Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 22-24

22 Ndipo Davide anati, “Nyumba ya Yehova Mulungu idzakhala pano, ndiponso guwa lansembe zopsereza za Israeli.”

Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu

Choncho Davide analamula kuti asonkhanitse alendo onse amene amakhala mu Israeli ndipo kuchokera pakati pawo anasankha amisiri a miyala kuti aseme miyala yomangira nyumba ya Mulungu. Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza. Iye anaperekanso mitengo yambiri ya mkungudza, yosawerengeka, pakuti anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo anabweretsa yambiri kwa Davide.

Davide anati, “Mwana wanga Solomoni ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Koma nyumba yomwe timangire Yehova iyenera kukhala yaulemerero, yotchuka ndi yokongola pamaso pa anthu a mitundu yonse. Choncho ndikonzekeratu zambiri.” Motero Davide anayikonzekera kwambiri asanamwalire.

Tsono iye anayitana Solomoni mwana wake ndipo anamulamula kuti adzamangire nyumba Yehova Mulungu wa Israeli. Davide anati kwa Solomoni, “Mwana wanga, ine ndinali ndi maganizo oti ndimangire nyumba Dzina la Yehova Mulungu wanga. Koma Yehova anandiyankhula kuti, ‘Iwe wapha anthu ambiri ndiponso wachita nkhondo zambiri. Sumangira dzina langa nyumba chifukwa wapha anthu ambiri pa dziko lapansi pamaso panga. Koma udzabala mwana wamwamuna amene adzakhala munthu wamtendere ndi wabata ndipo ndidzamupatsa mpumulo kuchokera kwa adani ake onse a mbali zonse. Dzina lake adzatchedwa Solomoni ndipo Ine ndidzapereka mtendere ndi bata kwa Israeli pa nthawi ya ulamuliro wake. 10 Iye ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu mʼdziko la Israeli mpaka muyaya.’ ”

11 “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo upambane ndi kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga momwe Iye ananenera kuti udzatero. 12 Yehova akupatse nzeru ndi kumvetsetsa pamene Iye adzakuyika kukhala wolamulira Israeli, kuti udzasunge malamulo a Yehova Mulungu wako. 13 Ndipo udzapambana ngati udzamvera mosamala malangizo ndi malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kudzera mwa Mose. Khala wamphamvu ndi wolimba mtima. Usachite mantha kapena kutaya mtima.

14 “Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi. 15 Iwe uli ndi antchito ambiri: osema miyala, amisiri a miyala, ndi amisiri a matabwa, komanso anthu ambiri aluso la ntchito zosiyanasiyana, 16 zagolide ndi zasiliva, zamkuwa, zazitsulo, amisiri osawerengeka. Tsopano yamba ntchito, ndipo Yehova akhale nawe.”

17 Tsono Davide analamula atsogoleri onse a Israeli kuti athandize Solomoni mwana wake. 18 Iye anawawuza kuti, “Kodi Yehova Mulungu, sali nanu? Ndipo Iye siwakupatsani mpumulo mbali zonse? Pakuti Iyeyo wapereka eni nthaka kwa inu ndipo dziko lili pa ulamuliro wa Yehova ndi anthu ake. 19 Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.”

Fuko la Levi

23 Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.

Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi. Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000. Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza. Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”

Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

Banja la Geresoni

Ana a Geresoni:

Ladani ndi Simei.

Ana a Ladani:

Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.

Ana a Simei:

Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.

Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.

10 Ndipo ana a Simei anali:

Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.

Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.

11 Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.

Banja la Kohati

12 Ana a Kohati:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.

13 Ana a Amramu:

Aaroni ndi Mose.

Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya. 14 Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.

15 Ana a Mose:

Geresomu ndi Eliezara.

16 Zidzukulu za Geresomu:

Mtsogoleri anali Subaeli.

17 Zidzukulu za Eliezara:

Mtsogoleri anali Rehabiya.

Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.

18 Ana a Izihari:

Mtsogoleri anali Selomiti.

19 Ana a Hebroni:

Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.

20 Ana a Uzieli:

Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.

Banja la Merari

21 Ana a Merari:

Mahili ndi Musi.

Ana a Mahili:

Eliezara ndi Kisi.

22 Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.

23 Ana a Musi:

Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.

24 Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova. 25 Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya, 26 sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.” 27 Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.

28 Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu. 29 Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake. 30 Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo, 31 ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.

32 Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.

Magulu a Ansembe

24 Magulu a ana a Aaroni anali awa:

Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.

Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.

Maere woyamba anagwera Yehoyaribu,

achiwiri anagwera Yedaya,

achitatu anagwera Harimu,

achinayi anagwera Seorimu,

achisanu anagwera Malikiya,

achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,

10 achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi,

achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,

11 achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa,

a khumi anagwera Sekaniya,

12 a 11 anagwera Eliyasibu,

a 12 anagwera Yakimu,

13 a 13 anagwera Hupa,

a 14 anagwera Yesebeabu,

14 a 15 anagwera Biliga,

a 16 anagwera Imeri,

15 a 17 anagwera Heziri,

a 18 anagwera Hapizezi,

16 a 19 anagwera Petahiya,

a 20 anagwera Ezekieli,

17 a 21 anagwera Yakini,

a 22 anagwera Gamuli,

18 a 23 anagwera Delaya,

ndipo a 24 anagwera Maaziya.

19 Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.

Alevi Ena Onse

20 Za zidzukulu zina zonse za Levi:

Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli;

kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.

21 Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake:

Mtsogoleri anali Isiya.

22 Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti;

kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.

23 Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.

24 Mwana wa Uzieli: Mika;

kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.

25 Mʼbale wa Mika: Isiya;

kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.

26 Ana a Merari: Mahili ndi Musi.

Mwana wa Yaaziya: Beno.

27 Ana a Merari:

Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.

28 Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.

29 Kuchokera kwa Kisi:

Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.

30 Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti.

Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. 31 Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.