Beginning
Ntchito za Ansembe ndi Alevi
18 Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu. 2 Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni. 3 Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe. 4 Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu.
5 “Inuyo muzisamalira malo wopatulika ndi guwa lansembe, kuti ukali wa Yehova usawagwerenso Aisraeli. 6 Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano. 7 Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.
Zopereka za Ansembe ndi Alevi
8 “Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse. 9 Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna. 10 Muzidya zimenezo ngati zinthu zopatulika kwambiri; mwamuna aliyense adyeko. Uzitenge kukhala zopatulika.
11 “Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.
12 “Ndikukupatsani mafuta onse abwino kwambiri a olivi ndi vinyo yense watsopano wabwino kwambiri ndi tirigu yense zomwe Aisraeli amapereka kwa Yehova ngati zipatso zoyamba pa zokolola zawo. 13 Zipatso zonse zoyamba kucha za mʼdziko lawo zomwe amapereka kwa Yehova zidzakhala zako. Aliyense mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa angathe kudyako.
14 “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. 15 Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa. 16 Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.
17 “Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 18 Nyama yake ikhale yanu monga momwe chimakhalira chidale cha nsembe yoweyula ndi ntchafu za miyendo ya kumanja, zonsezi ndi zako. 19 Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.”
20 Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.
21 “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano. 22 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo Aisraeli asamapite pafupi ndi tenti ya msonkhano. Ngati atero adzasenza zotsatira za tchimo lawo ndipo adzafa. 23 Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli. 24 Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ”
25 Yehova anati kwa Mose, 26 “Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. 27 Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. 28 Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. 29 Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’
30 “Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa. 31 Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. 32 Popereka gawo labwino kwambirilo simudzapezeka olakwa. Mukatero simudzadetsa zopereka zoyera za Aisraeli, ndipo simudzafa.’ ”
Phulusa ndi Madzi Oyeretsera
19 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2 “Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli. 3 Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. 4 Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano. 5 Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake. 6 Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. 7 Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 8 Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
9 “Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo. 10 Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.
11 “Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. 12 Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. 13 Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.
14 “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, 15 ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.
16 “Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.
17 “Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. 18 Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda. 19 Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. 20 Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. 21 Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo.
“Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”
Madzi Ochokera Mʼthanthwe
20 Pa mwezi woyamba gulu lonse la Aisraeli linafika ku chipululu cha Zini, ndipo anakhala ku Kadesi. Miriamu anafera kumeneko ndipo anayikidwa mʼmanda.
2 Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. 3 Anakangana ndi Mose kuti, “Kunali bwino ifenso tikanangofa pamene abale athu anafa pamaso pa Yehova! 4 Chifukwa chiyani unabweretsa gulu la Yehova mʼchipululu muno, kuti ife ndi ziweto zathu tife kuno? 5 Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!”
6 Mose ndi Aaroni anachoka mu msonkhano ndi kupita pa khomo la tenti ya msonkhano, nagwa pansi chafufumimba ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 7 Yehova anati kwa Mose, 8 “Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.”
9 Choncho Mose anatenga ndodo pamaso pa Yehova monga momwe anamulamulira. 10 Mose ndi Aaroni anasonkhanitsa anthuwo pamodzi ku thanthwelo ndipo Mose anawawuza kuti, “Tamverani osamvera inu, kodi tikupatseni madzi kuchokera ku thanthwe ili?” 11 Choncho Mose anatukula dzanja lake ndi kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake ndipo madzi ambiri anatuluka mwamphamvu, ndipo anthu ndi ziweto zawo anamwa.
12 Koma Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Chifukwa chakuti simunandikhulupirire ndiponso simunandilemekeze monga Woyera pamaso pa Aisraeli, simudzalowetsa anthuwa mʼdziko limene ndikupereka kwa iwo.”
13 Awa anali madzi a ku Meriba, kumene Aisraeli anakangana ndi Yehova ndiponso kumene Yehovayo anadzionetsa yekha kuti ndi Woyera pakati pawo.
Aedomu Akaniza Njira Aisraeli
14 Mose anatumiza amithenga kuchokera ku Kadesi kupita kwa mfumu ya ku Edomu, kukanena kuti,
“Mʼbale wako Israeli akunena izi: Inuyo mukudziwa za mavuto onse amene anatigwera. 15 Makolo athu anapita ku Igupto ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri. Aigupto anatizunza pamodzi ndi makolo athuwo, 16 koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.”
“Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu. 17 Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidzera mʼminda yanu kapena mu mpesa wanu, kapenanso kumwa madzi mʼchitsime chilichonse. Tidzayenda kutsata msewu waukulu wa mfumu ndipo sitidzapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”
18 Koma Edomu anayankha kuti,
“Musadutse kuno: Mukangoyesera tidzabwera ndi kumenyana nanu ndi lupanga.”
19 Aisraeli anayankha kuti,
“Tidzayenda motsata msewu waukulu. Ndipo ngati ife kapena ziweto zathu tidzamwa madzi anu tidzalipira. Tikungofuna tidutse nawo, palibenso china.”
20 Koma Edomu anayankhanso kuti,
“Musadutse.”
Kenaka Edomu anatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu komanso lamphamvu. 21 Edomu anakaniza Israeli kuti adutse mʼdziko lake, choncho Israeli anabwerera.
Aaroni Amwalira
22 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. 23 Ali pa phiri la Hori, pafupi ndi malire a Edomu, Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, 24 “Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba. 25 Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori. 26 Uvule Aaroni zovala zake ndipo umuveke mwana wake Eliezara, pakuti Aaroni adzafera komweko, ndipo adzakakhala ndi anthu a mtundu wake.”
27 Mose anachita monga Yehova anamulamulira: Anapita ku phiri la Hori gulu lonse likuona. 28 Pamenepo Mose anavula Aaroni zovala zake ndi kuveka mwana wake Eliezara. Aaroni anafa kumeneko pamwamba pa phirilo. Koma Mose ndi Eliezara anatsika ku phiriko, 29 ndipo pamene anthu onse anamva kuti Aaroni wafa, nyumba yonse ya Israeli inamulira Aaroniyo masiku makumi atatu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.