Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 22-24

Za Kuteteza Katundu

22 “Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi.

“Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe. Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha.

“Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.

“Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho.

“Ngati munthu alekerera ziweto zake kukalowa mʼmunda wa munthu wina kukadya mbewu zake, munthuyo amubwezere mwini mundawo mbewu zina zabwino kapena mpesa wina wabwino kwambiri.

“Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire.

“Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho. Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo. Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri.

10 “Ngati munthu wina anasungitsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa, kapena chiweto chilichonse ndipo chiweto chija nʼkufa kapena kupweteka kapena kutengedwa popanda wina kuona, 11 ndiye kuti anthu awiriwo ayenera kulumbira pamaso pa Mulungu kuti asatenge chinthu cha mnzake. Zikatero mwini katundu uja avomereze zimenezi ndipo asabwezeredwe kanthu. 12 Koma ngati chiwetocho chinabedwa, iye ayenera kubwezera mwini wakeyo. 13 Ngati chinagwidwa ndi zirombo, iye ayenera kubweretsa zotsalira ngati umboni ndipo sadzalipira kanthu.

14 “Ngati munthu abwereka chiweto cha mnzake ndipo chiweto chija nʼkuvulala kapena kufa chikanali ndi iyebe, wobwerekayo ayenera kulipira. 15 Koma ngati mwini wakeyo ali ndi chiwetocho, wobwerekayo sadzalipira. Ngati anapereka ndalama pobwereka chiwetocho, ndalama anaperekazo zilowa mʼmalo mwa chiweto chakufacho.

Malamulo a Kakhalidwe ka Anthu

16 “Ngati munthu anyenga namwali wosadziwa mwamuna amene sanapalidwe ubwenzi ndi kugona naye, munthuyo ayenera kulipira malowolo ndipo adzakhala mkazi wake. 17 Ngati abambo ake akanitsitsa kwamtuwagalu kumupereka kuti amukwatire, munthuyo aperekebe malowolo woyenera namwaliyo.

18 “Musayilole mfiti yayikazi kuti ikhale ndi moyo.

19 “Aliyense wogonana ndi chiweto ayenera kuphedwa.

20 “Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe.

21 “Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto.

22 “Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. 23 Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo. 24 Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.

25 “Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja. 26 Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe 27 chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo.

28 “Musachite chipongwe Mulungu wanu kapena kutemberera mtsogoleri wa anthu anu.

29 “Musachedwe kupereka kwa Ine zokolola zanu zochuluka ndi vinyo wanu wochuluka.

“Mundipatse ana anu achisamba aamuna. 30 Muchite chimodzimodzi ndi ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwa azikhala ndi amayi ake masiku asanu ndi awiri. Koma pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo muzimupereka kwa Ine.

31 “Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.”

Malamulo a Zachilungamo ndi Zachifundo

23 “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.

“Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri. Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.

“Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza.

“Usakhotetse milandu ya anthu osauka. Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.

“Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.

“Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.

Malamulo a Nthawi Zopuma

10 “Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. 11 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.

12 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.

13 “Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.

Masiku Atatu Akulu a Chikondwerero

14 “Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.

15 “Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto.

“Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja.

16 “Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda.

“Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda.

17 “Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka.

18 “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti.

“Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.

19 “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu.

“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.

Kutsogolera kwa Mngelo wa Mulungu

20 “Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza. 21 Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa. 22 Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu. 23 Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo. 24 Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo. 25 Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu. 26 Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali.

27 “Ine ndidzawachititsa mantha ndi kusokoneza anthu onse amene adzalimbana ndi inu ndipo adani anu onse adzakuthawani. 28 Ahivi, Akanaani ndi Ahiti adzathawa ngati kuti ndawatumizira mavu. 29 Komabe sindidzawachotseratu onse mʼchaka chimodzi chifukwa dziko lingadzakhale lopanda anthu ndipo nyama zakuthengo zidzakuchulukirani. 30 Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo.

31 “Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa. 32 Musachite pangano ndi iwo kapena ndi milungu yawo. 33 Asadzakhale mʼdziko lanu chifukwa angadzakuchimwitseni ndi kuyamba kupembedza milungu yawo. Mukadzatero ndiye kuti mwakodwa mu msampha.”

Kutsimikizira kwa Pangano

24 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali. Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.”

Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena.

Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano. Mose anatenga theka la magazi ndi kuyika mʼmbale, ndipo theka linalo analiwaza pa guwa lansembe. Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.”

Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.”

Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri, 10 ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo. 11 Ngakhale anaona Yehova koma sanafe, mʼmalo mwake anadya ndi kumwa.

12 Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”

13 Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa. 14 Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”

15 Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. 16 Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo. 17 Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo. 18 Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.