Beginning
17 Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa.
2 Ngati mwamuna kapena mkazi pakati panu, mʼmizinda imene Yehova akukupatsani apezeka akuchita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu pophwanya pangano lake, 3 ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba, 4 ndipo inu nʼkuwuzidwa zimenezi, mufufuze bwinobwino. Ngati ndi zoona, ndipo ngati zatsimikizika kuti chonyansa choterechi chachitikadi mu Israeli, 5 mumutengere mwamuna kapena mkazi amene wachita chonyansa choterechi ku chipata cha mzinda wanu ndi kumupha pomugenda miyala. 6 Munthu aziphedwa pakakhala mboni ziwiri kapena zitatu koma osati mboni imodzi yokha ayi. 7 Wochitira umboniwo ndiwo aziyamba kumupha munthuyo, ndipo kenaka anthu onse. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
Mabwalo a Milandu
8 Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 9 Mudzapite kwa ansembe Alevi ndi kwa woweruza wa pa nthawi imeneyo. Kawafunseni ndipo iwowo adzakuwuzani zoyenera kuchita. 10 Kachiteni zimene adzakuwuzenizo kuchokera ku malo amene Yehova adzasankhe. Kaonetsetseni kuti mukutsatira zonse zimene akuwuzanizo. 11 Kachiteni motsatira malamulo ndi malangizo amene adzakuwuzeni; osawanyoza, potembenukira kumanja kapena kumanzere. 12 Munthu aliyense amene adzanyoza woweruza kapena wansembe amene akutumikira kumeneko mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu, aphedwe ndithu. Muzichotsa choyipa pakati pa Israeli. 13 Anthu onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha, choncho sadzadzikuzanso.
Mfumu
14 Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,” 15 mudzakhazikitse mfumu yoti izikakulamulirani, mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati panu. Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Osasankha mlendo, munthu amene sachokera pakati pa abale anu Aisraeli. 16 Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.” 17 Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri.
18 Akakhala pa mpando waufumuwo, ayenera kulemba za iye mwini mʼbuku la malamuloli, kuchokera kwa ansembe Alevi. 19 Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa. 20 Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.
Zopereka za kwa Ansembe ndi Alevi
18 Ansembe Achilevi amene ndi fuko lonse la Alevi, asapatsidwe malo kapena cholowa pakati pa Aisraeli. Iwowa azidzadya zoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe, popeza zimenezo ndiye cholowa chawo. 2 Iwowa sadzakhala ndi cholowa pakati pa abale awo pakuti Yehova ndiye cholowa chawo monga anawalonjezera.
3 Anthu amene abwera kudzapereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe gawo lake motere: mwendo wakutsogolo, nyama yamʼmasaya ndi zamʼkati. 4 Muziwapatsa zamasika zoyamba za tirigu wanu, vinyo watsopano ndi mafuta, ndi ubweya woyamba pometa nkhosa zanu, 5 pakuti Yehova Mulungu wanu wawasankha iwowa ndi ana awo pakati pa mafuko anu onse kuti aziyimirira ndi kutumikira mʼdzina la Yehova nthawi zonse.
6 Ngati Mlevi asuntha achoka ku mzinda wake ndi kupita kumalo kwina kumene Yehova wasankha mu Israeli momwemo ndi mtima wake wonse, 7 kumeneko akhoza kukatumikirako mʼdzina la Yehova Mulungu wake monga Alevi anzake onse amene akutumikira pamaso pa Yehova. 8 Iye ayenera kulandira zogawana zawo mofanana ndi anzakewo ngakhale kuti iye anagulitsa kale cholowa cha pa banja pawo.
Makhalidwe Oletsedwa
9 Mukafika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire makhalidwe onyansa a anthu a mʼdzikolo. 10 Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti, 11 wolodza, kapena woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndi kumafunsira nzeru kwa anthu akufawo. 12 Aliyense wochita zinthu zotere ndi wonyansa pamaso pa Yehova, ndipo chifukwa cha zonyansa zimenezi Yehova adzakupirikitsirani mitundu ya anthu imeneyi. 13 Muzikhala angwiro pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
Aneneri
14 Mitundu ya anthu imene mudzayipirikitseyo imamvera anyanga kapena owombeza mawula. Koma inu Yehova Mulungu wanu sanakuvomerezeni kutero. 15 Yehova Mulungu wanu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine. Muyenera kumumvera ameneyo. 16 Pakuti izi ndi zimene munapempha kwa Yehova Mulungu wanu ku Horebu pa tsiku la msonkhano lija pamene munati, “Ife tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto woopsawu, kuopa kuti tingafe.”
17 Yehova anati kwa ine, “Zimene akunenazi ndi zabwino. 18 Ndidzawawutsira mneneri ngati iwe pakati pa abale awo ndipo ndidzayika mawu anga mʼkamwa mwake ndipo adzawawuza chilichonse chimene ndidzamulamula. 19 Ine mwini ndidzaweruza aliyense amene sadzamvera mawu anga amene mneneriyo adzayankhula mʼdzina langa. 20 Koma mneneri wonena zinthu mʼdzina langa ndisanamulamulire kutero, kapena mneneri wonenera mʼdzina la milungu ina, ayenera kuphedwa.”
21 Mwina mukhoza kumadzifunsa kuti, “Kodi tingadziwe bwanji kuti uthengawu sanayankhule ndi Yehova?” 22 Ngati zimene mneneriyo wanenera mʼdzina la Yehova sizinachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti umenewo si uthenga umene Yehova wayankhula. Mneneri ameneyo amangoyankhula za mʼmutu mwake ndiye musadzidzimuke naye.
