Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 8-11

Nowa Atuluka Mʼchombo

Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera.

Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. 10 Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. 11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. 12 Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.

13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. 14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.

15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”

18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.

20 Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza. 21 Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.

22 “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire,
nthawi yodzala ndi nthawi yokolola
yozizira ndi yotentha,
dzinja ndi chilimwe,
usana ndi usiku,
sizidzatha.”

Pangano la Mulungu ndi Nowa

Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi. Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire. Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse.

“Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda. Aliyense wopha munthu adzaphedwa, nyama iliyonse yopha munthu idzaphedwa, munthu aliyense wopha munthu mnzake, adzaphedwa.

“Aliyense wopha munthu,
    adzaphedwanso ndi munthu;
pakuti Mulungu analenga munthu
    mʼchifanizo chake.

Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.”

Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, “Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, 10 pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. 11 Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”

12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo. 13 Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi. 14 Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka, 15 ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi. 16 Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”

17 Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”

Ana Aamuna a Nowa

18 Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. 19 Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi.

20 Nowa anali munthu woyamba kulima munda wamphesa. 21 Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche. 22 Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja. 23 Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.

24 Nowa atadzuka, kuledzera kutatha, ndikudziwa zimene mwana wake wamngʼono wamwamuna uja anamuchitira, 25 anati,

“Atembereredwe Kanaani!
    Adzakhala kapolo
    wa pansi kwenikweni kwa abale ake.”

26 Anatinso,

“Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu!
    Kanaani akhale kapolo wa Semu.
27 Mulungu akulitse dziko la Yafeti;
    Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu,
    ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.”

28 Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. 29 Anamwalira ali ndi zaka 950.

Mndandanda wa Mitundu ya Anthu

10 Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.

Banja la Yafeti

Ana aamuna a Yafeti anali:

Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.

Ana aamuna a Gomeri anali:

Asikenazi, Rifati ndi Togarima.

Ana aamuna a Yavani anali:

Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).

Banja la Hamu

Ana aamuna a Hamu anali:

Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.

Ana aamuna a Kusi anali:

Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka.

Ana aamuna a Raama anali:

Seba ndi Dedani.

Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” 10 Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. 11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, 12 ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.

13 Igupto ndiye kholo la

Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 14 Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).

15 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,

Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; 16 Ayebusi, Aamori, Agirigasi; 17 Ahivi, Aariki, Asini, 18 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, 19 mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.

20 Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.

Banja la Semu

21 Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.

22 Ana aamuna a Semu anali:

Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.

23 Ana aamuna a Aramu anali:

Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.

24 Aripakisadi anabereka Sela,

ndipo Selayo anabereka Eberi.

25 A Eberi anabereka ana aamuna awiri:

Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.

26 Yokitani anabereka

Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 27 Hadoramu, Uzali, Dikila, 28 Obali, Abimaeli, Seba, 29 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

30 Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.

31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.

32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.

Nsanja ya Babeli

11 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.

Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”

Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”

Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.

Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu

10 Nayi mibado yochokera kwa Semu.

Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.

Mibado Yochokera mwa Tera

27 Nayi mibado yochokera mwa Tera.

Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.

31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.

32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.