chifukwa zinachita mwamsangamsanga.
Hezekiya Achita Chikondwerero cha Paska
30 Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. 2 Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri. 3 Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu. 4 Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse. 5 Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.
6 Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti,
“Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya. 7 Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu. 8 Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni. 9 Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye.”
10 Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe. 11 Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu. 12 Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.
13 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri. 14 Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.
15 Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova. 16 Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi. 17 Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova. 18 Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, “Yehova wabwino, khululukirani aliyense 19 amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika.” 20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.
21 Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.
22 Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.
23 Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala. 24 Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa. 25 Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda. 26 Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu. 27 Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.
31 Zonse zitatha, Aisraeli onse amene anali kumeneko anapita ku mizinda ya ku Yuda, nakaphwanya miyala yachipembedzo ndi kudula mitengo ya mafano a Asera. Iwo anakawononga malo achipembedzo ndi maguwa ansembe amene anali mʼdziko lonse la Yuda, Benjamini, Efereimu ndi Manase. Atawononga zonsezi, Aisraeli anabwerera ku mizinda yawo ndi ku malo awo.
Zopereka ku Ntchito ya Chipembedzo
2 Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova. 3 Kuchokera pa chuma chake, mfumu inapereka nsembe zopsereza za mmawa ndi madzulo ndiponso nsembe zopsereza za pa Chikondwerero cha Masabata, Chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndipo inakhazikitsa zikondwerero monga zinalembedwera mʼmalamulo a Yehova. 4 Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova. 5 Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse. 6 Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu. 7 Anayamba kuchita izi mwezi wachitatu ndipo anatsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. 8 Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli.
9 Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyi; 10 ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.”
11 Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika. 12 Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake. 13 Yehieli, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali oyangʼanira motsogozedwa ndi Konaniya ndi Simei, mʼbale wake. Iwowa anasankhidwa ndi mfumu Hezekiya ndi Azariya mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu.
14 Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika. 15 Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe.
16 Kuwonjezera apa, amagawira ana aamuna a zaka zitatu kapena kupitirira amene mayina awo anali mʼmbiri ya mibado yawo, amene adzalowe mʼNyumba ya Yehova kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku za magulu awo, molingana ndi udindo ndi magulu awo. 17 Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo. 18 Iwo anaphatikizanso ana onse aangʼono, akazi ndiponso ana aamuna ndi ana aakazi a gulu lonse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado yawo iyi, pakuti anakhulupirika pa kudzipatula okha.
19 Kunena za ansembe, zidzukulu za Aaroni, amene amakhala mʼminda yozungulira mizinda yawo kapena mzinda wina uliwonse, anthu anasankhidwa mowatchula mayina kuti azipereka magawo kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pawo ndiponso kwa onse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado ya Alevi.
20 Izi ndi zimene Hezekiya anachita mu Yuda monse, kuchita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21 Pa chilichonse chimene anachita pa ntchito ya Nyumba ya Mulungu ndi pa kumvera malangizo ndi malamulo, iye anafunafuna Mulungu wake ndipo anagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Ndipo zinthu zimamuyendera bwino.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.