Beginning
Mwambo wa Mdulidwe pa Giligala
5 Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo.
2 Tsono Yehova anati kwa Yoswa, “Panga mipeni ya miyala ndipo uchitenso mwambo wa mdulidwe pa Aisraeli.” 3 Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti.
4 Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto. 5 Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. 6 Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. 7 Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. 8 Atamaliza kuchita mdulidwe uja, anthu onse anakakhala ku misasa yawo kudikira kuti zilonda zipole.
9 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero.
10 Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. 11 Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. 12 Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani.
Kugwa kwa Makoma a Yeriko
13 Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?”
14 Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?”
15 Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.
6 Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.
2 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Taona ndapereka Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake mʼmanja mwako. 3 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. 4 Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. 5 Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo.”
6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake.” 7 Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.”
8 Mofanana ndi mmene Yoswa anayankhulira kwa anthu aja, ansembe asanu ndi awiri anapita patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Yehova akuliza malipenga a nyanga za nkhosa zija, ndipo Bokosi la Chipangano cha Yehova limabwera pambuyo pawo. 9 Ankhondo amayenda patsogolo pa ansembe amene amayimba malipenga, ndiponso gulu lina pambuyo pa Bokosilo. Nthawi yonseyi nʼkuti malipenga akulira. 10 Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!” 11 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anazungulira mzindawo kamodzi. Kenaka anthu anabwerera ku msasa wawo kukagona.
12 Yoswa anadzuka mmawa tsiku linalo ndipo ansembe ananyamula Bokosi la Yehova. 13 Ansembe asanu ndi awiri onyamula malipenga asanu ndi awiri anakhala patsogolo pa Bokosi la Yehova akuyimba malipenga. Ankhondo anali patsogolo pawo ndipo gulu lina linatsatira Bokosi la Yehova. Apa nʼkuti malipenga akulira. 14 Tsiku lachiwiri anazunguliranso mzinda kamodzi ndi kubwerera ku misasa. Iwo anachita izi kwa masiku asanu ndi limodzi.
15 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, anadzuka mʼbandakucha ndipo anazungulira mzindawo kasanu ndi kawiri. Ndi pa tsiku lokhali limene anazungulira mzindawu kasanu ndi kawiri. 16 Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu! 17 Mzindawu ndi zonse zimene zili mʼmenemo muziwononge. Rahabe yekha, mayi wadama, ndi aliyense amene ali pamodzi naye mʼnyumba mwake asaphedwe, chifukwa anabisa anthu odzazonda, amene ife tinawatuma 18 Koma musatenge kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukadzangotenga kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, misasa ya Israeli idzawonongedwa. 19 Zonse za siliva ndi golide, ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo, ndi zake za Yehova ndipo ziyenera kukasungidwa mosungiramo chuma chake.”
20 Ansembe analiza malipenga. Anthu atamva kulira kwa malipenga, anafuwula kwambiri ndipo makoma a Yeriko anagwa. Choncho ankhondo anabwera ku mzinda uja nawulanda. 21 Iwo analowa mu mzindawo nawononga ndi lupanga chilichonse chamoyo kuyambira amuna, akazi, ana ndi akulu, ngʼombe, nkhosa ndi abulu.
22 Yoswa anawuza anthu awiri amene anakazonda dziko aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadama uja ndipo mukamutulutse iye pamodzi ndi onse amene ali naye ndipo mukabwere nawo kuno, munamulumbirira.” 23 Choncho iwo anapita nakatenga Rahabe, abambo ake ndi amayi ake, abale ake ndi onse amene anali naye. Iwo anatulutsa banja lake lonse ndipo analiyika kuseri kwa msasa wa Aisraeli.
24 Kenaka iwo anawotcha mzinda wonse ndi chilichonse chimene chinali mʼmenemo, kupatulapo zasiliva ndi zagolide pamodzi ndi ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo zimene anakaziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha Yehova. 25 Koma Yoswa sanaphe Rahabe, mkazi wadamayo pamodzi ndi banja lake ndi onse amene anali naye, chifukwa anabisa anthu amene iye anawatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabeyo zikukhala pakati pa Aisraeli mpaka lero.
26 Pa nthawi imeneyo Yoswa anapereka chenjezo motemberera kuti, “Akhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda uwu wa Yeriko:
“Aliyense amene adzayike maziko ake,
mwana wake wamwamuna wachisamba adzafa,
aliyense womanga zipata zake
mwana wake wamngʼono adzafa.”
27 Motero Yehova anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake inafalikira dziko lonse.
Tchimo la Akani
7 Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri.
2 Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai.
3 Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.” 4 Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai. 5 Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.
6 Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo. 7 Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani! 8 Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake? 9 Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”
10 Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere? 11 Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. 12 Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu.
13 “Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’
14 “Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi. 15 Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!”
16 Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa. 17 Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa. 18 Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda.
19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”
20 Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi: 21 Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.”
22 Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake. 23 Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova.
24 Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori. 25 Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.”
Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo. 26 Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake.
Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Ai
8 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako. 2 Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”
3 Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku 4 nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo. 5 Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba. 6 Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa, 7 inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo. 8 Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”
9 Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.
10 Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai. 11 Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12 Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo. 13 Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.
14 Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo. 15 Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu. 16 Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo. 17 Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli.
18 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai. 19 Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira.
20 Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa. 21 Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai. 22 Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa 23 kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa.
24 Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo. 25 Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000. 26 Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa. 27 Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa.
28 Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu. 29 Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.
Kuchitanso Pangano pa Phiri la Ebala
30 Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala. 31 Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. 32 Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba. 33 Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.
34 Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose. 35 Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.