Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mbiri 21-24

21 Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli. Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.

Yehoramu Mfumu ya Yuda

Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli. Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.

Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku. 10 Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda.

Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake. 11 Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.

12 Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti,

“Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda. 13 Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo. 14 Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu. 15 Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’ ”

16 Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi. 17 Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.

18 Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika. 19 Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.

20 Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.

Ahaziya Mfumu ya Yuda

22 Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.

Ahaziya anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Dzina la amayi ake linali Ataliya, chidzukulu cha Omuri.

Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake. Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu, kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu.

Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa.

Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu. Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu anapeza atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya amene amatumikira Ahaziya, ndipo anawapha. Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu.

Ataliya ndi Yowasi

10 Ataliya, amayi ake a Ahaziya, ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakapha onse a banja laufumu la Yuda. 11 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, momuba ndi kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene amati aphedwe ndipo anamuyika iye ndi mlezi wake mʼchipinda chogona. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa wansembe Yehoyada, yemwe anali mlongo wake wa Ahaziya anamubisa mwanayo kuti Ataliya asamuphe. 12 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi iwo mu Nyumba ya Mulungu kwa zaka zisanu ndi chimodzi muulamuliro wa Ataliya.

23 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu, msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu.

Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide. Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo, ndi limodzi la magawo atatu likakhale ku nyumba yaufumu ndipo limodzi la magawo atatu likakhale ku chipata cha Maziko ndipo anthu ena onse akakhale mʼmabwalo a Nyumba ya Yehova. Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula. Alevi akhale mozungulira mfumu, munthu aliyense ali ndi chida chake mʼmanja. Aliyense amene alowe mʼNyumba ya Mulungu ayenera kuphedwa. Mukhale nayo pafupi mfumu kulikonse kumene izipita.”

Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite. Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu. 10 Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu.

11 Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”

12 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga ndi kukondwerera mfumu, anapita ku Nyumba ya Yehova komwe kunali anthuko. 13 Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”

14 Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,” 15 choncho anamugwira pamene amafika pa chipata cha Kavalo pa bwalo la nyumba yaufumu, ndipo anamuphera pamenepo.

16 Tsono Yehoyada anachita pangano, iye mwini ndi anthu onse ndiponso mfumu kuti adzakhala anthu a Yehova. 17 Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo.

18 Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira. 19 Ndipo anayika alonda a pa khomo pa zipata za Nyumba ya Yehova kuti aliyense amene ndi odetsedwa asalowe.

20 Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka, 21 ndipo anthu onse a mʼderali anakondwera. Tsono mu mzinda munali bata chifukwa Ataliya anaphedwa ndi lupanga.

Yowasi Akonzanso Nyumba ya Mulungu

24 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. Dzina la amayi ake linali Zibiya wa ku Beeriseba. Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova nthawi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada. Yehoyada anamupezera iye akazi awiri, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

Patapita nthawi Yowasi anatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Yehova. Iye anayitanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi ndipo anawawuza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda ndi kukasonkhetsa ndalama za pa chaka kwa Aisraeli onse zokonzera Nyumba ya Mulungu wanu. Chitani zimenezi tsopano.” Koma Alevi sanachite zimenezi mwachangu.

Choncho mfumu inayitanitsa Yehoyada, mkulu wa ansembe ndipo inati kwa iye, “Kodi nʼchifukwa chiyani simunawuze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi Yerusalemu, msonkho umene anakhazikitsa Mose mtumiki wa Yehova ndiponso gulu lonse la Aisraeli mu tenti yaumboni?”

Ana a mkazi woyipa, Ataliya, anathyola chitseko cha Nyumba ya Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zopatulika popembedza Baala.

