Beginning
Yakobo Abwerera ku Beteli
35 Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”
2 Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu. 3 Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” 4 Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu. 5 Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.
6 Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani. 7 Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake.
8 Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro).
9 Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa. 10 Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli.
11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu. 12 Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.” 13 Kenaka Mulungu anamusiya Yakobo.
14 Yakobo anayika mwala wachikumbutso pa malo pamene Mulungu anayankhula naye paja. Iye anathirapo nsembe yachakumwa ndi yamafuta. 15 Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli.
Imfa ya Isake ndi Rakele
16 Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka. 17 Akanali chivutikire choncho, mzamba anamulimbikitsa nati, “Usaope pakuti ubala mwana wina wamwamuna.” 18 Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.
19 Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu). 20 Pa manda ake, Yakobo anayimika mwala wachikumbutso wa pa manda ndipo ulipobe mpaka lero.
21 Israeli (Yakobo) anasunthanso nakamanga tenti yake kupitirira nsanja ya Ederi. 22 Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi.
Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:
23 Ana a Leya ndi awa:
Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo,
Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.
24 Ana a Rakele ndi awa:
Yosefe ndi Benjamini.
25 Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa:
Dani ndi Nafutali.
26 Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa:
Gadi ndi Aseri.
Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu.
27 Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale. 28 Isake anakhala ndi moyo zaka 180. 29 Anamwalira ali wokalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ndipo ana ake Esau ndi Yakobo anamuyika mʼmanda.
Zidzukulu za Esau
36 Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:
2 Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi 3 ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.
4 Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; 5 ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.
6 Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. 7 Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. 8 Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.
9 Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.
10 Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau:
Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.
11 Awa ndi mayina a ana a Elifazi:
Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.
12 Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.
13 Awa ndi ana a Reueli:
Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.
14 Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa:
Yeusi, Yolamu ndi Kora.
15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau:
Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa:
Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, 16 Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.
17 Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa:
Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.
18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa:
Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.
19 Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.
20 Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo:
Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 21 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.
22 Ana aamuna a Lotani anali awa:
Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
23 Ana aamuna a Sobala anali awa:
Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa:
Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.
25 Ana a Ana anali:
Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.
26 Ana aamuna a Disoni anali awa:
Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.
27 Ana aamuna a Ezeri anali awa:
Bilihani, Zaavani ndi Akani.
28 Ana aamuna a Disani anali awa:
Uzi ndi Arani.
29 Mafumu a Ahori anali awa:
Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 30 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.
Mafumu a ku Edomu
31 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
32 Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
33 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
34 Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.
35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
36 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.
37 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.
38 Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
39 Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
40 Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa:
Timna, Aliva, Yeteti, 41 Oholibama, Ela, Pinoni, 42 Kenazi, Temani, Mibezari, 43 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo.
Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.
Maloto a Yosefe
37 Yakobo ankakhala mʼdziko la Kanaani kumene abambo ake ankakhala.
2 Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi:
Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.
3 Tsono Israeli ankakonda Yosefe koposa ana ake ena onse, chifukwa anali mwana wobadwa muukalamba wake. Ndipo anamusokera mkanjo wa manja aatali. 4 Pamene abale ake anaona kuti abambo awo ankakonda Yosefe kuposa aliyense wa iwo, anayamba kumuda Yosefe ndipo sankayankhula naye zamtendere.
5 Tsiku lina Yosefe analota maloto ndipo pamene anawuza abale ake za malotowo, iwo anawonjeza kumuda. 6 Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota: 7 Ife timamanga mitolo ya tirigu ku munda ndipo mwadzidzidzi mtolo wanga unayimirira chilili, pamene mitolo yanu inazungulira mtolo wangawo nʼkumawugwadira.”
8 Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo.
9 Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.”
10 Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?” 11 Abale ake anamuchitira nsanje, koma abambo ake anasunga nkhaniyi mu mtima.
Yosefe Agulitsidwa ndi Abale Ake
12 Tsono abale ake anapita kukadyetsa ziweto za abambo awo ku Sekemu, 13 ndipo Israeli anati kwa Yosefe, “Tsono, ndikufuna kukutuma kwa abale ako.”
Iye anayankha nati, “Chabwino.”
