Beginning
Za Kuuka kwa Khristu
15 Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. 2 Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.
3 Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba, 4 kuti anayikidwa mʼmanda, kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu monga mwa Malemba; 5 ndipo kuti anaonekera kwa Petro, ndipo kenaka kwa Atumwi khumi ndi awiriwo. 6 Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo. 7 Kenaka anaonekeranso kwa Yakobo, kenaka kwa atumwi onse. 8 Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane.
9 Pakuti ine ndine wamngʼono kwa atumwi ndipo sindiyenera nʼkomwe kutchedwa mtumwi chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. 11 Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.
Kuuka kwa Oyera Mtima
12 Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa? 13 Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso. 14 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito. 15 Kuwonjezera pamenepa, ndiye kuti ndife mboni zabodza pa za Mulungu, pakuti tikuchita umboni kuti Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa. Ngati nʼzoona kuti akufa saukitsidwa, ndiye kuti Mulungu sanaukitsenso Khristu. 16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, ndiye kuti nayenso Khristu sanaukitsidwe. 17 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu. 18 Ndiye kuti nawonso amene agona tulo mwa Ambuye ndi otayika. 19 Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.
20 Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo. 21 Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu. 22 Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. 23 Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. 24 Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. 25 Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse. 26 Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa. 27 Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu. 28 Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29 Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo? 30 Ndipo kwa ife, tikuyikiranji moyo wathu pachiswe nthawi ndi nthawi? 31 Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 32 Ngati ndinalimbana ndi zirombo za kuthengo ku Efeso pa zifukwa za umunthu chabe, ndapindulanji? Ngati akufa sadzaukitsidwa,
“Tiyeni tidye ndi kumwa,
pakuti mawa tifa.”
33 Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.” 34 Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi.
Kuukitsidwa kwa Thupi
35 Koma wina akhoza kufunsa kuti, “Kodi akufa amaukitsidwa motani? Adzauka ndi thupi la mtundu wanji?” 36 Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa. 37 Mukadzala, simudzala thupi limene lidzamere, koma mbewu chabe, mwina ya tirigu kapena ya china chake. 38 Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake. 39 Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso. 40 Palinso matupi akumwamba ndipo palinso matupi a dziko lapansi; koma ulemerero wa matupi akumwamba ndi wina, ndi wa matupi a dziko lapansi ndi winanso. 41 Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana.
42 Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. 43 Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. 44 Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu.
Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. 45 Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. 46 Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. 47 Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. 48 Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. 49 Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.
50 Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda. 51 Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. 52 Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika. 53 Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. 54 Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.”
55 “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti?
Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”
56 Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo. 57 Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
58 Choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.
Ndalama Zothandizira Akhristu a ku Yerusalemu
16 Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite. 2 Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha. 3 Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu. 4 Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi.
Paulo Afotokoza za Maulendo ake ndi Zina
5 Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako. 6 Mwina ndidzakhala nanu kanthawi kochepa kapenanso nyengo yonse yozizira, kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite. 7 Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola. 8 Koma ndikhala ndili ku Efeso mpaka nthawi ya Pentekosite, 9 pakuti mwayi waukulu wapezeka woti nʼkugwira ntchito yaphindu, koma pali ambiri amene akutsutsana nane.
10 Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine. 11 Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.
12 Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.
13 Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu. 14 Chitani zonse mwachikondi.
15 Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale, 16 kuti muziwamvera anthu oterewa, ndiponso aliyense wogwira nawo ntchitoyi modzipereka. 17 Ndikondwera kuti Stefano, Fortunato ndi Akayiko afika, chifukwa akhala akundithandiza pakuti inu simuli nane. 18 Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.
Mawu Otsiriza
19 Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni. 20 Abale onse kuno akupereka moni wawo. Patsanani moni wachikondi chenicheni.
21 Ineyo Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa mawu awa akuti moni.
22 Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!
23 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu.
24 Chikondi changa chikhale ndi nonsenu mwa Khristu Yesu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.