Beginning
Malo omwe Aisraeli Anayima pa Ulendo Wawo
33 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. 2 Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:
3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, 4 pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.
5 Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.
6 Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.
7 Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.
8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.
9 Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.
10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.
11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.
12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.
13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.
14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.
15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai
16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.
17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.
18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.
19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.
20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.
21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.
22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.
23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.
24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.
25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.
26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.
27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.
28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.
29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.
30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.
31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.
32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.
33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.
34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.
35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.
36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.
37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. 38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.
40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.
41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.
42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.
43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.
44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.
45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.
46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.
47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.
48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.
50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, 52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. 53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. 54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.
55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. 56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ”
Malire a Dziko la Kanaani
34 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. 4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, 5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori 8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, 9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. 11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. 12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.
“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”
13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, 14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. 15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. 19 Mayina awo ndi awa:
Kalebe mwana wa Yefune,
wochokera ku fuko la Yuda,
20 Semueli mwana wa Amihudi,
wochokera ku fuko la Simeoni;
21 Elidadi mwana wa Kisiloni,
wochokera ku fuko la Benjamini;
22 Buki mwana wa Yogili,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 Hanieli mwana wa Efodi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 Kemueli mwana wa Sifitani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 Elizafani mwana wa Parinaki,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 Palitieli mwana wa Azani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 Ahihudi mwana wa Selomi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 Pedaheli mwana wa Amihudi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.