Beginning
Mlevi ndi Mzikazi Wake
19 Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu.
Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda. 2 Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi. 3 Mwamuna wake anamulondola kuti akayankhule naye mofatsa kumupempha kuti abwerere. Iye anali ndi antchito ake ndi abulu ake awiri. Anafika ku nyumba kwa mkazi uja ndipo iye anamulowetsa mʼnyumba ya abambo ake. Abambo aja atamuona mnyamata uja anamulandira mwachimwemwe. 4 Mpongozi wake, yemwe anali abambo a mtsikanayo, anamupempha kuti aswere. Choncho anakhalako masiku atatu. Ankadya, kumwa ndi kugona komweko.
5 Tsiku lachinayi anadzuka mʼmamawa kukonzekera kuti azipita kwawo, koma abambo ake a mtsikanayo anawuza mkamwini wawo uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, ndipo kenaka mutha kupita.” 6 Choncho onse awiri anakhala pansi ndi kudya ndi kumwa pamodzi. Atadya, abambo a mtsikanayo anati, “Chonde mugonenso konkuno musangalale.” 7 Ndipo pamene mwamunayo anakonzeka kuti azipita, apongozi ake anamuwumirizanso kuti asapite. Choncho anagona komweko usiku umenewo. 8 Mmawa wa tsiku lachisanu, atadzuka kuti azipita abambo ake a mtsikanayo anamuwuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mutandale mpaka madzulo.” Choncho awiriwo anadya pamodzi.
9 Pambuyo pake munthu uja pamodzi ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki anakonzeka kuti azipita. Koma abambo a mtsikana uja anatinso kwa iye, “Onani tsopano kukuda. Gonani konkuno pakuti tsiku latha kale. Gonani ndipo musangalale. Mawa mudzuka mʼmamawa ndi kumapita kwanu.” 10 Koma munthuyo sanafune kugonanso tsiku limenelo. Choncho ananyamuka kumapita, ndipo anakafika ku malo oyangʼanana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu ake awiri okhala ndi zokhalira zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.
11 Akuyandikira ku Yebusi nʼkuti kutada ndithu. Tsono mtumiki uja anawuza mbuye wake kuti, “Tiyeni, tipatukire ku mzinda wa Ayebusiwa ndipo tigone.”
12 Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.” 13 Tsono anamuwuza mtumiki wake uja kuti, “Tiye tipite ku amodzi a malo awa, ku Gibeya kapena ku Rama ndipo tikagone kumeneko.” 14 Choncho nayenda ulendo wawo, ndipo dzuwa linawalowera akuyandikira ku Gibeya mʼdziko la Benjamini. 15 Ndipo anapatukira kumeneko kuti alowe mu mzinda wa Gibeya kukagona usiku umenewo. Anakalowa mu mzindamo ndi kukakhala pabwalo popeza panalibe munthu amene anawalandira ku nyumba kwake kuti akagone.
16 Pambuyo pake anangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito ya ku munda kwake madzulo. Iyeyu anali wa ku dziko la mapiri ku Efereimu, koma ankakhala ku Gibeya. Koma anthu a kumeneko anali a fuko la Benjamini. 17 Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”
18 Iye anayankha kuti, “Tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda ndipo tikupita kutali ku dziko lamapiri la Efereimu kumene ndimakhala. Ndinapita ku Betelehemu mʼdziko la Yuda ndipo tsopano ndikubwerera kwathu. Koma palibe aliyense amene wanditengera ku nyumba yake. 19 Tili ndi udzu ndi chakudya cha abulu athu. Tilinso ndi buledi ndi vinyo wokwanira ifeyo: ine, mdzakazi wanuyu, ndi mtumiki amene ali nafeyu. Palibe chimene tikusowa.”
20 Munthu wokalambayo anati, “Mtendere ukhale nanu. Ine ndikuthandizani pa zosowa zanu zonse, koma musagone pabwalo usiku uno.” 21 Choncho anapita nawo ku nyumba yake, ndipo anawapatsa abulu ake chakudya. Alendo aja anasamba mapazi awo, nalandira chakudya ndi chakumwa.
22 Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.”
23 Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. 24 Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.”
25 Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite. 26 Ndipo mmawa kukucha mzikazi uja anabwerera nakagwa pansi pa khomo pa nyumba imene mwamuna wake anali, ndipo anakhala pomwepo mpaka kunayera.
