Beginning
Paulo Apita ku Yerusalemu
21 Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara. 2 Kumeneko tinapeza sitima yapamadzi yopita ku Foinike. Choncho tinalowamo nʼkunyamuka. 3 Tinaona chilumba cha Kupro ndipo tinadutsa kummwera kwake nʼkupita ku Siriya. Tinakayima ku Turo chifukwa sitima yathuyo imayenera kusiya katundu kumeneko. 4 Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 5 Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera. 6 Titatsanzikana, tinalowa mʼsitima ija, iwowo anabwerera ku nyumba zawo.
7 Ife tinapitiriza ulendo wathu wochokera ku Turo mpaka tinafika ku Ptolemayi. Kumeneko tinalonjera abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja. 9 Iye anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene anali ndi mphatso ya uneneri.
10 Titakhala kumeneko masiku ambiri, kunabwera mneneri wina wochokera ku Yudeya dzina lake Agabu. 11 Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’ ”
12 Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu kumeneko tinamudandaulira Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”
15 Pambuyo pake, ife tinakonzeka ndi kunyamuka kumapita ku Yerusalemu. 16 Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.
Paulo Afika ku Yerusalemu
17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mwachimwemwe. 18 Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko. 19 Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.
20 Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose. 21 Iwo anawuzidwa kuti iwe umaphunzitsa Ayuda onse amene akukhala pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Mose, kuti asamachite mdulidwe kapena kutsatira miyambo. 22 Nanga pamenepa ife titani? Iwo adzamva ndithu kuti iwe wabwera, 23 tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu. 24 Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo. 25 Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”
26 Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.
Agwira Paulo
27 Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo, 28 akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.” 29 Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.
30 Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata. 31 Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka. 32 Nthawi yomweyo iye anatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali ndi kuthamangira kumene kunali anthuwo. Anthuwo ataona mkuluyo ndi asilikali ake analeka kumenya Paulo.
33 Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani. 34 Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali. 35 Paulo atafika pa makwerero olowera ku malo a asilikaliwo, ananyamulidwa ndi asilikali chifukwa cha ukali wa anthuwo. 36 Gulu la anthu limene linamutsatira linapitiriza kufuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi!”
Paulo Ayankhula
37 Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?”
Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki? 38 Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”
39 Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”
40 Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri.
22 Iye anati, “Inu abale anga ndi makolo anga, tamvani mawu akudziteteza kwanga.” 2 Atamva iye akuyankhula Chihebri, anakhala chete.
Kenaka Paulo anati, 3 “Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero. 4 Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende. 5 Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.
6 “Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira. 7 Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’ ”
8 Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?”
Iye anayankha kuti, “Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.” 9 Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.
10 Ine ndinafunsa kuti, “Kodi ndichite chiyani Ambuye?”
Ambuye anati, “Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.” 11 Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.
12 “Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu. 13 Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.
14 “Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake. 15 Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva. 16 Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’
17 “Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka. 18 Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ”
19 Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu. 20 Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”
21 Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”
Paulo Nzika ya Chiroma
22 Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”
23 Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba, 24 mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere. 25 Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”
26 Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”
27 Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?”
Paulo anayankha kuti, “Inde.”
28 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.”
Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”
29 Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.
Paulo ku Bwalo Lalikulu la Ayuda
30 Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.
23 Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.” 2 Chifukwa cha mawu amenewa, mkulu wa ansembe Ananiya analamulira amene anali pafupi ndi Paulo kuti amumenye pakamwa. 3 Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”
4 Anthu amene anayimirira pafupi ndi Paulo anati, “Bwanji ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?”
5 Paulo anayankha nati, “Abale, ine sindinazindikire kuti ndi mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa kuti, ‘Usayankhule zoyipa kwa mtsogoleri wa anthu ako.’ ”
6 Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.” 7 Iye atanena zimenezi, mkangano unabuka pakati pa Afarisi ndi Asaduki mpaka anthu kugawikana. 8 Asaduki amati kulibe kuuka kwa akufa, kulibenso ngakhale angelo kapena mizimu, koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.
9 Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.” 10 Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.
11 Usiku omwewo Ambuye anayimirira pambali pa Paulo nati, “Limba mtima! Monga wandichitira Ine umboni mu Yerusalemu, moteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.”
Ayuda Achita Chiwembu Paulo
12 Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. 13 Anthu amene anakonza chiwembuchi analipo makumi anayi. 14 Iwo anapita kwa akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda nakawawuza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitidya kalikonse mpaka titapha Paulo. 15 Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”
16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, anapita ku malo a asilikali aja namufotokozera Paulo.
17 Paulo anayitana mmodzi wa wolamulira asilikali 100 aja, namuwuza kuti, “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali. Iyeyu ali ndi mawu oti akamuwuze.” 18 Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”
19 Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”
20 Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye. 21 Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”
22 Mkulu wa asilikaliyo anawuza mnyamatayo kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Usawuze munthu aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”
Paulo Apita ku Kaisareya
23 Kenaka mkulu wa asilikaliyo anayitana awiri a asilikali olamulira asilikali 100 nawalamula kuti, “Uzani asilikali 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndi 200 onyamula mikondo kuti akonzeke kupita ku Kaisareya usiku omwe uno nthawi ya 9 koloko. 24 Mumukonzerenso Paulo akavalo woti akwerepo kuti akafike bwino kwa bwanamkubwa Felike.”
25 Iye analemba kalata iyi:
26 Ine Klaudiyo Lusiya,
Kwa wolemekezeka, bwanamkubwa Felike:
Ndikupereka moni.
27 Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma. 28 Ndinkafuna kudziwa mlandu umene anapalamula, choncho ndinapita naye ku Bwalo lawo Lalikulu. 29 Ine ndinapeza kuti amamuyimba mlandu wa nkhani ya malamulo awo, koma panalibe mlandu woyenera kumuphera kapena kumuyika mʼndende. 30 Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.
31 Pamenepo asilikali aja anatenga Paulo monga anawalamulira napita naye ku Antipatri usiku. 32 Mmawa mwake iwo anabwerera ku malo a asilikali nasiya okwera pa akavalo kuti apitirire ndi Paulo. 33 Asilikali okwera pa akavalowo atafika ku Kaisareya anapereka kalatayo kwa bwanamkubwa, namuperekanso Paulo. 34 Bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anamufunsa Paulo za dera limene amachokera. Atazindikira kuti amachokera ku Kilikiya, 35 iye anati, “Ndidzamva mlandu wako okuyimba mlandu akabwera kuno.” Ndipo analamulira kuti asilikali adzimulondera Paulo ku nyumba ya mfumu Herode.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.