Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 26-27

Mphotho ya Kumvera

26 “ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.

“ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake. Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.

“ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo. Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.

“ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu. 10 Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano. 11 Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu. 12 Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga. 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.

Chilango Chakusamvera

14 “ ‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa, 15 ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa, 16 Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya. 17 Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.

18 “ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 19 Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa. 20 Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.

21 “ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu. 22 Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.

23 “ ‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine, 24 Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu. 25 Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu. 26 Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.

27 “ ‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine, 28 pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 29 Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi. 30 Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu. 31 Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu. 32 Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa. 33 Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. 34 Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35 Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.

36 “ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37 Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38 Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39 Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.

40 “ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41 zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42 Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44 Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ”

46 Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.

Kuwombola Zomwe ndi za Yehova

27 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati munthu anachita lumbiro lapadera loti adzapereka munthu mnzake kwa Yehova ndipo akufuna kuti amuwombole, mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. Ndipo ngati ndi wamkazi, mtengo wake ukhale masekeli makumi atatu. Mtengo wa munthu wamwamuna wa zaka zapakati pa zisanu ndi makumi awiri ukhale masekeli makumi awiri ndipo munthu wamkazi ukhale masekeli khumi. Ngati ndi munthu wamwamuna wa pakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, mtengo wa munthu wamwamuna ukhale masekeli asanu a siliva ndipo ngati ndi wamkazi, ukhale masekeli atatu a siliva. Ngati ndi munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi kapena kuposerapo, mtengo wa wamwamuna ukhale masekeli khumi ndi asanu, ndipo wamkazi ukhale masekeli khumi. Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira.

“ ‘Ngati chimene anachitira lumbiro kuti apereke ndi nyama imene amapereka kukhala nsembe kwa Yehova, zonse zimene amapereka kwa Yehova nʼzopatulika. 10 Munthu asasinthanitse ndi ina kapena kupereka ina yabwino mʼmalo mwa yoyipa, kapena yoyipa mʼmalo mwa yabwino. Ngati asinthitsa nyama ina mʼmalo mwa ina, nyamayo pamodzi ndi inzake wasinthitsayo zikhala zopatulika. 11 Ngati chimene anachitira lumbiro ndi nyama yodetsedwa, nyama imene siloledwa kuyipereka kukhala nsembe kwa Yehova, nyamayo abwere nayo kwa wansembe, 12 ndipo wansembeyo atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 13 Ngati mwini wakeyo akufuna kuwombola nyamayo, awonjezere pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu zamtengowo.

14 “ ‘Ngati munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 15 Ngati munthu amene wapereka nyumbayo afuna kuyiwombola nyumbayo, awonjezere pamtengo wake wa nyumbayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ndipo nyumbayo idzakhalanso yake.

16 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova mbali ina ya malo a makolo ake, mtengo umene awuyike ukhale wolingana ndi mtengo wa mbewu zimene zimadzabzalidwamo. Zikhale mbewu za barele za makilogalamu makumi awiri ndipo mtengo wake ukhale masekeli makumi asanu. 17 Ngati munthu apereka munda wake kuyambira chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mtengo wake ukhale umene unakhazikitsidwa. 18 Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo. 19 Ngati munthu amene wapereka munda afuna kuwuwombola, ayenera kuwonjezera pa mtengo wake wa mundawo, limodzi mwa magawo asanu a mtengowo. Ndipo mundawo udzakhalanso wake. 20 Koma ngati sawuwombola mundawo, kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzawomboledwanso. 21 Mwini mundawo akawusiya mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu ndiye kuti mundawo udzakhala wopatulika monga woperekedwa kwa Yehova: udzakhala munda wa ansembe.

22 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova munda umene anagula, umene si malo a makolo ake, 23 wansembe atchule mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo monga ndalama zopatulika kwa Yehova. 24 Pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene anawugulitsayo, amene malowo anali ake. 25 Potchula mtengo uliwonse wansembe awerengere molingana ndi mtengo wa sekeli wa ku Nyumba ya Mulungu: magera makumi awiri pa sekeli imodzi.

26 “ ‘Koma pasapezeke munthu wopereka mwana woyamba kubadwa wa nyama, popeza mwana woyamba kubadwa ali kale wa Yehova, kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, zimenezi ndi za Yehova. 27 Ngati ili nyama yodetsedwa, ayiwombole pa mtengo umene wansembe wawuyika, ndi kuwonjezeranso pa mtengo wake wa nyamayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ngati sayiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe awuyike.

28 “ ‘Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu, nyama, kaya ndi malo a makolo, chimenechi chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Choperekedwa kwa Yehova motere nʼchopatulika kwambiri.

29 “ ‘Munthu amene waperekedwa kotheratu sangawomboledwe. Munthuyo ayenera kuphedwa.

30 “ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova. 31 Ngati munthu afuna kuwombola chakhumi chilichonse, awonjezere pamtengo wake chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo. 32 Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova. 33 Palibe amene adzaloledwa kusankha nyama yomwe ili yabwino kapena kusinthitsa. Ngati asinthitsa, nyamayo pamodzi ndi inzakeyo zidzakhala zopatulika ndipo sangaziwombole.’ ”

34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anamupatsa Mose pa Phiri la Sinai kuti awuze Aisraeli.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.