Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 4-8

Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse.

Afilisti Alanda Bokosi la Chipangano

Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo. Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.”

Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu.

Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka. Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?”

Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako, Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe. Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu. Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ”

10 Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. 11 Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa.

Imfa ya Eli

12 Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni. 13 Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira.

14 Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?”

Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera. 15 Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona. 16 Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.”

Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?”

17 Iye anayankha kuti, “Aisraeli athawa pamaso pa Afilisti. Anthu ambirimbiri aphedwa. Ana anunso Hofini ndi Finehasi aphedwa. Bokosi la Mulungu nalonso lalandidwa.”

18 Atangotchula Bokosi la Yehova, Eli anagwa chagada, kuchoka pa mpando wake umene unali mʼmbali mwa chitseko cha mpanda. Khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali okalamba ndi onenepa kwambiri. Iye anatsogolera Israeli zaka makumi anayi.

19 Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana. 20 Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako.

21 Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake. 22 Ananena momwemo kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli, pakuti Bokosi la Mulungu lalandidwa.”

Bokosi la Chipangano Pakati pa Afilisti

Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi. Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala. Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde.

Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira. Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.” Choncho anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anawafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu wa Israeli tichite nalo chiyani?”

Iwo anayankha kuti, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lipite ku Gati.” Kotero analichotsa Bokosi la Mulungu wa Israelilo.

Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa. 10 Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni.

Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.” 11 Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko. 12 Anthu amene sanafe anavutika ndi zithupsa, ndipo kulira kwa anthu a mu mzindamo kunamveka kumwamba.

Bokosi la Chipangano Libwerera ku Israeli

Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.”

Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.”

Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?”

Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu. Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu. Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi?

“Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita. Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.”

10 Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. 11 Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa. 12 Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi.

13 Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. 14 Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. 15 Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. 16 Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo.

17 Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni. 18 Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.

19 Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri. 20 Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?”

21 Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”

Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.

Samueli Agonjetsa Afilisti ku Mizipa

Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize. Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho Aisraeli anachotsa milungu yawo ya Baala ndi Asitoreti ndi kutumikira Yehova yekha.

Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.” Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa.

Afilisti anamva kuti Aisraeli asonkhana ku Mizipa, choncho akalonga awo anabwera kudzawathira nkhondo. Ndipo Aisraeli atamva anachita mantha chifukwa cha Afilisti. Choncho anati kwa Samueli, “Musasiye kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti atipulumutse mʼdzanja la Afilistiwa.” Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha.

10 Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa. 11 Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari.

12 Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.” 13 Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli.

Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli. 14 Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori.

15 Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse. 16 Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa. 17 Koma pambuyo pake ankabwerera ku Rama, kumene kunali nyumba yake. Ankaweruza Aisraeli kumeneko. Ndipo iye anamanga guwa lansembe la Yehova kumeneko.

Aisraeli Apempha kuti Akhale ndi Mfumu

Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli. Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya, ndipo ankaweruza ku Beeriseba. Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo.

Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.”

Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova. Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo. Kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mpaka lero zochita zawo zakhala zondikana Ine nʼkumatumikira milungu ina. Tsopano akukukananso iwe. Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.”

10 Samueli anawawuza anthu amene amamupempha mfumu aja mawu onse a Yehova. 11 Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo. 12 Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. 13 Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. 14 Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake. 15 Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake. 16 Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. 17 Iyo idzatenga gawo lakhumi la zoweta zanu, ndipo inu eni mudzakhala akapolo ake. 18 Nthawi imeneyo ikadzafika inu mudzalira momvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhira, koma Yehova sadzakuyankhani.”

19 Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. 20 Kotero ifenso tidzakhala ngati mayiko ena. Mfumu yathu idzatiweruza ndiponso idzatuluka nafe kutitsogolera kukamenya nkhondo.”

21 Samueli atamva zonse zimene anthuwo ananena, iye anakazifotokozanso kwa Yehova. 22 Yehova anamuyankha nati, “Amvere zimene akunena ndipo apatse mfumu.”

Ndipo Samueli anati kwa Aisraeli aja, “Bwererani aliyense kwawo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.