27 Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde. 28 Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo.
29 Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli. 30 Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!”
Aisraeli Achita Nkhondo ndi Fuko la Benjamini
20 Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dziko la Dani mpaka ku Beeriseba ndiponso ku dziko la Giliyadi ananyamuka ngati munthu mmodzi nakasonkhana pamaso pa Yehova ku Mizipa. 2 Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga. 3 Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.”
4 Choncho Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwa uja anayankha nati, “Ine ndinapita ku Gibeya mʼdziko la Benjamini pamodzi ndi mzikazi wanga kuti tikagone kumeneko. 5 Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa. 6 Ine ndinatenga mzikazi wangayo ndi kumudula nthulinthuli ndikuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraeli. Anthu amenewa, zedi achita chinthu chonyansa kwambiri mʼdziko lino la Israeli. 7 Ndi zimenezotu inu Aisraeli nonse; yankhulaponi mawu ndi kupereka maganizo anu.”
8 Anthu onse anayimirira ngati munthu mmodzi nanena kuti, “Palibe mmodzi wa ife amene apite ku nyumba kwake. Palibe amene abwerere ku nyumba kwake. 9 Koma tsopano chimene ife tichite ndi dziko la Gibeya ndi ichi: Tidzapita kukamenyana nawo potsatira zimene maere anene. 10 Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.” 11 Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo.
12 Mafuko a Israeli anatumiza anthu kwa fuko lonse la Benjamini kukafunsa kuti, “Kodi zoyipa zachitika pakati panuzi ndi zotani? 13 Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.”
Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo. 14 Mʼmalo mwake, Abenjaminiwo anatuluka mʼmizinda yawo ku Gibeya kukamenyana ndi Aisraeli. 15 Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa. 16 Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya.
17 Aisraeli, kupatula fuko la Benjamini, anasonkhanitsa anthu 400,000 a malupanga, onse odziwa bwino nkhondo.
18 Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?”
Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.”
19 Mmawa mwake Israeli ananyamuka nakamanga msasa moyangʼanana ndi Gibeya. 20 Aisraeli anapita kukachita nkhondo ndi fuko la Benjamini ndipo anandandalika ankhondo awo moyangʼanana ndi Gibeya. 21 A fuko la Benjamini anatuluka ku Gibeya ndipo tsiku limenelo anapha Aisraeli 22,000 ku nkhondoko. 22 Koma ankhondo a Israeli analimbikitsananso mtima ndipo anasonkhanitsanso kachiwiri ankhondo awo pa malo pamene anawandandalika poyamba paja. 23 Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?”
Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.”
24 Ndipo Aisraeli anayandikiranso pafupi ndi fuko la Benjamini tsiku lachiwiri lake kuti amenyane nawo. 25 Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga.
26 Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. 27 Bokosi la Chipangano cha Yehova linali kumeneko. 28 Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?”
Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.”
29 Choncho Aisraeli anayika anthu obisalira mozungulira Gibeya. 30 Tsiku lachitatu anapita kukamenyana ndi Benjamini ndipo anayika ankhondo mʼmalo mwawo kuti amenyane ndi Gibeya monga anachitira poyamba. 31 Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera.
32 Abenjamini ankanena kuti, “Tikuwagonjetsa monga poyamba.” Koma Aisraeli ankanena kuti, “Tiyeni tithawe kuti apite ku msewu chapatali ndi mzinda wawo.”
33 Choncho Aisraeli onse anachoka mʼmalo mwawo ndi kukandanda ku Baala-Tamara, ndipo Aisraeli obisalira aja anatuluka mʼmalo awo kummawa kwa Geba. 34 Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. 35 Tsono Yehova anagonjetsa Abenjamini pamaso pa Israeli motero kuti Aisraeli anapha ankhondo a Abenjamini 25,100 tsiku limenelo. 36 Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa.
Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya. 37 Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga. 38 Chizindikiro chimene Aisraeli anapangana ndi anthu obisalira aja chinali chakuti obisalira aja akangofukiza utsi wambiri ngati mtambo mu mzindamo, 39 ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo.
Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.” 40 Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba. 41 Kenaka Aisraeli anabwerera ndipo Abenjamini anachita mantha, chifukwa anaona kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. 42 Choncho anathawa pamaso pa Aisraeli kudzera njira ya ku chipululu, koma nkhondo inawapeza. Ndipo anaphedwa kumeneko ndi Aisraeli amene anachokera mu mzindamo. 43 Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya. 44 Abenjamini 18,000 olimba mtima anaphedwa. 45 Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000.
