Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Chivumbulutso 4-8

Mapembedzedwe a Kumpando Waufumu Kumwamba

Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.” Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo. Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo. Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu. Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu. Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo.

Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti,

“Woyera, woyera, woyera
ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”

Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. 10 Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati:

11 “Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu,
    Ambuye ndi Mulungu wathu,
pakuti munalenga zinthu zonse,
    ndipo mwakufuna kwanu
    zinalengedwa monga zilili.”

Buku la Mwana Wankhosa

Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri. Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake. Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zamʼkati mwake. Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”

Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi. Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo. Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima. Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti,

“Inu ndinu woyenera kulandira bukuli
    ndi kumatula zomatira zake,
chifukwa munaphedwa,
    ndipo magazi anu munagulira Mulungu
    anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.
10 Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu,
    ndipo adzalamulira dziko lapansi.”

11 Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. 12 Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti,

“Mwana Wankhosa amene anaphedwayu
    ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu,
    ulemerero ndi mayamiko.”

13 Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,

“Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,
    kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu
mpaka muyaya!”

14 Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.

Kutsekulidwa kwa Zimatiro Zisanu ndi Chimodzi

Ndinaona pamene Mwana Wankhosa anatsekula chomatira choyamba cha zomatira zisanu ndi ziwiri zija. Ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chikunena liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo pake ndinaona kavalo woyera! Wokwerapo wake anali ndi uta ndipo anapatsidwa chipewa chaufumu, ndipo anatuluka kupita kukagonjetsa anthu ena.

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chija chikuti, “Bwera!” Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wakuda! Wokwerapo wake anali ndi masikelo awiri mʼmanja mwake. Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!”

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachinayi, ndinamva chamoyo chachinayi chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayangʼana patsogolo panga ndinaona kavalo wotuwa! Wokwerapo wake dzina lake linali Imfa ndipo Hade inali kumutsatira pambuyo pake. Anapatsidwa ulamuliro pa gawo limodzi la magawo anayi a dziko lapansi kuti aphe ndi lupanga, njala, mliri, ndi zirombo zakuthengo za mʼdziko lapansi.

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. 10 Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?” 11 Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.

12 Ndinayangʼanitsitsa pamene ankatsekula chomatira chachisanu ndi chimodzi. Ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Dzuwa linada ngati chiguduli chopanga ndi bweya wambuzi wakuda. Mwezi wonse unafiira ngati magazi, 13 ndipo nyenyezi zakuthambo zinagwa pa dziko lapansi ngati muja zimagwera nkhuyu zotsalira mu mtengo mphepo yamphamvu ikawomba. 14 Thambo linachoka ngati amayalulira mphasa ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa pa malo pake.

15 Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri. 16 Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa! 17 Pakuti tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika ndipo ndi ndani angathe kulimbapo?”

Anthu 144,000

Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse. Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti, “Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.” Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.

Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro.

Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000;

ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;

ochokera fuko la Aseri analipo 12,000;

ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000;

ochokera fuko la Manase analipo 12,000;

ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000;

ochokera fuko la Levi analipo 12,000;

ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;

ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000;

ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000;

ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.

Gulu Lalikulu la Anthu Ovala Zoyera

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo. 10 Ndipo ankafuwula mokweza kuti:

“Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu,
wokhala pa mpando waufumu
ndi kwa Mwana Wankhosa.”

11 “Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu. 12 Iwo anati,

“Ameni!
Matamando ndi ulemerero,
nzeru, mayamiko, ulemu,
ulamuliro ndi mphamvu
zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi,
Ameni!”

13 Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?”

14 Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.”

Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa. 15 Nʼchifukwa chake,

“iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu
    ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu;
ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu
    adzawaphimba ndi tenti yake.
16 ‘Iwowa sadzamvanso njala,
    sadzamvanso ludzu,
dzuwa kapena kutentha kulikonse
    sikudzawawotcha.’
17 Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu
    adzakhala mʼbusa wawo.
‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’
    ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

Kutsekulidwa kwa Chimatiro Chachisanu ndi Chiwiri

Atatsekula chomatira chachisanu ndi chiwiri, kumwamba kunakhala chete mphindi makumi atatu.

Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri aja amene amayimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi awiri.

Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu. Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo. Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi.

Malipenga

Angelo asanu ndi awiri anakonzekera kuyimba malipenga asanu ndi awiri.

Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso.

Mngelo wachiwiri anayimba lipenga lake, ndipo chinthu china chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto, chinaponyedwa mʼnyanja. Gawo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka magazi. Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa.

10 Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi. 11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo.

12 Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.

13 Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.