Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 8-10

Musayiwale Yehova

Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu. Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi. Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova. Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe. Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.

Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye. Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri, dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi; dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.

10 Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani. 11 Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, 12 kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, 13 ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, 14 mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. 15 Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. 16 Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. 17 Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” 18 Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.

19 Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu. 20 Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.

Osati Chifukwa cha Kulungama kwa Israeli

Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba. Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?” Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.

Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako. Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika.

Mwana Wangʼombe Wagolide

Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova. Ku Horebu munaputa mkwiyo wa Yehova, kotero kuti anakwiya kwambiri nafuna kukuwonongani. Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi. 10 Yehova anandipatsa miyala iwiri yolembedwa ndi chala chake. Pa miyalapo panali malamulo onse amene Yehova analengeza kwa inu pa phiri kuchokera mʼmoto pa tsiku la msonkhano.

11 Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano. 12 Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.”

13 Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi! 14 Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.”

15 Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga. 16 Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani. 17 Motero ine ndinaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwanga, ndi kuyiphwanya inu mukuona.

18 Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri. 19 Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso. 20 Ndipo Yehova anakwiya ndi Aaroni ndipo akanamuwononga, koma ine ndinamupemphereranso Aaroniyo. 21 Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri.

22 Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava.

23 Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera. 24 Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova.

25 Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani. 26 Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu. 27 Kumbukirani atumiki anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Musatengere kupulupudza, kuyipa ndi kuchimwa kwawo anthuwa. 28 Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’ 29 Koma iwowa ndi anthu anu, chuma chanu chimene munachitulutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ndi mkono wanu wotambasuka.”

Miyala Ngati Yoyamba Ija

10 Pa nthawi imeneyo Yehova anati kwa ine, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo ubwere nayo kwa Ine ku phiri. Upangenso bokosi lamatabwa. Ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ndipo iwe ukuyenera kuyika miyalayo mʼbokosimo.”

Choncho ndinapanga bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha ndi kusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo ndinapita ku phiri nditanyamula miyala iwiri mʼmanja mwanga. Yehova analemba pa miyala iwiriyo zimene analemba poyamba, Malamulo Khumi amene analengeza kwa inu pa phiri paja, mʼmoto, pa tsiku la msonkhano. Ndipo Yehova anawapereka kwa ine. Tsono ndinatsika ku phiri kuja ndi kuyika miyalayo mʼbokosi ndinapanga lija monga Yehova anandilamulira, ndipo panopa ili mʼmenemo.

Aisraeli anayenda kuchokera ku Beeroti Beni Yaakani mpaka ku Mosera. Kumeneko Aaroni anamwalira nayikidwa mʼmanda, ndipo mwana wake Eliezara anakhala wansembe mʼmalo mwake. Kuchokera kumeneko Aisraeli anapita ku Gudigoda, napitirira mpaka ku Yotibata, ku dziko la mitsinje ya madzi. Pa nthawi imeneyo Yehova anapatula fuko la Levi kuti anyamule bokosi la pangano la Yehova lija, kuti ayimirire pamaso pa Yehova, kutumikira ndi kunena madalitso pa dzina lake monga amachitira mpaka lero. Nʼchifukwa chake Alevi alibe gawo kapena cholowa pakati pa abale awo. Yehova ndiye cholowa chawo monga momwe Yehova Mulungu wanu anawawuzira.

10 Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni. 11 Yehova anati kwa ine, “Pita ndi kutsogolera anthuwa pa njira yawo, kuti alowe ndi kulandira dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndiwapatse.”

Kuopa Yehova

12 Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, 13 ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.

14 Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 15 Yehova anayika mtima wake pa makolo anu okha ndipo anawakondadi nasankha adzukulu awo mwa mitundu yonse pa dziko lapansi, kunena inuyo monga mulili lero. 16 Motero chitani mdulidwe wa mitima yanu ndipo musakhalenso opulupudza. 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. 18 Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. 19 Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto. 20 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye. Mumukakamire Iyeyo ndi kuchita malumbiro anu mʼdzina lake. 21 Iye ndiye matamando anu, Mulungu wanu amene anakuchitirani zodabwitsa zazikulu ndi zoopsa zimene munaona ndi maso anu zija. 22 Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.