Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 16-18

Mana ndi Zinziri

16 Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai. Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”

Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?” Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”

Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”

10 Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.

11 Yehova anati kwa Mose, 12 “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

13 Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. 14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. 15 Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe.

Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye. 16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ”

17 Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa. 18 Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya.

19 Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.”

20 Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.

21 Mmawa uliwonse aliyense amatola zimene amazifuna, ndipo dzuwa likatentha zimasungunuka. 22 Tsiku lachisanu ndi chimodzi anatuta malita anayi munthu aliyense, ndipo atsogoleri a mpingo wonse anabwera kudzawuza Mose za zimenezi. 23 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ”

24 Choncho anasunga mpaka mmawa monga Mose anawalamulira, ndipo sananunkhe kapena kuchita mphutsi. 25 Mose anati, “Idyani lero chifukwa lero ndi Sabata la Yehova. Lero simukapeza chilichonse kunjaku. 26 Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.”

27 Komabe anthu ena anapita kuti akatole chakudya tsiku lachisanu ndi chiwiri, koma sanapeze kanthu. 28 Ndipo Yehova anafunsa Mose nati, “Kodi inu muzipitirira kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti? 29 Taonani, popeza Yehova wakupatsani Sabata nʼchifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi amakupatsani chakudya cha masiku awiri. Aliyense azikhala pamene ali pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, pasapezeke wotuluka kunja.” 30 Kotero anthu anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri.

31 Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi. 32 Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”

33 Choncho Mose anati kwa Aaroni, “Tenga mtsuko ndipo uyikemo malita awiri a mana. Ndipo uyike manawo pamaso pa Yehova kusungira mibado imene ikubwera.”

34 Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike. 35 Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani.

36 (Malita awiri amafanana ndi gawo lakhumi la efa).

Madzi Otuluka Mʼthanthwe

17 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.”

Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”

Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”

Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”

Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”

Aisraeli Agonjetsa Aamaleki

Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli. Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”

10 Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri. 11 Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana. 12 Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa. 13 Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga.

14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”

15 Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi). 16 Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.”

Yetero Abwera Kudzaona Mose

18 Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.

Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”

Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa. Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”

Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.

Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. 10 Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. 11 Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.” 12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

13 Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. 14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”

15 Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. 16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”

17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.”

24 Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. 25 Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. 26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.

27 Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.