Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 11-13

Chakudya Choyeretsedwa ndi Chodetsedwa

11 Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.

“ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye. Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa.

“ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu. 11 Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu.

13 “ ‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 14 nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, 15 akhungubwi a mitundu yonse, 16 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi 17 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, dembo, 19 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.

20 “ ‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. 21 Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira. 22 Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. 23 Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu.

24 “ ‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 25 Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

26 “ ‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa. 27 Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28 Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.

29 “ ‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse, 30 gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe. 31 Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 32 Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa. 33 Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo. 34 Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa. 35 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa. 36 Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa. 37 Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino. 38 Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu.

39 “ ‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 40 Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

41 “ ‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya. 42 Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa. 43 Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa. 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.

46 “ ‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa. 47 Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’ ”

Kudziyeretsa kwa Mkazi Atabala Mwana

12 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe. Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha. Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.

“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake.

“ ‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”

Malamulo a Nthenda za pa Khungu Zopatsirana

13 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, “Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe. Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa. Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera. Koma ngati mʼbukowo ufalikira pakhungu atakadzionetsa kale kwa wansembe ndipo wansembeyo nʼkulengeza kuti munthuyo ndi woyeretsedwa, ndiye kuti apitenso kukadzionetsa kwa wansembeyo. Wansembe amuonetsetsenso munthuyo, ndipo ngati mʼbukowo wafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa ndi kuti nthendayo ndi khate.

“Ngati munthu aliyense ali ndi nthenda ya pakhungu yoyipitsa thupi, wodwalayo abwere naye kwa wansembe. 10 Wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati ali ndi chithupsa chamaonekedwe woyera pa khungupo chimene chasandutsa ubweya wa pamalopo kukhala woyera, ndipo ngati pali zilonda pa chotupacho, 11 limenelo ndi khate lachikhalire la pa khungu, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamutsekere munthu woteroyo pakuti ndi wodetsedwa kale.

12 “Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13 wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati khatero lagwira thupi lake lonse, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Popeza kuti thupi lonse lasanduka loyera, munthuyo ndi woyeretsedwa. 14 Koma pa tsiku limene zilonda zidzaoneka pa iye, munthuyo adzakhala wodetsedwa. 15 Wansembe aonetsetse zilondazo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zilondazo ndi zodetsedwa ndipo ili ndi khate. 16 Koma zilondazo zikasinthika ndi kusanduka zoyera, munthuyo ayenera kupita kwa wansembe. 17 Wansembe amuonetsetse ndipo ngati zilondazo zasanduka zoyera, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woyera ndipo adzakhala woyera ndithu.

18 “Ngati pa khungu la munthu wodwalayo pali chithupsa chimene chinapola kale, 19 ndipo pamalo pamene panali chithupsacho pakatuluka chotupa choyera kapena banga loyera mofiirira, munthuyo ayenera kukadzionetsa kwa wansembe. 20 Wansembe aonetsetse bwino ndipo ngati chikuoneka kuti chazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka woyera, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yatuluka mʼchithupsacho. 21 Koma ngati wansembe waonetsetsa napeza kuti palibe ubweya woyera ndipo chithupsacho sichinazame, koma chazimirira, wansembeyo amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 22 Ngati nthendayo ikufalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limeneli ndi khate. 23 Koma bangalo likakhala malo amodzi, wosafalikira, chimenecho ndi chipsera cha chithupsacho, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera.

24 “Munthu akakhala ndi bala lamoto pa khungu lake, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera, 25 wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu. 26 Koma ngati wansembe waonetsetsa balalo ndipo palibe ubweya woyera, ndipo ngati balalo silinazame ndi kuti lazirala, wansembe amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 27 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso wodwalayo, ndipo ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate. 28 Koma ngati bangalo likhala pa malo amodzi wosafalikira pa khungu, ndipo lazimirira, limenelo ndi thuza la bala lamoto, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Chimenecho ndi chipsera chamoto.

