Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 3-5

Ana a Davide

Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa:

Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli;

wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli;

wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;

wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;

wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali;

wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila.

Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi.

Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33, ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa:

Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli. Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti, Noga, Nefegi, Yafiya, Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi. Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.

Mafumu a Yuda

10 Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu,

Rehabiamu anabereka Abiya,

Abiya anabereka Asa,

Asa anabereka Yehosafati,

11 Yehosafati anabereka Yehoramu,

Yehoramu anabereka Ahaziya,

Ahaziya anabereka Yowasi,

12 Yowasi anabereka Amaziya,

Amaziya anabereka Azariya,

Azariya anabereka Yotamu,

13 Yotamu anabereka Ahazi,

Ahazi anabereka Hezekiya,

Hezekiya anabereka Manase,

14 Manase anabereka Amoni,

Amoni anabereka Yosiya.

15 Ana a Yosiya anali awa:

Yohanani mwana wake woyamba,

Yehoyakimu mwana wake wachiwiri,

Zedekiya mwana wake wachitatu,

Salumu mwana wake wachinayi.

16 Ana a Yehoyakimu:

Yekoniya

ndi Zedekiya mwana wake.

Mayina a Mafumu Utatha Ukapolo

17 Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi:

mwana wake Silatieli, 18 Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya.

19 Ana a Pedaya anali awa:

Zerubabeli ndi Simei.

Ana a Zerubabeli anali awa:

Mesulamu ndi Hananiya.

Mlongo wawo anali Selomiti.

20 Panalinso ana ena asanu awa:

Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi.

21 Zidzukulu za Hananiya zinali izi:

Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya.

22 Zidzukulu za Sekaniya zinali izi:

Semaya ndi ana ake:

Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi.

23 Ana a Neariya anali awa:

Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu.

24 Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu,

Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri.

Mabanja Ena a Yuda

Ana a Yuda anali awa:

Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali.

Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati.

Ana a Etamu anali awa:

Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi. Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa.

Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu.

Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.

Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara.

Ana a Hela:

Zereti, Zohari, Etinani, ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi.

Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.” 10 Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.

11 Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni. 12 Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka.

13 Ana a Kenazi anali awa:

Otanieli ndi Seraya.

Ana a Otanieli anali awa:

Hatati ndi Meonotai. 14 Meonotai anabereka Ofura.

Seraya anabereka Yowabu,

amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri.

15 Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa:

Iru, Ela ndi Naama.

Mwana wa Ela anali

Kenazi.

16 Ana a Yehaleleli anali awa:

Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli.

17 Ana a Ezara anali awa:

Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa. 18 (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.

19 Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa:

abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.

20 Ana a Simeoni anali awa:

Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni.

Ana a Isi anali awa:

Zoheti ndi Beni-Zoheti.

21 Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa:

Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya, 22 Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale). 23 Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.

Simeoni

24 Ana a Simeoni anali awa:

Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;

25 Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.

26 Zidzukulu za Misima zinali izi:

Hamueli, Zakuri ndi Simei.

27 Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda. 28 Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali, 29 Biliha, Ezemu, Toladi, 30 Betueli, Horima, Zikilagi, 31 Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide. 32 Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu 33 ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.

34 Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35 Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli, 36 komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37 ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.

38 Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri 39 ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo. 40 Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.

41 Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. 42 Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri. 43 Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.

Fuko la Rubeni

Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa:

Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.

Ana a Yoweli anali awa:

Semaya, Gogi,

Simei, Mika,

Reaya, Baala,

ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.

Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa:

Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi.

10 Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi.

Fuko la Gadi

11 Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka:

12 Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati.

13 Abale awo mwa mabanja awo anali awa:

Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri.

14 Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi.

15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo.

16 Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera.

17 Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.

18 Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. 19 Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. 20 Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. 21 Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, 22 enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo.

Theka la Fuko la Manase

23 Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri.

24 Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. 25 Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. 26 Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.