46 Pa tsiku limenelo Abenjamini olimba mtima okhala ndi malupanga okwana 25,000 anafa. 47 Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi. 48 Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza.
Akazi a Abenjamini
21 Aisraeli anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe mmodzi wa ife adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.”
2 Anthu anapita ku Beteli kumene anakakhala pansi pamaso pa Mulungu mpaka madzulo. Iwo anakweza mawu nalira kwambiri. 3 Iwo ankanena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli, nʼchifukwa chiyani izi zachitika mʼdziko la Israeli kuti lero fuko limodzi lisowe mu Israeli?”
4 Mmawa mwake anthu anadzuka namanga guwa lansembe ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.
5 Kenaka Aisraeli anafunsa kuti, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Israeli sanafike ku msonkhano wa Yehova?” Anatero chifukwa anachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene alephere kupita ku Mizipa ndi kuti woteroyo ayenera kuphedwa.
6 Tsono Aisraeli anamva chisoni chifukwa cha abale awo, Abenjamini. Iwo anati, “Lero fuko limodzi lachotsedwa mu Israeli. 7 Kodi tingawapezere bwanji anthu otsalawa akazi woti awakwatire? Paja ife tinalumbira kwa Yehova kuti sitidzapereka ana anthu aakazi kuti awakwatire. 8 Kenaka anafunsa kuti, ‘Kodi mu fuko la Israeli ndani amene sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?’ ” Tsono panapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wochokera ku Yabesi Giliyadi amene anapita ku msonkhano ku misasa kuja. 9 Pamene anthu anawerengana anangoona kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi palibe.
10 Choncho msonkhano unatumiza anthu ankhondo 12,000 ndi kuwalamula kuti, “Mukaphe anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi, kuphatikizapo akazi ndi ana.” 11 Izi ndi zimene mukachite. “Mukaphe mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense amene anadziwapo mwamuna.” 12 Iwo anapeza atsikana 400 pakati pa anthu okhala mu Yabesi Giliyadi amene anali asanadziwepo mwamuna ndipo anabwera nawo ku misasa ku Silo mʼdziko la Kanaani.
13 Kenaka msonkhano wonse unatumiza uthenga kwa Abenjamini amene ankakhala ku thanthwe la Rimoni kuwawuza kuti nkhondo yatha. 14 Choncho Abenjamini anabwera nthawi imeneyo ndipo Aisraeli anawapatsa akazi a ku Yabesi Giliyadi amene sanaphedwe. Koma sanapezeke owakwanira.
15 Aisraeli anamvera chisoni Abenjamini, chifukwa Yehova anachita ngati waligwerula dzino fuko la Israeli. 16 Choncho akuluakulu a msonkhano anati, “Kodi tikawapezera kuti akazi anthu otsalirawa kuti awakwatire popeza kuti akazi a fuko la Benjamini anaphedwa?” 17 Iwo anati, “Abenjamini amene anapulumukawa ayenera kukhala ndi zidzukulu, kuti mtundu wa Israeli usafafanizike. 18 Ife sitingathe kuwapatsa ana anthu aakazi kuti akwatire. Paja tinalumbira kuti, ‘Akhale wotembereredwa aliyense amene adzapereka mwana wake wamkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini kuti akwatire.’ 19 Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ”
20 Choncho anawalamulira Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale mʼminda ya mpesa 21 ndipo mukakhale tcheru. Ana aakazi a ku Silo akadzatulukira kudzavina nawo magule, pomwepo inu mutuluke minda ya mpesa ndi kukawagwira aliyense wake ndi kupita nawo ku dziko la Benjamini. 22 Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ”
23 Abenjamini anachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja anagwirapo ena, malingana ndi chiwerengero chawo, nawatenga kuti akhale akazi awo. Kenaka ananyamuka kubwerera ku dziko la kwawo, nakamanganso mizinda yawo ndi kumakhalamo.
24 Pambuyo pake Aisraeli anachoka kumeneko ndi kubwerera kwawo, ku mafuko ndi ku mabanja awo, aliyense ku dera la cholowa chake.
25 Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense ankangochita zimene zomukomera yekha.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.