Beginning
Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu
Mpaka pa Ana a Nowa
1 Adamu, Seti, Enosi 2 Kenani, Mahalaleli, Yaredi, 3 Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.
4 Ana a Nowa,
Semu, Hamu ndi Yafeti.
Fuko la Yafeti
5 Ana aamuna a Yafeti anali:
Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
6 Ana aamuna a Gomeri anali:
Asikenazi, Rifati ndi Togarima
7 Ana aamuna a Yavani anali:
Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
Fuko la Hamu
8 Ana aamuna a Hamu anali:
Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani
9 Ana aamuna a Kusi anali:
Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka
Ana aamuna a Raama anali:
Seba ndi Dedani.
10 Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu
kwambiri pa dziko lapansi.
11 Igupto ndiye kholo la
Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 12 Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.
13 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni,
ndipo anaberekanso Ahiti, 14 Ayebusi, Aamori, Agirigasi 15 Ahivi, Aariki, Asini 16 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
Fuko la Semu
17 Ana aamuna a Semu anali:
Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
Ana aamuna a Aramu anali:
Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
18 Aripakisadi anabereka Sela
ndipo Selayo anabereka Eberi:
19 Eberi anabereka ana aamuna awiri:
wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
20 Yokitani anabereka
Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 21 Hadoramu, Uzali, Dikila 22 Obali, Abimaeli, Seba, 23 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
24 Semu, Aripakisadi, Sela
25 Eberi, Pelegi, Reu
26 Serugi, Nahori, Tera
27 ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).
Banja la Abrahamu
28 Ana a Abrahamu ndi awa:
Isake ndi Ismaeli.
Zidzukulu za Hagara
29 Zidzukulu zake zinali izi:
Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 30 Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, 31 Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.
Zidzukulu za Ketura
32 Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa:
Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.
Ana a Yokisani ndi awa:
Seba ndi Dedani
33 Ana aamuna a Midiyani anali,
Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.
Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
Zidzukulu za Sara
34 Abrahamu anabereka Isake.
Ana a Isake anali awa:
Esau ndi Israeli.
Ana a Esau
35 Ana aamuna a Esau anali awa:
Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.
36 Ana a Elifazi anali awa:
Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi:
Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.
37 Ana a Reueli anali awa:
Nahati, Zera, Sama ndi Miza.
Anthu a ku Seiri ku Edomu
38 Ana a Seiri anali awa:
Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.
39 Ana aamuna a Lotani anali awa:
Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
40 Ana aamuna a Sobala anali awa:
Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
Ana aamuna a Zibeoni anali awa:
Ayiwa ndi Ana.
41 Mwana wa Ana anali
Disoni.
Ana a Disoni anali awa:
Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani
42 Ana aamuna a Ezeri anali awa:
Bilihani, Zaavani ndi Yaakani.
Ana aamuna a Disani anali awa:
Uzi ndi Arani.
Mafumu a ku Edomu
43 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
44 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
45 Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.
46 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
47 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.
48 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.
49 Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
50 Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. 51 Hadadi anamwaliranso.
Mafumu a ku Edomu anali:
Timna, Aliva, Yeteti, 52 Oholibama, Ela, Pinoni, 53 Kenazi, Temani, Mibezari, 54 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.
Ana a Israeli
2 Ana a Israeli anali awa:
Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, 2 Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.
Yuda Mpaka pa Ana a Hezironi
Ana a Hezironi
3 Ana a Yuda anali awa:
Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha. 4 Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
5 Ana a Perezi anali awa:
Hezironi ndi Hamuli.
6 Ana a Zera anali awa:
Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
7 Mwana wa Karimi anali
Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
8 Mwana wa Etani anali
Azariya.
9 Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali:
Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.
Kuchokera kwa Ramu Mwana wa Hezironi
10 Ramu anabereka
Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda. 11 Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi, 12 Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
13 Yese anabereka
Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea, 14 wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15 wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide. 16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli. 17 Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.
Kalebe Mwana wa Hezironi
18 Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. 19 Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri. 20 Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
21 Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu. 22 Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi. 23 (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
24 Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.
Yerahimeeli Mwana wa Hezironi
25 Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali:
Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya. 26 Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
27 Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa:
Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28 Ana a Onamu anali awa:
Shamai ndi Yada.
Ana a Shamai anali awa:
Nadabu ndi Abisuri.
29 Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
30 Ana a Nadabu anali awa:
Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31 Ana a Apaimu anali awa:
Isi, amene anabereka Sesani.
Sesani anabereka Ahilai.
32 Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa:
Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
33 Ana a Yonatani anali awa:
Peleti ndi Zaza.
Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
34 Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha.
Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha. 35 Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
36 Atayi anali abambo ake a Natani,
Natani anali abambo ake a Zabadi,
37 Zabadi anali abambo a Efilali,
Efilali anali abambo a Obedi,
38 Obedi anali abambo a Yehu,
Yehu anali abambo a Azariya,
39 Azariya anali abambo a Helezi,
Helezi anali abambo a Eleasa,
40 Eleasa anali abambo ake a Sisimai,
Sisimai anali abambo a Salumu,
41 Salumu anali abambo a Yekamiya,
Yekamiya anali abambo a Elisama.
Mabanja a Kalebe
42 Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa:
Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
43 Ana a Hebroni anali awa:
Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. 44 Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai. 45 Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
46 Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
47 Ana a Yahidai anali awa:
Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
48 Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana. 49 Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. 50 Izi zinali zidzukulu za Kalebe.
Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa:
Sobala abambo a Kiriati Yearimu, 51 Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
52 Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi:
Harowe, theka la banja la Manahati, 53 ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
54 Zidzukulu za Salima zinali izi:
Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori, 55 ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.