Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 8-12

Kupambana kwa Davide pa Nkhondo

Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndi kuwapambana ndipo analanda Metegi Ama kuchoka mʼmanja mwa Afilistiwo.

Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho.

Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.

Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. Mfumu Davide inatenga mkuwa wambiri kuchokera ku Beta ndi Berotai, mizinda ya Hadadezeri.

Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri, 10 anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.

11 Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa: 12 Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Iye anaperekanso zolanda ku nkhondo zochokera kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba.

13 Ndipo Davide anatchuka atabwera kokakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.

14 Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

Akuluakulu a Davide

15 Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 16 Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika. 17 Zadoki mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Seraya anali mlembi; 18 Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti; ndipo ana a Davide anali ansembe.

Davide ndi Mefiboseti

Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?”

Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?”

Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”

Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?”

Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”

Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?”

Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.”

Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli.

Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye.

Davide anati, “Mefiboseti!”

Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”

Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”

Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”

Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake. 10 Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).

11 Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.

12 Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13 Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.

Davide agonjetsa Aamoni

10 Patapita nthawi, mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni analowa ufumu mʼmalo mwake. Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.

Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni, atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anameta munthu aliyense mbali imodzi ya ndevu zake, ndi kudula zovala zake pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera, ndipo anawabweza kwawo.

Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”

Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.

Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene Aaramu a ku Aramu-Zoba ndi Rehobu ndi ankhondo a ku Tobu ndi Maaka anali kwa wokha ku malo wopanda mitengo.

Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 10 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 11 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 12 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”

13 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 14 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.

15 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anasonkhananso. 16 Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri.

17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. 18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo. 19 Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo.

Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.

Davide ndi Batiseba

11 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.

Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”

Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.

10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”

11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”

12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. 13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.

14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. 15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.”

16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. 17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.

18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. 19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, 20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? 21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ”

22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. 23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. 24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”

25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”

26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. 27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.

Natani Adzudzula Davide

12 Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.

“Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”

Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”

Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli. Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri. Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. 10 Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’

11 “Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. 12 Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ”

13 Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.”

Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi. 14 Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.”

15 Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. 16 Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse. 17 Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo.

18 Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.”

19 Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?”

Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”

20 Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya.

21 Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!”

22 Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’ 23 Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.”

24 Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye. 25 Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya.

26 Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. 27 Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. 28 Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.”

29 Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. 30 Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 31 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.