Beginning
Madalitso Akabwerera kwa Yehova
30 Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu, 2 ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino, 3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani. 4 Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso. 5 Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu. 6 Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo. 7 Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani. 8 Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino. 9 Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu, 10 ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Moyo kapena Imfa
11 Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali. 12 Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 13 Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 14 Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere.
15 Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko. 16 Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.
17 Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza, 18 lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge.
19 Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo. 20 Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose
31 Tsono Mose anapita ndi kukayankhula mawu awa kwa Aisraeli onse: 2 “Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukutsogolerani. Yehova wandiwuza kuti, ‘Iwe sudzawoloka Yorodani.’ 3 Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova. 4 Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo. 5 Ambuye adzawapereka kwa inu, ndipo inu mukawachitire zonse zimene ndakulamulani. 6 Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”
7 Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo. 8 Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”
Kuwerenga Malamulo
9 Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli. 10 Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa, 11 pamene Aisraeli onse abwera kudzaonekera pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamalo pamene Iye adzasankhe, mudzawerenge malamulo onsewa iwo akumva. 12 Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa. 13 Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”
Aneneratu za Kuwukira kwa Aisraeli
14 Yehova anawuza Mose kuti, “Nthawi ya kufa kwako yafika. Itana Yoswa ndipo mubwere ku tenti ya msonkhano, kumene Ine ndidzamulangiza.” Choncho Mose ndi Yoswa anabwera ku tenti ya msonkhano.
15 Pamenepo Yehova anaonekera ku tenti mʼchipilala cha mtambo, ndipo mtambowo unayima pamwamba pa khomo lolowera mu tenti. 16 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, “Iwe ukupita kukapuma kumene kuli makolo ako, ndipo ukangomwalira, anthu awa adzayamba kupembedza milungu yachilendo ya mʼdziko limene akukalowamo. Adzanditaya ndi kuphwanya pangano lomwe ndinachita nawo. 17 Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’ 18 Ndipo Ine ndidzabisa ndithu nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoyipa zimene anachita potembenukira kwa milungu ina.
19 “Tsopano ulembe mawu a nyimbo iyi ndipo uwaphunzitse Aisraeli, uwawuze kuti aziyimba, kuti ikhale mboni yanga yowatsutsa. 20 Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa. 21 Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.” 22 Choncho Mose analemba nyimbo iyi tsiku limenelo ndi kuwaphunzitsa Aisraeli.
23 Yehova analamula Yoswa mwana wa Nuni kuti, “Khala wamphamvu ndipo limba mtima, chifukwa udzalowetsa Aisraeli mʼdziko limene ndinawalonjeza mwa lumbiro, ndipo Ine mwini ndidzakhala nawe.”
24 Mose atatha kulemba malamulowa mʼbuku, osasiyako kanthu, 25 analamula Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova kuti, 26 “Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani. 27 Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira! 28 Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko anu pamodzi ndi akuluakulu onse, kuti ndiyankhule mawu awa iwo akumva ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni yowatsutsa. 29 Chifukwa ndikudziwa kuti ine ndikamwalira mudzayipa kwambiri ndi kutembenuka kuleka njira imene ndinakulamulani. Masiku amene akubwera, masautso adzakugwerani chifukwa mudzachita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuputa mkwiyo wake chifukwa cha zimene manja anu anapanga.”
Nyimbo ya Mose
30 Ndipo Mose ananena mawu a nyimbo iyi kuyiimba koyambira mpaka potsiriza gulu lonse la Aisraeli likumva:
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.