14 Choncho anati kwa iye, “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso nkhosa ngati zili bwino. Kenaka ubwere udzandiwuze.” Choncho Israeli anatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni.
Yosefe atafika ku Sekemu, 15 munthu wina anamupeza akungozungulirazungulira mʼmunda ndipo anamufunsa, “Ukufunafuna chiyani?”
16 Iye anayankha, “Ndikufuna abale anga. Mungandiwuze kumene akudyetsa ziweto zawo?”
17 Munthuyo anayankha nati, “Anasamukako kuno. Ndinawamva akuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’ ”
Choncho Yosefe analondola abale ake ndipo anakawapeza ku Dotani. 18 Abale ake aja anamuonera patali. Ndipo asanafike nʼkomwe kumene kunali iwo kuja, anayamba kale kumupangira chiwembu choti amuphe.
19 Iwo anawuzana nati, “Uyo akubwera apo wamaloto uja. 20 Tsono tiyeni timuphe ndi kuponya thupi lake mu chimodzi mwa zitsime izi ndipo tidzati anadyedwa ndi nyama zakuthengo zolusa. Tsono timuonera zomwe ziti zichitike ndi maloto ake aja.”
21 Koma Rubeni atamva izi, anapulumutsa Yosefe. Iye anati kwa abale ake, “Ayi, tisamuphe, 22 tisakhetse magazi. Tiyeni timuponye mʼchitsime ku chipululu konkuno. Koma tisamuvulaze nʼkomwe. Rubeni ananena zonsezi kuti apulumutse Yosefe ndi kuti pambuyo pake akamupereke kwa abambo awo.”
23 Choncho Yosefe atafika kwa abale ake, iwo anamuvula mkanjo wake wamanja aatali uja umene anavala 24 ndipo anamutenga namuponya mʼchitsime chopanda madzi komanso mopanda chilichonse.
25 Atakhala pansi kuti adye chakudya, anatukula maso naona gulu la Aismaeli akubwera kuchokera ku Giliyadi. Ngamira zawo zinanyamula zonunkhiritsa bwino zakudya zamitundumitundu, ndipo zimenezi ankapita nazo ku Igupto.
26 Yuda anafunsa abale ake nati, “Kodi tidzapindula chiyani tikapha mʼbale wathuyu ndi kuphimbitsa magazi ake? 27 Bwanji timugulitse kwa Aismaeliwa, koma ife tisamuchite kanthu kalikonse. Ameneyu ndi mʼbale wathu thupi limodzi ndi ife.” Abale ake anavomereza zimenezi.
28 Amalonda ena a ku Midiyani ankadutsa pomwepo. Tsono abale ake a Yosefe anamutulutsa Yosefe uja mu chitsime chija ndipo anamugulitsa kwa Aismaeli aja pamtengo wa masekeli makumi awiri. Choncho anapita naye Yosefe ku Igupto.
29 Rubeni atabwerera ku chitsime kuja anapeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo. Pamenepo iye anangʼamba zovala zake 30 nabwerera kwa abale ake nati, “Mnyamata uja mulibemo! Nanga ndilowere kuti ine tsopano?”
31 Tsono anapha kamwana ka mbuzi, natenga mkanjo wa Yosefe ndi kuwunyika mʼmagazi ake. 32 Iwo anatenga mkanjo uja nabwerera nawo kwa abambo awo nati, “Ife tapeza mkanjowu. Tawuyangʼanitsitsani muone ngati uli wa mwana wanu.”
33 Iye anawuzindikira ndipo anati, “Ndi mkanjo wa mwana wanga umenewu! Nyama yakuthengo yolusa yamudya. Mosakayika, mwana wanga Yosefe wakhadzulidwa.”
34 Pamenepo Yakobo anangʼamba zovala zake, navala chisaka mʼchiwuno mwake. Iye analira maliro a mwana wake masiku ambiri. 35 Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake.
36 Amidiyani aja anagulitsa Yosefe kwa Potifara, mmodzi mwa nduna za Farao ku Igupto. Potifarayu anali mkulu wa asilikali olonda nyumba ya Farao.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.