Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 27-29

Yakobo Alandira Madalitso kwa Isake

27 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.”

Iye anayankha, “Ine abambo.”

Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa. Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama. Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”

Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama, Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti, ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera. 10 Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”

11 Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala. 12 Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”

13 Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”

14 Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera. 15 Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo. 16 Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi. 17 Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.

18 Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.”

Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”

19 Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”

20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?”

Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”

21 Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”

22 Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.” 23 Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa. 24 Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?”

Yakobo anayankha, “Inde ndine.”

25 Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.”

Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa. 26 Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”

27 Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati,

“Haa, fungo la mwana wanga
    lili ngati fungo la munda
    umene Yehova waudalitsa.
28 Mulungu akugwetsere mame akumwamba
    ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
    ndi vinyo watsopano.
29 Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
    ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
    ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
    ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”

30 Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja. 31 Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”

32 Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?”

Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”

33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”

34 Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”

35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”

36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”

37 Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”

38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.

39 Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti,

“Malo ako okhalapo
    sadzabala dzinthu,
    ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.
40 Udzakhala ndi moyo podalira lupanga
    ndipo udzatumikira mʼbale wako.
Koma idzafika nthawi
    pamene udzakhala mfulu
    udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”

Yakobo Athawira kwa Labani

41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”

42 Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire. 43 Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. 44 Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika. 45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”

46 Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”

28 Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani. Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu. Mulunguyo akudalitse iwe monga mmene anamudalitsira Abrahamu kuti zidzukulu zako zidzalandira dziko limene ukukhalamo ngati mlendo kuti lidzakhale lawo. Ili ndi dziko limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu.” Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau.

Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.” Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu. Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani; anapita kwa Ismaeli mwana wa Abrahamu nakwatira Mahalati mwana wa Ismaeli, mlongo wake wa Nebayoti. Anatero kuwonjezera akazi amene anali nawo kale.

Maloto a Yakobo pa Beteli

10 Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani. 11 Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona. 12 Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo. 13 Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo. 14 Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. 15 Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”

16 Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.” 17 Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

18 Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake 19 Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi.

20 Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; 21 ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga, 22 ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”

Yakobo Afika ku Padanaramu

29 Yakobo anapitiriza ulendo wake kupita ku dziko la anthu a kummawa. Atafika kumeneko anaona chitsime ku busa ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pafupi ndi chitsimecho chifukwa nkhosazo zimamwetsedwa madzi ochokera mʼchitsimecho. Pamwamba pa chitsimecho panali mwala waukulu. Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo.

Yakobo anafunsa abusawo kuti, “Abale anga, mwachokera kuti?”

Iwo anayankha, “Tachokera ku Harani.”

Iye anawafunsanso kuti, “Kodi Labani, mdzukulu wa Nahori mukumudziwa?”

Iwo anayankha, “Inde tikumudziwa?”

Ndipo Yakobo anawafunsanso, “Kodi ali bwino?”

Iwo anati, “Inde ali bwino. Nayu Rakele mwana wake akubwera apoyu ndi nkhosa.”

Iye anati, “Taonani, dzuwa likanalipo ndipo nthawi yosonkhanitsa nkhosa sinakwane. Bwanji osazimwetsa madzi nkhosazi.”

Iwo anayankha, “Ayi sitingatero. Tidikira mpaka nkhosa zonse zisonkhane. Zikatero, tigubuduza mwalawu kuwuchotsa pamwamba pa chitsimepo, kenaka nʼkuzimwetsa madzi nkhosazo.”

Ali chiyankhulire nawo, Rakele anafika ndi nkhosa za abambo ake popeza ndiye amene ankaweta nkhosazo. 10 Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo. 11 Kenaka Yakobo anapsompsona Rakele nayamba kulira mokweza. 12 Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake.

13 Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika. 14 Ndipo, Labani anati kwa iye, “Iwe ndiwe ndithu fupa ndi mnofu wanga.”

Yakobo Akwatira Leya ndi Rakele

Yakobo anakhala ndi Labani mwezi umodzi. 15 Tsono Labani anawuza Yakobo kuti, “Zoona iwe ndi ife ndi abale. Koma suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro. Ndiwuze kuti malipiro ako azikhala wotani?”

16 Tsono Labani anali ndi ana aakazi awiri; dzina la wamkulu linali Leya, ndipo dzina la wamngʼono linali Rakele. 17 Leya anali ndi maonekedwe wofowoka koma Rakele anali wa maonekedwe wokongola kwambiri. 18 Yakobo anakonda Rakele ndipo anati, “Ndidzakugwirirani ntchito kwa zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha mwana wanu wamngʼono, Rakele.”

19 Labani anati, “Kuli bwino kuti ndimupereke kwa iwe ameneyu kusiyana ndi munthu wina. Khala ndi ine kuno.” 20 Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele.

21 Kenaka Yakobo anati kwa Labani, “Nthawi yanga ndakwanitsa, ndipatseni mwana wanu kuti ndimukwatire.”

22 Pamenepo Labani anakonza phwando la ukwati, nayitana anthu onse a pamalopo. 23 Koma pokwana usiku, Labani anatenga mwana wake wamkazi Leya namupatsa Yakobo, ndipo Yakobo anagona naye. 24 Ndipo Labani anapereka wantchito wake wamkazi Zilipa kwa Leya kuti akhale wantchito wake.

25 Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?”

26 Labani anayankha, “Si mwambo wathu kuno kupereka wamngʼono ku banja, wamkulu asanakwatiwe. 27 Yamba watsiriza sabata ya chikondwerero cha ukwati wa Leya; kenaka ndidzakupatsanso Rakele. Koma udzayenera kundigwirira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri.”

28 Yakobo anachitadi momwemo. Anamaliza sabata ya chikondwerero cha Leya, ndipo Labani anamupatsa Rakele kuti akhale mkazi wake. 29 Labani anapereka wantchito wake wamkazi Biliha kwa Rakele kuti akhale wantchito wake. 30 Yakobo analowana ndi mkazi wake Rakele, ndipo Yakobo anakonda Rakele kuposa Leya. Ndipo anamugwirira ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele.

Ana a Yakobo

31 Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala. 32 Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.”

33 Anakhalanso ndi pathupi ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Yehova anamva kuti mwamuna wanga sakundikonda, choncho wandipatsanso mwana winayu.” Ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.

34 Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi.

35 Anatenganso pathupi pena, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna, iye anati, “Nthawi ino ndidzalemekeza Yehova.” Choncho anamutcha Yuda. Kenaka analeka kubereka.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.