Mfumu italamulira, bokosi linapangidwa ndipo linayikidwa panja pa chipata cha Nyumba ya Yehova. Ndipo analengeza kwa anthu a mu Yuda ndi mu Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu analamulira Aisraeli mʼchipululu. 10 Akuluakulu onse ndi anthu onse anabweretsa zopereka zawo mokondwera ndipo anaziponya mʼbokosi mpaka linadzaza. 11 Nthawi ina iliyonse imene Alevi abweretsa bokosilo kwa akuluakulu a mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi waufumu ndi nduna yayikulu ya mkulu wa ansembe amabwera ndi kuchotsa ndalama mʼbokosi muja ndipo amalitenga kukaliyika pamalo pake. Iwo amachita izi nthawi ndi nthawi ndipo anapeza ndalama zambiri. 12 Mfumu pamodzi ndi Yehoyada anapereka ndalamazo kwa anthu oyangʼanira ntchito ku Nyumba ya Yehova. Analemba ntchito amisiri a miyala ndi a matabwa kuti akonzenso Nyumba ya Yehova. Analembanso ntchito amisiri a zitsulo ndi mkuwa kuti akonze Nyumba ya Mulungu.

13 Anthu amene ankagwira ntchito anali odziwa bwino, ndipo ntchitoyo inagwiridwa bwino ndi manja awo. Iwo anamanganso Nyumba ya Mulungu motsatira mapangidwe ake oyamba ndipo anayilimbitsa. 14 Atamaliza, iwo anabweretsa ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, ndipo anazigwiritsira ntchito popangira zida za mʼNyumba ya Yehova: ziwiya zogwiritsa ntchito potumikira ndi popereka nsembe zopsereza, komanso mbale ndi ziwiya zagolide ndi siliva. Nthawi yonse ya moyo wa Yehoyada, nsembe zopsereza zinkaperekedwa mosalekeza mʼNyumba ya Yehova.

15 Tsono Yehoyada anakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Pambuyo pake iye anamwalira ali ndi zaka 130. 16 Iyeyo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu mu mzinda wa Davide chifukwa cha zabwino zimene anachita mu Israeli, kuchitira Mulungu ndi Nyumba yake.

Kuyipa kwa Yowasi

17 Atamwalira Yehoyada, akuluakulu a Yuda anabwera kudzapereka ulemu kwa mfumu, ndipo mfumu inawamvera. 18 Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu. 19 Ngakhale Yehova anatumiza aneneri kwa anthuwo kuti awabweze kwa Iye, ngakhale aneneri ananenera mowatsutsa, anthuwo sanamvere.

20 Kenaka Mzimu wa Mulungu unabwera pa Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anayimirira pamaso pa anthu ndipo anati, “Zimene Mulungu akunena ndi Izi: ‘Chifukwa chiyani simukumvera Malamulo a Yehova? Simudzapindula. Chifukwa mwasiya Yehova, Iyenso wakusiyani.’ ”

21 Koma anthuwo anamuchitira chiwembu molamulidwa ndi mfumu ndipo anamugenda miyala ndi kumupha mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu. 22 Mfumu Yowasi sinakumbukire zabwino zimene Yehoyada abambo ake a Zekariya anamuchitira, koma anapha mwana wake. Pamene amafa, iye ananena kuti, “Yehova aone zimenezi ndipo abwezere chilango.”

23 Pakutha kwa chaka, gulu lankhondo la Aramu linadzamenyana ndi Yowasi. Linalowa mu Yuda ndi mu Yerusalemu ndi kupha atsogoleri onse a anthu. Zonse zimene analanda anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko. 24 Ngakhale kuti gulu lankhondo la Aramu linabwera ndi anthu ochepa okha, Yehova anapereka mʼmanja mwawo gulu lalikulu lankhondo. Chifukwa Yuda anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, chiweruzo chinachitika pa Yowasi. 25 Pamene Aaramu amachoka, anasiya Yowasi atavulazidwa kwambiri. Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu chifukwa anapha mwana wa wansembe Yehoyada, ndipo anamupha ali pa bedi pake. Choncho anafa ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati manda a mafumu.

26 Iwo amene anamuchitira chiwembu anali Zabadi mwana wa Simeati, mkazi wa ku Amoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simiriti, mkazi wa ku Mowabu. 27 Za ana ake aamuna, uneneri wonena za iye, mbiri ya kumanganso Nyumba ya Mulungu, zalembedwa mʼbuku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.