Beginning
Nsembe Zopsereza
1 26 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati, 2 “Aliyense wa inu ngati abwera ndi nsembe kwa Yehova kuchokera pa ziweto zake, choperekacho chikhale ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.
3 “ ‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire. 4 Munthuyo asanjike dzanja lake pa mutu pa nsembe yopserezayo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake. 5 Pambuyo pake aphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo ansembe, ana a Aaroni, atenge magazi ake ndi kuwawaza mbali zonse za guwa lansembe limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 6 Munthuyo asende nsembe yopserezayo ndi kuyidula nthulinthuli. 7 Ndipo ana a Aaroni, wansembe uja asonkhe moto pa guwa ndi kuyalapo nkhuni pa motopo. 8 Kenaka ana a Aaroni, wansembe uja, ayike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe pa nkhuni zimene zili paguwapo. 9 Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.
10 “ ‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema. 11 Ayiphere kumpoto kwa guwa, pamaso pa Yehova, ndipo ana a Aaroni amene ndi ansembe, awaze magazi ake mbali zonse za guwalo. 12 Kenaka ayidule nyamayo nthulinthuli, ndipo wansembe ayike nthulizo pa guwa, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo ayike zonsezi pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. 13 Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe abwere nazo zonse ndi kuzitentha pa guwa. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chotentha pa moto, fungo lokomera Yehova.
14 “ ‘Koma ngati chopereka kwa Yehova ndi nsembe yopsereza ya mbalame, ndiye ikhale njiwa kapena mawunda. 15 Wansembe abwere nayo ku guwa, ayidule mutu moyipotola ndi kutentha mutuwo pa guwa. Magazi ake awathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa. 16 Iye achotse chithokomiro pamodzi ndi nthenga zake zomwe ndi kuzitaya ku malo wotayirako phulusa, kummawa kwa guwalo. 17 Kenaka ayingʼambe pakati, koma asachotse mapiko. Ndipo wansembe ayiwotche pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, yowotcha pa moto ndiponso ya fungo lokomera Yehova.
Nsembe Zachakudya
2 “ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, 2 ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova. 3 Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
4 “ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. 5 Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. 6 Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya. 7 Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 8 Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa. 9 Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova. 10 Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
11 “ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. 12 Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. 13 Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.
14 “ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. 15 Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya. 16 Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.
Nsembe Yachiyanjano
3 “ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema. 2 Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo, ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ansembe, ana a Aaroni, awaze magazi mbali zonse za guwalo. 3 Pa nsembe yachiyanjanopo, ayenera kupatula zamʼkati mwa nyamayo ndi mafuta onse amene amakuta zamʼkati kupereka nsembe ya chakudya kwa Yehova. 4 Apatulenso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake omwe ndiponso mafuta okuta chiwindi amene achotsedwa pamodzi ndi impsyo zija. 5 Ndipo ana a Aaroni atenthe zimenezi pa guwa, pamwamba pa chopereka chopsereza chimene chili pa nkhuni zoyakazo. Imeneyi ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Yehova.
6 “ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, choperekacho chikhale nkhosa yayimuna kapena yayikazi yopanda chilema. 7 Ngati apereka nsembe ya mwana wankhosa, abwere naye pamaso pa Yehova. 8 Asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosayo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magaziwo mbali zonse za guwalo. 9 Pa nsembe yachiyanjanopo ayenera kuchotsa ndi kubweretsa: mafuta a nkhosayo, mchira wake wonse wonona atawudulira mʼtsinde pafupi ndi fupa la msana, zamʼkati zonse ndi mafuta onse amene akuta ziwalo zamʼkatimo, 10 impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta amene akuta impsyozo, msonga ya chiwindi imene idzachotsedwere limodzi ndi impsyozo. 11 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya chotentha pa moto choperekedwa kwa Yehova.
