Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 25-26

Abrahamu Amwalira

25 Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura. Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.

Abrahamu anasiyira Isake chilichonse anali nacho. Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.

Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. Abrahamu anamwalira atakalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti, 10 uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara. 11 Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).

Ana Aamuna a Ismaeli

12 Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu.

13 Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 14 Misima, Duma, Masa, 15 Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; 16 Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. 17 Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 18 Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.

Yakobo ndi Esau

19 Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu.

Abrahamu anabereka Isake 20 ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu.

21 Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi. 22 Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.

23 Yehova anati kwa iye,

“Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana,
    ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana;
fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake,
    ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”

24 Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. 26 Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.

27 Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba. 28 Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.

29 Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala. 30 Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).

31 Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.”

32 Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?”

33 Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.

34 Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita.

Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.

Isake ndi Abimeleki

26 Tsono kunagwa njala ina mʼdzikomo kuwonjezera pa ija ya poyamba ya nthawi ya Abrahamu ndipo Isake anapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo. Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako. Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa Abrahamu anandimvera, nasunga malamulo anga onse.” Choncho Isake anakhala ku Gerari.

Anthu akumaloko atafunsa Isake za mkazi wake, iye anati, “Ndi mlongo wanga ameneyu.” Iye anaopa kunena kuti, “Ndi mkazi wanga ameneyu,” popeza ankaganiza kuti anthu akumeneku akhoza kumupha ndi kukwatira mkazi wake popeza Rebeka anali wokongola.

Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake. Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?”

Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”

10 Tsono Abimeleki anati, “Nʼchiyani chimene watichitira? Mmodzi mwa anthuwa anatsala pangʼono kugona ndi mkazi wako ndipo ukanatisandutsa ife kukhala olakwa.”

11 Choncho Abimeleki analamula anthu ake onse nati, “Aliyense amene avutitse munthu uyu pamodzi ndi mkazi wake adzaphedwa ndithu.”

12 Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa. 13 Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. 14 Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje. 15 Nthawi iyi nʼkuti Afilisti atakwirira ndi dothi zitsime zonse zimene antchito abambo ake Abrahamu anakumba mu nthawi ya abambo akewo.

16 Ndipo Abimeleki anati kwa Isake, “Muchoke pakati pathu chifukwa mwasanduka wamphamvu kuposa ife.”

17 Choncho Isake anachokako kumeneko nakakhala ku chigwa cha Gerari kumene anakhazikikako. 18 Isake anafukulanso zitsime zija zimene zinakumbidwa mu nthawi ya abambo ake Abrahamu. Atamwalira Abrahamu, Afilisti anakwirira zitsimezi. Tsono anazitcha mayina omwewo amene abambo ake anazitcha.

19 Antchito a Isake anakumba mʼchigwamo ndipo anapezamo kasupe wa madzi. 20 Koma abusa a ku Gerari anakangana ndi abusa a Isake nati, “Madziwa ndi athu.” Motero iye anachitcha chitsimecho Mkangano chifukwa anakangana naye. 21 Kenaka iwo anakumba chitsime china, koma anakangananso chifukwa cha chitsimecho. Choncho anachitcha dzina lakuti Chidani. 22 Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.”

23 Kenaka Isake anachoka ku malo kuja kupita ku Beeriseba. 24 Usiku umenewo Yehova anadza kwa Isake nati, “Ine ndine Mulungu wa abambo ako Abrahamu. Usachite mantha popeza Ine ndili ndi iwe. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.”

25 Isake anamanga guwa lansembe pamenepo ndipo anapembedza Yehova. Pomwepo anamanga tenti yake, ndipo antchito ake anakumba chitsime.

26 Abimeleki pamodzi ndi Ahuzati mlangizi wake ndi Fikolo mkulu wa ankhondo ake anabwera kwa Isake kuchokera ku Gerari. 27 Tsopano Isake anawafunsa kuti, “Bwanji mwabwera kwa ine, popeza munandichitira nkhanza ndi kundithamangitsa?”

28 Iwo anayankha, “Tsopano tadziwa kuti Yehova anali ndi iwe; ndiye taganiza kuti inu ndi ife tichite lumbiro. Ife tichite pangano ndi inu 29 kuti inu simudzatichitira zoyipa monga ifenso sitinakuchitireni nkhondo. Ife tinakuchitirani zabwino zokhazokha, ndipo tinakulolani kuti musamuke kuchoka kwathu mu mtendere. Tsopano Yehova wakudalitsani.”

30 Tsono Isake anawakonzera phwando, ndipo anadya ndi kumwa. 31 Mmawa wake aliyense analumbira pangano kwa mnzake. Tsono Isake anawalola kuti anyamuke ndipo anamusiya mu mtendere.

32 Tsiku limenelo, antchito a Isake anabwera namuwuza za chitsime chimene anakumba. Iwo anati, “Tawapeza madzi!” 33 Iye chitsimecho anachitcha Pangano. Nʼchifukwa chake mzindawu umatchedwa Beeriseba mpaka lero.

34 Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti. 35 Akazi awiriwa anasandutsa Isake ndi Rebeka kukhala ndi moyo wa madandawulo nthawi zonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.