Beginning
Petro Afotokozera Mpingo
11 Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu. 2 Tsono Petro atafika ku Yerusalemu, abale amene anali a mdulidwe anamutsutsa iye, 3 ndipo anati, “Iwe unalowa mʼnyumba ya anthu osachita mdulidwe ndi kudya nawo.”
4 Koma Petro anayamba kuwafotokozera zonse mwatsatanetsatane momwe zinachitikira kuti, 5 “Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine. 6 Ine ndinayangʼana mʼkati mwake ndipo ndinaona nyama za miyendo inayi za mʼdziko lapansi, zirombo, zokwawa, ndi mbalame zamlengalenga. 7 Kenaka ine ndinamva mawu akuti, ‘Petro, Imirira. Ipha, nudye.’
8 “Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’
9 “Mawu ochokera kumwamba ananenanso kachiwiri kuti, ‘Chimene Mulungu wachiyeretsa usanene kuti ndi chodetsedwa.’ 10 Zimenezi zinachitika katatu ndipo kenaka zonse zinatengedwa kupita kumwamba.
11 “Nthawi yomweyo anthu atatu amene anatumidwa kuchokera ku Kaisareya anayima pa nyumba yomwe ndimakhalayo. 12 Mzimu anandiwuza kuti ndisakayike, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi awa anapitanso nane ndipo tinalowa mʼnyumba ya munthuyo. 13 Iye anatiwuza mmene anaonera mngelo atayimirira mʼnyumba mwake ndi kumuwuza kuti, ‘Tumiza anthu ku Yopa kuti akayitane Simoni wotchedwa Petro. 14 Iye adzakuwuza uthenga umene udzapulumutsa iwe ndi a pa banja ako.’
15 “Nditangoyamba kuyankhula, Mzimu Woyera anafika pa iwo monga momwe anafikira pa ife poyamba paja. 16 Kenaka ndinakumbukira zimene Ambuye ananena kuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’ 17 Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”
18 Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”
Mpingo wa ku Antiokeya
19 Tsopano amene anabalalika chifukwa cha mazunzo amene anayamba ataphedwa Stefano, anapita mpaka ku Foinike, ku Kupro ndi ku Antiokeya, ndipo ankalalikira kwa Ayuda okha. 20 Komabe, ena pakati pawo ochokera ku Kupro ndi ku Kurene anapita ku Antiokeya ndipo iwo anayamba kuyankhulanso kwa Agriki, nawawuza za Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. 21 Mphamvu ya Ambuye inali nawo ndipo anthu ambiri anakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.
22 Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya. 23 Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye. 24 Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.
25 Kenaka Barnaba anapita ku Tarisisi kukafuna Saulo, 26 ndipo pamene anamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Barnaba ndi Saulo anasonkhana ndi mpingo kwa chaka chimodzi naphunzitsa anthu ambirimbiri. Okhulupirirawo anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
27 Masiku amenewo ku Antiokeya kunafika aneneri ena ochokera ku Yerusalemu. 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo). 29 Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. 30 Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo.
Petro Apulumuka Mʼndende
12 Inali nthawi yomweyi imene mfumu Herode anamanga ena a mu mpingo ndi cholinga chakuti awazunze. 2 Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. 3 Ataona kuti zimenezi zinakondweretsa Ayuda, anawonjeza ndi kugwiranso Petro. Izi zinachitika pa nthawi ya Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. 4 Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.
5 Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.
6 Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. 7 Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.
8 Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” 9 Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. 10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
11 Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”
12 Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. 13 Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. 14 Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!”
15 Anthuwo anati kwa iye, “Wopenga iwe!” Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, “Ameneyo ndi mngelo wake.”
16 Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri. 17 Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.
18 Pamene kunacha kunali phokoso lalikulu pakati pa asilikali, iwo anafunsa kuti, “Kodi chamuchitikira Petro ndi chiyani?” 19 Herode atamufunafuna ndipo wosamupeza, anawafunsa asilikali ndipo analamulira kuti asilikaliwo aphedwe.