12 “ ‘Ngati munthuyo apereka mbuzi ngati nsembe, abwere nayo kwa Yehova. 13 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ana a Aaroni awaze magazi ake mbali zonse za guwa. 14 Tsono pa nsembe yoti iwotchedwe kukhala nsembe chakudya ya Yehova, achotse ndi kubweretsa: mafuta onse amene amaphimba zamʼkati kapena mafuta onse a mʼkatimo, 15 impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse omwe akuta impsyozo ndi msonga ya chiwindi imene adzachotsera pamodzi ndi impsyo zija. 16 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya cha Yehova, chowotcha pa moto ndiponso cha fungo lokomera Yehova. Mafuta onse ndi a Yehova.
17 “ ‘Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.’ ”
Nsembe Yopepesera Tchimo
4 Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa ndi kuchita chilichonse chimene Yehova walamula kuti asachite, azichita izi:
3 “ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake. 4 Wansembeyo abwere nayo ngʼombeyo pa khomo la tenti ya msonkhano pamaso pa Yehova. Asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo ndipo ayiphe pamaso pa Yehova. 5 Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 6 Iye aviyike chala chake mʼmagazi, ndipo awawaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani yotchinga malo wopatulika. 7 Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 8 Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo. 9 Achotsenso ndi kubwera ndi impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta onse ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi ndi impsyo 10 monga momwe amachotsera mafuta a ngʼombe yoperekedwa kuti ikhale chopereka chachiyanjano. Tsono wansembe atenthe zimenezi pa guwa lansembe zopsereza. 11 Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo, 12 kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.
13 “ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu. 14 Akazindikira tchimo limene achita, gulu lonse lipereke mwana wangʼombe wamphongo kuti akhale chopereka chopepesera tchimo ndipo abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 15 Akuluakulu a anthuwo asanjike manja awo pa mutu pa ngʼombe pamaso pa Yehova, ndipo ayiphe pomwepo pamaso pa Yehova. 16 Tsono wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano. 17 Aviyike chala chake mʼmagaziwo ndi kuwawaza pamaso pa Yehova kasanu ndi kawiri patsogolo pa nsalu yotchinga. 18 Pambuyo pake iye apake magaziwo pa nyanga za guwa limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 19 Kenaka achotse mafuta onse a ngʼombeyo ndi kuwatentha pa guwa, 20 ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa. 21 Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse.
22 “ ‘Ngati mtsogoleri achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova Mulungu wake, ndiye kuti wapalamula. 23 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, iye abwere ndi mbuzi yayimuna yopanda chilema kuti ikhale chopereka chake. 24 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mbuziyo ndi kuyiphera pamalo pamene amaphera zopereka zopsereza pamaso pa Yehova. Ichi ndi chopereka chopepesera tchimo. 25 Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a chopereka chopepesera tchimocho ndi chala chake, ndipo awapake pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Athire magazi otsalawo pa tsinde la guwalo. 26 Wansembeyo atenthe mafuta onse pa guwapo monga amatenthera chopereka chachiyanjano. Pochita zimenezi, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo, ndipo adzakhululukidwa.
27 “ ‘Ngati munthu wamba achimwa mosadziwa nachita zimene ndi zoletsedwa ndi Yehova, ndiye kuti wapalamula. 28 Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo. 29 Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo ndipo ayiphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 30 Ndipo wansembe atenge magazi ndi chala chake ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza ndi kuthira magazi wotsalawo pa tsinde la guwalo. 31 Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.
32 “ ‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema. 33 Asanjike dzanja lake pa mutu wa mwana wankhosayo ndipo amuphe pamalo pamene amaphera chopereka chopsereza. 34 Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo. 35 Iye achotse mafuta onse, monga amachotsera mafuta a mwana wankhosa wa chopereka chachiyanjano, ndipo wansembe awatenthe pa guwa pamodzi ndi zopereka zina zopsereza za Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo limene munthuyo anachita ndipo adzakhululukidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.