Mizinda Yothawirako
19 Yehova Mulungu wanu akadzawononga anthu amene dziko lawo akukupatsani, ndipo inu mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼmizinda ndi mʼnyumba zawo, 2 mukapatule mizinda itatu imene ili pakati pa dziko lomwe Yehova Mulungu akukupatsani kukhala lanu. 3 Mudzakonze misewu ndi kuligawa patatu dzikolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, kuti aliyense wopha munthu akhoza kuthawirako.
4 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa. 5 Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake. 6 Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala. 7 Ichi ndi chifukwa chake ndikukulamulani kuti mudzipatulire nokha mizinda itatu.
8 Ngati Yehova Mulungu wanu akulitsa malire anu monga analonjezera pa malumbiro ndi makolo anu, nakupatsani dziko lonse monga analonjezera, 9 chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera. 10 Muchite zimenezi kuti musakhetse magazi wosalakwa mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa, ndipo kuti musapezeke ndi mlandu wokhetsa magazi.
11 Koma ngati munthu adana ndi mnzake namubisalira panjira nʼkumuvulaza mpaka kumupha, nathawira ku umodzi mwa mizindayi, 12 akuluakulu a mu mzinda wake akamugwire ndi kumubwezera ku mzinda wake namupereka kwa wolipsira kuti aphedwe. 13 Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
14 Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Mboni
15 Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.
16 Ngati mboni yonama ifuna kunamizira munthu mlandu, 17 anthu awiri okhudzidwa ndi mlanduwo ayenera kuyima pamaso pa Yehova pali ansembe ndi oweruza amene ali pa ntchito pa nthawiyo. 18 Oweruza afufuze bwinobwino, ndipo ngati zatsimikizika kuti mboniyo ndi yabodza, yopereka umboni wonama pa mʼbale wake, 19 ndiye kuti amuchitire iyeyo zimene anafuna kuchitira mʼbale wakezo. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 20 Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu. 21 Osachita chisoni, moyo uzilipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja ndi phazi kulipira phazi.
Za ku Nkhondo
20 Pamene mukupita kokachita nkhondo ndi adani anu, mukaona akavalo kapena magaleta kapena gulu la ankhondo kuposa inuyo musamaope chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto adzakhala nanu. 2 Pamene mwatsala pangʼono kuyamba nkhondo, wansembe azibwera kutsogolo ndipo aziyankhula ku gulu lonse lankhondolo. 3 Iye aziti, “Tamverani inu Aisraeli, mukupita kukachita nkhondo ndi adani anu lero. Musataye mitima kapena kuchita mantha ayi. Musaopsedwe kapena kunjenjemera pamaso pawo, 4 pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene apite nanu kukakumenyerani nkhondo ndi kugonjetsa adani anu.”
5 Akuluakulu ankhondo adzati kwa gulu la ankhondolo, “Kodi pali wina amene wangomanga nyumba kumene ndipo sanayitsekulire? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondoko ndipo wina ndi kudzayitsekulira. 6 Kodi pali wina amene analima munda wamphesa ndipo sanayambe kudyerera? Ayambe wapita ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzadyerera mundawo. 7 Kodi pali amene wachita chinkhoswe ndi mkazi ndipo sanamukwatire mkaziyo? Ayambe wabwerera ku mudzi chifukwa mwina akafera ku nkhondo ndipo wina adzakwatira mkaziyo.” 8 Ndipo akuluakulu ankhondowo akapitirize kuti, “Kodi pali amene akuchita mantha kapena kutaya mtima? Abwerere ku mudzi kuopa kuti abale ake angatayenso mtima.” 9 Akuluakuluwo akatsiriza kuyankhula ndi gulu la ankhondolo, adzasankhe olilamulira.
10 Pamene mukuyandikira kuphwanya mzinda, muyambe mwafunsa anthu a mu mzindawo ngati afuna zamtendere. 11 Akavomera natsekula zipata zawo, anthu wonse mu mzindawo adzagwidwa ukapolo nakugwirirani ntchito. 12 Koma akakana za mtendere nachita nanu nkhondo, muwuphwanye mzindawo. 13 Yehova Mulungu wanu akakupatsani mzindawo, muwaphe amuna onse. 14 Akazi, ana, ziweto ndi china chilichonse mu mzindamo, mukhoza kuzitenga kuti zikhale zanu monga katundu wolanda ku nkhondo. Katundu wa adani anuyu amene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukhoza kumugwiritsa ntchito. 15 Mizinda yonse yakutali osati ya mitundu yapafupi, muzichita nayo chomwechi.
16 Komabe mʼmizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, musasiyemo chamoyo chilichonse. 17 Muwawononge kwathunthu Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi monga momwe Yehova Mulungu wanu anakulamulirani. 18 Mukapanda kutero adzakuphunzitsani kuti mutengere zinthu zonyansa zimene amachita popembedza milungu yawo ndipo mudzachimwira Yehova Mulungu wanu.
19 Mukalimbana ndi mzinda nthawi yayitali, kuchita nawo nkhondo pofuna kuwugonjetsa, musawononge podula mitengo yake ndi nkhwangwa, osayidula chifukwa zipatso zakezo mukhoza kudya. Kodi mitengo ya ku munda ndi anthu kuti mukalimbane nayo? 20 Komabe mukhoza kudula mitengo imene mukudziwa kuti si ya zipatso ndi kuyigwiritsa ntchito pa nkhondo mpaka mzinda umene mukumenyana nawowo utagwetsedwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.