Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 10-11

Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ibwera Kudzacheza ndi Solomoni

10 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga, chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.

Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva. Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”

10 Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.

11 (Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola. 12 Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).

13 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.

Chuma ndi Ulemerero wa Solomoni

14 Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000, 15 osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.

16 Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka. 17 Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.

18 Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri. 19 Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse. 20 Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse. 21 Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni. 22 Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.

23 Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi. 24 Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. 25 Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu.

26 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu. 27 Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri. 28 Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe. 29 Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.

Akazi a Solomoni

11 Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake.

Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.

Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse. 10 Ngakhale kuti Yehova anamuletsa Solomoni kutsatira milungu ina, iyeyo sanamvere lamulo la Yehova. 11 Pamenepo Yehova anati kwa Solomoni, “Popeza mtima wako ndi wotere ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo anga amene ndinakuwuza, ndithudi, Ine ndidzawugawa ufumuwu kuwuchotsa kwa iwe ndi kuwupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. 12 Koma chifukwa cha Davide abambo ako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo. Ndidzawugawa mʼdzanja la mwana wako. 13 Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.”

Adani a Solomoni

14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, Hadadi Mwedomu, wochokera ku banja laufumu ku Edomu. 15 Kale pamene Davide ankachita nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wa ankhondo, amene anapita kukakwirira Aisraeli akufa, anakantha amuna onse ku Edomu. 16 Yowabu ndi Aisraeli onse anakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi mpaka anawononga amuna onse a ku Edomu. 17 Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake. 18 Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.

19 Farao anamukomera mtima Hadadi ndipo anamupatsa mkazi amene anali mngʼono wake wa Mfumukazi Tahipenesi. 20 Mngʼono wake wa Tahipenesi anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Genubati, amene analeredwa mʼnyumba yaufumu ndi Tahipenesi. Genubatiyo ankakhala limodzi ndi ana a Farao.

21 Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.”

22 Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?”

Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!”

23 Ndipo Mulungu anawutsira Solomoni mdani wina, Rezoni mwana wa Eliada, amene anali atathawa mbuye wake, Hadadezeri mfumu ya ku Zoba. 24 Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira. 25 Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli.

Yeroboamu Awukira Solomoni

26 Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye.

27 Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake. 28 Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe.

29 Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko, 30 ndipo Ahiya anagwira mwinjiro watsopano umene anavala ndi kuwungʼamba zidutswa 12. 31 Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 32 Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha. 33 Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.

34 “ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga. 35 Ndidzalanda ufumu mʼdzanja la mwana wake ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 36 Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa. 37 Koma kunena za iwe, ndidzakutenga ndipo udzalamulira chilichonse chimene mtima wako ukukhumba; udzakhala mfumu ya Israeli. 38 Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli. 39 Ine ndidzalanga zidzukulu za Davide chifukwa cha zimenezi, koma osati kwamuyaya.’ ”

40 Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.

Kumwalira kwa Solomoni

41 Ntchito zina za Solomoni, zonse zomwe anachita komanso za nzeru zake, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya Solomoni? 42 Solomoni analamulira Aisraeli onse mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. 43 Ndipo anagona ndi makolo ake nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo ake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.