Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 23-25

Uthenga Woyamba wa Balaamu

23 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.

Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.

Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.”

Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”

Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu. Ndipo Balaamu ananena uthenga wake:

“Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu,
    mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa.
Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga,
    pita nyoza Israeli.’
Ndingatemberere bwanji
    amene Mulungu sanawatemberere?
Ndinganyoze bwanji
    amene Yehova sanawanyoze?
Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu,
    ndikuwaona kuchokera pa zitunda.
Ndikuona anthu okhala pawokha,
    osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina.
10 Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi,
    kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli?
Lekeni ndife imfa ya oyera mtima,
    ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!”

11 Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!”

12 Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?”

Uthenga Wachiwiri wa Balaamu

13 Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.” 14 Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.

15 Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.”

16 Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”

17 Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”

18 Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake:

“Nyamuka Balaki ndipo tamvera;
    Undimvere iwe mwana wa Zipori.
19 Mulungu si munthu kuti aname,
    kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.
Kodi amayankhula koma osachita?
    Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?
20 Wandilamula kuti ndidalitse,
    Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.

21 “Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo,
    sanaone chovuta mu Israeli.
Yehova Mulungu wawo ali nawo:
    mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.
22 Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto,
    ali ndi mphamvu ngati za njati.
23 Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo,
    palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli.
Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti,
    ‘Onani zimene Mulungu wachita!’
24 Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi;
    adzuka okha ngati mkango waumuna
umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira
    ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.”

25 Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa!

26 “Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ”

Uthenga Wachitatu wa Balaamu

27 Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” 28 Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.

29 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 30 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.

24 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye ndipo ananena uthenga wake:

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,
    uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,
uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,
    yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,
    yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:

“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,
    misasa yako, iwe Israeli!

“Monga zigwa zotambalala,
    monga minda mʼmbali mwa mtsinje,
monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,
    monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.
Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;
    mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.

“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;
    ufumu wake udzakwezedwa.

“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto
    ali ndi mphamvu ngati za njati.
Amawononga mitundu yomuwukira
    ndi kuphwanya mafupa awo,
    amalasa ndi mivi yake.
Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,
    monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?

“Amene adalitsa iwe, adalitsike
    ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”

10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. 11 Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”

12 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, 13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? 14 Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”

Uthenga Wachinayi wa Balaamu

15 Ndipo iye ananena uthenga wake nati,

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,
    uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.
16 Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,
    amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba,
amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,
    amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:

17 “Ndikumuona iye koma osati tsopano;
    ndikumupenya iye koma osati pafupi.
Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo;
    ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli.
Iye adzagonjetsa Mowabu
    ndi kugonjetsa ana onse a Seti.
18 Edomu adzagonjetsedwa;
    Seiri, mdani wake, adzawonongedwa
    koma mphamvu za Israeli zidzachuluka.
19 Wolamulira adzachokera mwa Yakobo
    ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.”

Uthenga Wachisanu wa Balaamu

20 Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu:

“Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu
    koma potsiriza pake adzawonongeka.”

Uthenga Wachisanu ndi Chimodzi wa Balaamu

21 Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake,

“Malo amene mukukhalamo ndi otetezedwa,
    chisa chanu chinayikidwa pa thanthwe;
22 komabe inu Akeni mudzawonongedwa,
    pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.”

Uthenga Wachisanu ndi Chiwiri wa Balaamu

23 Ndipo ananenanso uthenga wina kuti,

“Aa, ndani adzakhala ndi moyo Mulungu akachita zimenezi?
24     Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu;
kupondereza Asuri ndi Eberi,
    koma iwonso adzawonongeka.”

25 Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.

Aisraeli Achita Chigololo

25 Aisraeli akukhala ku Sitimu, anayamba kuchita chigololo ndi akazi a ku Mowabu, amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo. Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri.

Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.”

Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.”

Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano. Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake. Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli. Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa.

10 Yehova anawuza Mose kuti, 11 “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga. 12 Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye. 13 Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.”

14 Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni. 15 Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko.

16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe, 18 chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.