29 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena ku chibwano, 30 wansembe aonetsetse balalo ndipo likaoneka kuti lazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka wachikasu ndi wonyololoka, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zimenezo ndi mfundu zonyerenyetsa, khate lakumutu kapena ku chibwano. 31 Koma wansembe akaonetsetsa mfundu zonyerenyetsazo, ndipo zikaoneka kuti sizinazame ndi kuti palibe ubweya wakuda, wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku asanu ndi awiri. 32 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo, ndipo ngati sizinafalikire ndipo palibe ubweya wachikasu pamalopo ndiponso sizinazame, 33 wodwalayo ametedwe, koma pamene pali mfunduyo pasametedwe. Wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 34 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo ndipo ngati sizinafalikire pa khungu ndi kuti sizinazame, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Tsono achape zovala zake, ndipo adzakhala woyera. 35 Koma mfundu zonyerenyetsazo zikafalikira pa khungu, wansembe atalengeza kuti ndi woyera, 36 wansembe amuonetsetsenso wodwalayo ndipo ngati mfunduzo zafalikira pa khungu, iye asalabadirenso zoyangʼana ngati ubweya uli wachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37 Koma ngati wansembe waonetsetsa kuti mfunduzo sizinasinthe ndipo ubweya wakuda wamera pa mfundupo, ndiye kuti wodwalayo wachira. Tsono wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa.

38 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi mawanga woyera pa khungu, 39 wansembe aonetsetse mawangawo, ndipo ngati ali otuwa, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pa khungu. Munthuyo ndi woyera.

40 “Tsitsi la munthu likayoyoka kumutu ndiye kuti ndi dazi limenelo koma munthuyo ndi woyeretsedwa. 41 Ngati tsitsi lake layoyoka chapamphumi ndiye kuti ndi dazi la pa chipumi limenelo koma munthuyo ndi woyera. 42 Koma ngati pa dazi la pamutu kapena la pa chipumi pakhala chithupsa choyera mofiirira, ndiye kuti ndi khate limenelo lochokera mu dazi la pamutu lija kapena pa chipumi lija. 43 Tsono wansembe amuonetsetse wodwalayo ndipo ngati chithupsa cha pa dazi lapankhongo kapena pa dazi lapachipumicho ndi choyera mofiirira monga nthenda ya khate imaonekera, 44 ndiye kuti munthuyo ali ndi khate, motero ndi wodetsedwa. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha chithupsa cha pamutu pakepo.

45 “Munthu wa khate lotere avale sanza, tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wapamwamba ndipo azifuwula kuti, ‘Ndine wodetsedwa, ndine wodetsedwa!’ 46 Munthu wodwalayo adzakhala wodetsedwa kwa nthawi yonse imene ali ndi nthendayo. Iye ayenera kumakhala payekha kunja kwa msasa.

Malamulo a Nguwi ya pa Zovala

47 “Nsalu iliyonse ikakhala ndi nguwi, 48 kaya ndi chovala chopangidwa ndi nsalu yathonje kapena yaubweya, yoluka ndi thonje kapena ubweya, yachikopa kapena yopangidwa ndi chikopa, 49 ndipo ngati pamalo pamene pachita nguwiyo pali ndi maonekedwe obiriwira kapena ofiirira imeneyo ndi nguwi yoyipitsa chovala ndipo chovalacho chikaonetsedwe kwa wansembe. 50 Wansembeyo ayionetsetse nguwiyo ndipo chovalacho achiyike padera kwa masiku asanu ndi awiri. 51 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa. 52 Wansembe atenthe chovala chathonje kapena chaubweya chija, ngakhalenso chinthu chachikopa chija popeza nguwiyo yachidetsa. Nguwiyo ndi yoopsa choncho chinthucho achitenthe.

53 “Koma ngati wansembe akayangʼanitsitsa nguwiyo apeza kuti sinafalikire pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chachikopa, 54 iye alamulire kuti chinthu choyipitsidwacho achichape. Akatero achiyike padera kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 55 Chovalacho chitachapidwa, wansembe achionenso ndipo ngati nguwiyo sinasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti sinafalikire, chovalacho ndi chodetsedwa ndithu. Muchitenthe, ngakhale kuti nguwiyo ili kumbuyo kapena kumaso kwa chinthucho. 56 Koma ngati wansembe aonetsetsa nʼkupeza kuti nguwi ija yathimbirira pa chovala chija kapena pa chinthu chachikopa chija atachichapa, ndiye angʼambeko chinthucho pa banga la nguwiyo. 57 Koma ngati nguwiyo iwonekanso pa chovala chathonje kapena chaubweya ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Chilichonse chimene chili ndi nguwi chiyenera kutenthedwa. 58 Chovala chathonje kapena chaubweya, ngakhale chinthu china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachichapa nguwi yake nʼkuchoka muchichapenso kawiri ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”

59 Amenewa ndiwo malamulo a nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena pa chovala chathonje, kapenanso pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa kuti muzitha kulekanitsa choyeretsedwa ndi chodetsedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.