Imfa ya Herode
Kenaka Herode anachoka ku Yudeya ndi kupita ku Kaisareya ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi 20 Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo.
21 Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo. 22 Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.
24 Koma Mawu a Mulungu anapitirirabe kufalikirafalikira.
25 Barnaba ndi Saulo atamaliza ntchito yawo anachoka ku Yerusalemu, atatenga Yohane wotchedwanso Marko.
Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo
13 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira.” 3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.
Ku Kupro
4 Barnaba ndi Saulo motumidwa ndi Mzimu Woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 5 Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.
6 Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. 7 Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. 8 Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. 9 Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, 10 “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? 11 Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.”
Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. 12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.
Antiokeya wa ku Pisidiya
13 Kuchokera ku Pafo, Paulo ndi anzake anayenda pa sitima ya pamadzi kupita ku Perga wa ku Pamfiliya, kumeneko Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu. 14 Kuchokera ku Perga anapita ku Pisidiya wa ku Antiokeya. Pa tsiku la Sabata analowa mʼsunagoge, nakhala pansi. 15 Atawerenga mawu a mʼMalamulo ndi Aneneri, akulu a sunagoge anawatumizira mawu ndi kuti, “Abale ngati muli ndi mawu olimbikitsa nawo anthuwa, nenani.”
16 Atayimirira, Paulo anakweza dzanja lake ndi kuti, “Inu Aisraeli ndiponso inu a mitundu ina amene mumapembedza Mulungu, tandimverani! 17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Ndipo Iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu kwa zaka makumi anayi. 19 Mulungu anawagonjetsera mitundu isanu ndi iwiri ya ku Kanaani ndipo anapereka dzikolo kwa Israeli kuti likhale lawo. 20 Izi zonse zinatenga zaka 450.
“Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli. 21 Kenaka anthu anapempha kuti awapatse mfumu, ndipo anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, wa fuko la Benjamini amene analamulira zaka makumi anayi. 22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’
23 “Kuchokera mwa zidzukulu za munthu ameneyu, Mulungu anawutsa Yesu kukhala Mpulumutsi wa Aisraeli, monga analonjezera. 24 Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo. 25 Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’
26 “Abale, ana a Abrahamu, ndiponso inu a mitundu ina amene mumaopa Mulungu, Iye watumiza uthenga wachipulumutsowo kwa ife. 27 Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse. 28 Ngakhale sanapeze chifukwa choti afe, anapempha Pilato kuti amuphe. 29 Atachita zonse zimene zinalembedwa za Iye, iwo anamuchotsa pa mtengo ndipo anamuyika mʼmanda. 30 Koma Mulungu anamuukitsa, 31 ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa amene anayenda naye kuchokera ku Galileya mpaka ku Yerusalemu. Iwowa tsopano ndi mboni zake kwa anthu a Israeli.
32 “Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu. 33 Iye wakwaniritsa zimenezi kwa ife ana awo, poukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Monga zinalembedwa mu Salimo lachiwiri kuti,
“Iwe ndiwe mwana wanga;
lero ine ndakhala Atate ako.”
34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa:
“ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’
35 Nʼchifukwa chakenso zinalembedwa mu Salimo lina kuti,
“ ‘Simudzalekerera woyera wanu kuti awole.’
36 “Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu mʼbado wake, anamwalira, iye anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi.
38 “Nʼchifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. 39 Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. 40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:
41 “ ‘Onani, inu anthu onyoza,
dabwani ndipo wonongekani,
chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu,
inu simudzazikhulupirira
ngakhale wina atakufotokozerani!’ ”
42 Pamene Paulo ndi Barnaba amatuluka mʼSunagoge, anthu anawapempha kuti adzapitirize kuyankhula zinthu zimenezi Sabata linalo. 43 Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.
44 Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye. 45 Pamene Ayuda anaona gulu la anthu, anachita nsanje ndipo anayankhula zamwano kutsutsana ndi zimene Paulo amanena.
46 Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife:
“ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina,
kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”
48 Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira.
49 Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse. 50 Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. 51 Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya. 52 Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndiponso ndi Mzimu Woyera.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.