Beginning
Manase ndi Efereimu
48 Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo. 2 Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.
3 Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa, 4 nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’
5 “Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni. 6 Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo. 7 Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).
8 Israeli ataona ana a Yosefe anafunsa kuti, “Anyamatawa ndi a yani?”
9 Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.”
Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.”
10 Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira.
11 Israeli anati kwa Yosefe, “Ine sindinali kuyembekeza kuti nʼkudzaonanso nkhope yako, ndipo tsopano Mulungu wandilola kuti ndionenso ngakhale ana ako.”
12 Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi. 13 Yosefe anawagwira ana onse awiri padzanja, Efereimu ku dzanja lake lamanja kulunjika dzanja lamanzere la Israeli ndipo Manase ku dzanja lamanzere kulunjikitsa dzanja lamanja la Israeli, ndipo anawayandikiza kwa Yakobo. 14 Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.
15 Kenaka anadalitsa Yosefe nati,
“Mulungu amene makolo anga
Abrahamu ndi Isake anamutumikira,
Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wanga
moyo wanga wonse kufikira lero,
16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse,
ameneyo adalitse anyamata awa.
Kudzera mwa iwowa
dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka.
Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu
pa dziko lapansi.”
17 Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, 18 nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”
19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” 20 Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati,
“Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati:
Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.”
Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.
21 Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. 22 Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”
Yakobo Adalitsa Ana ake Aamuna
49 Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.
2 “Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo;
mverani abambo anu Israeli.
3 “Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa;
mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga,
wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
4 Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana,
iwe unagona pa bedi la abambo ako,
ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.
5 “Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo,
anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.
6 Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri,
kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo,
pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo
ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
7 Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi
ndi ukali wawo wankhanza choterewu!
Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo
ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.
8 “Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda;
dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako;
abale ako adzakugwadira iwe.
9 Yuda ali ngati mwana wa mkango;
umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga.
Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi,
ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
10 Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda,
udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse,
mpaka mwini wake weniweni atabwera
ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
11 Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa,
ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino.
Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo;
ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
12 Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo,
mano ake woyera chifukwa cha mkaka.
13 “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja;
adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi;
malire ake adzafika ku Sidoni.
14 “Isakara ali ngati bulu wamphamvu
wogona pansi pakati pa makola.
15 Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira
ndi kukongola kwa dziko lake,
iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake
ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.
16 “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake
monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.
17 Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu,
songo yokhala mʼnjira
imene imaluma chidendene cha kavalo
kuti wokwerapoyo agwe chagada.
18 “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.
19 “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo,
koma iye adzawathamangitsa.
20 “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma,
ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.
21 “Nafutali ali ngati mbawala yayikazi
yokhala ndi ana okongola kwambiri.
22 “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso,
mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe,
nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
23 Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza;
anamuthamangitsa ndi mauta awo.
24 Koma uta wake sunagwedezeke,
ndi manja ake amphamvu aja analimbika,
chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo,
chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
25 Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza;
chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa
ndi mvula yochokera kumwamba,
ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,
ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
26 Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa
madalitso a mapiri akale
oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona.
Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe,
pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.
27 “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa;
umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha,
ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”
28 Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.
Kumwalira kwa Yakobo
29 Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30 Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32 Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”
33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.
50 Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. 2 Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. 3 Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.
4 Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, 5 ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”
6 Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”
7 Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. 8 Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni 9 Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.
10 Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.
12 Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14 Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.
Yosefe Abwereza Kutsimikizira Abale Ake
15 Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?” 16 Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: 17 ‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
18 Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”
19 Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu? 20 Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri. 21 Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.
Kumwalira kwa Yosefe
22 Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 23 ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.
24 Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.” 25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
26 Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.